“Ndani Kweni-kweni Amene Ali Kapolo Wokhulupilika Ndi wanzelu?”
“Ndani kweni-kweni amene ali kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anila anchito ake apakhomo?”—MAT. 24:45.
KODI MUNGAYANKHE?
Kodi kapolo wokhulupilika ndi wanzelu ndani?
Kodi anchito apakhomo ndani? Nanga ndi liti pamene Yesu anaika kapolo wokhulupilika kuti aziyang’anila anchito ake apakhomo?
Kodi ndi liti pamene Kristu adzaika kapolo wokhulupilika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse? Ndipo zinthu zimenezo zidzaphatikizapo ciani?
1, 2. Kodi Yesu masiku ano amagwilitsila nchito njila iti kuti atidyetse mwa kuuzimu? Ndipo n’cifukwa ciani tifunikila kuidziŵa bwino njila imeneyo?
“ABALE, sindingakwanitse kuchula kuti ndi nkhani zingati zimene ndalandila zimene ndinali kufunitsitsa, ndiponso panthawi imene ndinali kuzifuna kwambili.” Izi ndi zimene mlongo wina analemba m’kalata yopita kwa abale amene amagwila nchito ku likulu lathu pofuna kuwayamikila. Kodi inunso munamvapo conco? Ambili a ife tamvapo conco. Kodi zimenezi ziyenela kutidabwitsa? Iyai.
2 Cakudya ca kuuzimu ca panthawi yake cimene timalandila ndi umboni wakuti Yesu, Mutu wa mpingo, wasunga lonjezo lake lakuti adzatidyetsa. Kodi amatidyetsa kupitila mwa ndani? Popeleka cizindikilo ca kukhalapo kwake, Yesu ananena kuti adzagwilitsila nchito “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kupatsa anchito ake apakhomo “cakudya pa nthawi yoyenela.”a (Ŵelengani Mateyu 24:45-47.) Kapolo wokhulupilika ameneyo ndiye njila imene Yesu amagwilitsila nchito kudyetsa otsatila ake oona m’nthawi yamapeto ino. Conco, tifunika kumudziŵa bwino kapolo wokhulupilika ameneyo, cifukwa moyo wathu wa kuuzimu ndi ubwenzi wathu ndi Mulungu zimadalila pa kapolo ameneyo.—Mat. 4:4; Yoh. 17:3.
3. Kodi mabuku athu anati ciani ponena za fanizo la kapolo wokhulupilika?
3 Motelo, kodi fanizo la Yesu la kapolo wokhulupilika limatanthauza ciani? M’mbuyomu mabuku athu anali kufotokoza kuti, pa Pentekosite mu 33 C.E., Yesu anaika kapolo wokhulupilika kuti aziyang’anila anchito ake apakhomo. Anafotokozanso kuti kapolo ameneyu amaimila gulu lonse la Akristu odzozedwa amene ali ndi moyo padziko lapansi panthawi ina iliyonse kucokela mu 33 C.E. Zofalitsa zathu zinanena kuti anchito apakhomo amaimila odzozedwa amodzi-modziwo aliyense payekha. Zinanenanso kuti mu 1919, Yesu anaika kapolo wokhulupilika kuti “aziyang’anila zinthu zake zonse,” zimene ndi zinthu za Ufumu padziko lapansi. Komabe, pambuyo popemphela ndi kuphunzila mosamalitsa mau a Yesu onena za kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, taona kuti kamvedwe kathu pankhani imeneyi kayenela kusintha. (Miy. 4:18) Tiyeni tikambitsilane fanizo limeneli ndi kuona mmene limatikhudzila, kaya ciyembekezo cathu ndi copita kumwamba kapena cokhala padziko lapansi.
KODI FANIZO LIMENELI LIDZAKWANILITSIDWA LITI?
4-6. N’cifukwa ciani tinganene kuti fanizo la Yesu la kapolo wokhulupilika linayamba kukwanilitsidwa kokha pambuyo pa 1914?
4 Nkhani ya fanizo la kapolo wokhulupilika ndi wanzelu imaonetsa kuti fanizo limeneli linayamba kukwanilitsidwa m’nthawi ino ya mapeto, osati pa Pentekosite mu 33 C.E. Tiyeni tione mmene Malemba amatithandizila kumvetsetsa zimenezi.
5 Fanizo la kapolo wokhulupilika ndi mbali ya ulosi wa Yesu wonena za “cizindikilo ca kukhalapo [kwake] ndi ca mapeto a nthawi ino.” (Mat. 24:3) Mbali yoyamba ya ulosi umenewu wolembedwa pa Mateyu 24:4-22, ili ndi kukwanilitsidwa kwa mbali ziŵili. Kukwanilitsidwa koyamba kunacitika mu 33 C.E. mpaka mu 70 C.E., ndipo kukwanilitsika kwaciŵili ndiponso kwakukulu kukucitika masiku ano. Kodi zimenezi zitanthauza kuti mau a Yesu onena za kapolo wokhulupilika naonso adzakwanilitsidwa m’mbali ziŵili? Iyai.
6 Kuyambila ndi Mau olembedwa pa Mateyu 24:29, Yesu maka-maka anafotokoza zinthu zimene zidzacitika m’masiku athu. (Ŵelengani Mateyu 24:30, 42, 44.) Pofotokoza zimene zidzacitika pa nthawi ya cisautso cacikulu, iye anakamba kuti anthu “adzaona Mwana wa munthu akubwela pamitambo ya kumwamba.” Ndiyeno, polimbikitsa anthu amene adzakhala m’masiku otsiliza ponena za kufunika kokhala maso, Yesu anati: “Simukudziŵa tsiku limene Ambuye wanu adzabwele.” Ndipo, “Pa ola limene simukuliganizila, Mwana wa munthu adzabwela.”b Pamene Yesu anamaliza kufotokoza zinthu zimene zidzacitika m’masiku otsiliza, iye anafotokozanso fanizo la kapolo wokhulupilika. Conco, tinganene kuti mau ake onena za kapolo wokhulupilika anayamba kukwanilitsidwa kokha pambuyo pakuti masiku otsiliza ayamba mu 1914. Mfundo imeneyi ndi yomveka. N’cifukwa ciani tikutelo?
7. Kodi ndi funso lofunika liti limene linabuka pamene nyengo yokolola inayamba? Nanga n’cifukwa ciani panabuka funso limenelo?
7 Ganizilani funso lakuti: “Ndani kweni-kweni amene ali kapolo wokhulupilika ndi wanzelu?” M’nthawi ya atumwi, panalibe cifukwa cofunsila funso limeneli. Monga mmene tinaonela m’nkhani yapita, atumwi anali kucita zozizwitsa ndi kupatsa ena mphatso yocita zozizwitsa pofuna kuonetsa kuti anali kuthandizidwa ndi Mulungu. (Mac. 5:12) Conco, panalibe cifukwa cakuti munthu afunse kuti ndani kweni-kweni amene Kristu anaika kuti azitsogolela. Koma mu 1914, zinthu zinasintha kwambili. Nthawi yokolola inayamba m’caka cimeneco. Nthawi inafika yakuti alekanitse namsongole ndi tiligu. (Mat. 13:36-43) Pamene nthawi yokolola inayamba, panabuka funso lofunika kwambili. Funso limenelo linali lakuti, kodi Akristu odzozedwa amene anali monga tiligu akanadziŵika bwanji popeza panali Akristu onama ambili amene anali kudzicha kuti ndi otsatila oona a Yesu? Fanizo la kapolo wokhulupilika linayankha funso limenelo. Otsatila a Kristu odzozedwa ndi amene anali kudyetsedwa bwino mwa kuuzimu.
KODI KAPOLO WOKHULUPILIKA NDI WANZELU NDANI?
8. N’cifukwa ciani n’koyenela kuti anthu amene amapanga kapolo wokhulupilika akhale Akristu odzozedwa?
8 Anthu amene amapanga kapolo wokhulupilika ayenela kukhala Akristu odzozedwa padziko lapansi. Anthu amenewa amachedwa kuti “ansembe acifumu,” ndipo alamulidwa kuti ‘alengeze makhalidwe abwino kwambili a amene anawaitana kucoka mu mdima kuloŵa m’kuwala kwake kodabwitsa.’ (1 Pet. 2:9) Ndipo n’zomveka kuti “ansembe acifumu” amenewa azigwila nchito yophunzitsa okhulupilila anzao coonadi.—Mal. 2:7; Chiv. 12:17.
9. Kodi Akristu onse odzozedwa padziko lapansi ndi kapolo wokhulupilika? Fotokozani.
9 Kodi Akristu onse odzozedwa padziko lapansi ndi kapolo wokhulupilika? Iyai. Si odzozedwa onse amene ali ndi nchito yogaŵila cakudya ca kuuzimu kwa okhulupilila anzao padziko lonse lapansi. Pakati pa anthu amene ali monga tiligu, pali abale odzozedwa amene amatumikila monga atumiki othandiza kapena akulu m’mipingo yao. Iwo amalalikila kunyumba ndi nyumba ndi kuphunzitsa m’mipingo yao, ndipo mokhulupilika amagwilizana ndi citsogozo cocokela ku malikulu. Koma io alibe mbali mu nchito yogaŵila cakudya ca kuuzimu ku gulu lonse la abale padziko lapansi. Ndiponso pakati pa odzozedwa amenewa, pali alongo odzicepetsa amene samaganizapo zokhala aphunzitsi mumpingo.—1 Akor. 11:3; 14:34.
10. Kodi kapolo wokhulupilika ndi wanzelu ndani?
10 Conco, kodi kapolo wokhulupilika ndi wanzelu ndani? Monga mmene Yesu anadyetsela anthu ambili mwa kugwilitsila nchito anthu ocepa, kapolo ameneyu ndi kagulu kocepa ka abale odzozedwa amene mwacindunji amagwila nchito yokonza cakudya ca kuuzimu ndi kucigaŵila m’nthawi ya kukhalapo kwa Kristu. M’masiku otsiliza ano, abale odzozedwa amene amapanga kapolo wokhulupilika akhala akugwilila nchito pamodzi ku malikulu. Conco, kapolo wokhulupilika ndi wanzelu ndi Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova. Komabe, m’fanizo lake, Yesu anaonetsa kuti padzakhala “kapolo” mmodzi. Conco, Bungwe Lolamulila limapanga zosankha zake monga gulu.
KODI ANCHITO APAKHOMO NDANI?
11, 12. (a) Kodi kapolo wokhulupilika ndi wanzelu anapatsidwa maudindo aŵili ati? (b) Kodi ndi liti pamene Yesu anaika kapolo wokhulupilika kuti aziyang’anila anchito ake apakhomo? Ndipo kodi iye anasankha ndani?
11 Tiyenelanso kukumbukila kuti m’fanizo la Yesu, kapolo wokhulupilika ndi wanzelu anaikidwa kuyang’anila zinthu ziŵili zosiyana. Coyamba ndi kuyang’anila anchito apakhomo, ndipo caciŵili ndi kuyang’anila zinthu zonse za ambuye. Popeza kuti fanizo limeneli likukwanilitsika kokha m’nthawi ino yomaliza, uyang’anilo wonse uŵili umenewu unayenela kupatsidwa kwa kapolo ameneyu pambuyo pakuti Yesu wayamba kulamulila monga mfumu mu 1914.
12 Kodi ndi liti pamene Yesu anaika kapolo wokhulupilika kuti aziyang’anila anchito ake apakhomo? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikumbukile mmene zinthu zinalili mu 1914, pamene nthawi yokolola inayamba. Monga mmene tinaphunzilila kale, panthawi imeneyo magulu ambili a zipembedzo anali kunena kuti ndi Akristu. Kodi Yesu anayenela kusankha kapolo wokhulupilika kuti akhale woyang’anila kucokela m’gulu liti? Funso limenelo linayankhidwa pamene Yesu ndi Atate ake anabwela kudzayendela kacisi kapena kuti makonzedwe a kuuzimu a kulambila, kuyambila mu 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919.c (Mal. 3:1) Iwo anasangalala kupeza anthu ocepa amene anali Ophunzila Baibo okhulupilika omwe anaonetsa kuti anali kukonda Yehova ndi Mau ake. N’zoona kuti io anafunika kuyeletsedwa. Koma modzicepetsa anapanga masinthidwe oyenelela m’kanthawi kocepa kamene io anali kuyesedwa ndi kuyengedwa. (Mal. 3:2-4) Ophunzila Baibo okhulupilika amenewo analidi Akristu oona okhala ngati tiligu. Mu 1919, pamene zinthu za kuuzimu zinayambanso kuyenda bwino, Yesu anasankha abale odzozedwa oyenelela pakati pao kuti akhale kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, ndipo anawaika kuti aziyang’anila anchito ake apakhomo.
13. Kodi anchito apakhomo amaphatikizapo ndani? Nanga n’cifukwa ciani?
13 Nanga anchito apakhomo amenewa ndani? Kunena mwacidule, ndi anthu onse amene amapatsidwa cakudya ca kuuzimu. Kuciyambi kwa masiku otsiliza, anchito apakhomo onse anali odzozedwa. Pambuyo pake, anchito apakhomo amenewa anaphatikizapo khamu lalikulu la nkhosa zina. Masiku ano a nkhosa zina ndi amene amapanga mbali yaikulu ya “gulu limodzi” la nkhosa lotsogoleledwa ndi Kristu. (Yoh. 10:16) Magulu onse aŵili amapindula ndi cakudya ca kuuzimu cofanana ndi ca panthawi yake cimene amalandila kudzela mwa kapolo wokhulupilika. Nanga bwanji ponena za mamembala a Bungwe Lolamulila amene ndi gulu la kapolo wokhulupilika ndi wanzelu masiku ano? Abale amenewa naonso amafunikila kudya cakudya ca kuuzimu. Conco, io modzicepetsa amazindikila kuti aliyense wa io payekha ndi wanchito wa pakhomo monga mmene aliyense wa otsatila oona a Yesu alili.
14. (a) Kodi kapolo wokhulupilika anapatsidwa udindo wotani? Nanga udindo umenewo umaphatikizapo ciani? (b) Kodi ndi cenjezo lotani limene Yesu anapatsa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu? (Onani bokosi lakuti, “Ngati Kapolo Woipayo . . .”)
14 Yesu anapatsa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu udindo waukulu kwambili. M’nthawi za m’Baibo, kapolo wokhulupilika, kapena kuti mtumiki, anali munthu amene anali kuyang’anila nyumba ya ambuye wake. (Luka 12:42) Conco, kapolo wokhulupilika ndi wanzelu anapatsidwa udindo woyang’anila Akristu anzao. Udindo umenewu umaphatikizapo kuyang’anila katundu, nchito yolalikila, misonkhano yadela ndi yacigawo, nchito yosindikiza mabuku ogwilitsila nchito mu utumiki wakumunda, pa phunzilo laumwini ndi pa misonkhano ya mpingo. Anchito apakhomo amadalila zogaŵila zonse za kuuzimu zimene gulu la kapolo limapeleka.
KODI NDI LITI PAMENE ADZAIKIDWA KUYANG’ANILA ZINTHU ZONSE ZA AMBUYE?
15, 16. Kodi ndi liti pamene Yesu adzaika kapolo wokhulupilika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse?
15 Kodi ndi liti pamene Yesu adzapatsa kapolo wokhulupilika nchito yaciŵili, imene ndi kuyang’anila “zinthu zake zonse”? Yesu anati: “Kapolo ameneyu adzakhala wodala ngati mbuye wake pobwela adzam’peza akucita zimenezo. Ndithu ndikukuuzani, Adzamuika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse.” (Mat. 24:46, 47) Onani kuti Yesu adzapatsa kapoloyo nchito yaciŵili pambuyo pakuti wabwela ndi kupeza kuti kapolo ameneyo “akucita zimenezo,” zimene ndi kugaŵila cakudya ca kuuzimu mokhulupilika. Conco, panayenela kudutsa nthawi kuti apatsidwe nchito yaciŵili kucokela pamene anapatsidwa nchito yoyamba. Kuti timvetsetse kuti ndi motani, ndipo ndi liti pamene Yesu adzaika kapolo kuyang’anila zinthu zake zonse, tiyenela kudziŵa zinthu ziŵili. Coyamba, nthawi imene iye adzabwela ndipo caciŵili, cimene zinthu zake zimaphatikizapo.
16 Kodi Yesu adzabwela liti? Yankho lake limapezeka pa zimene iye ananena. Kumbukilani kuti pamene mavesi apamwamba pa lemba la Mateyu 24:46 akamba kuti Yesu “adzabwela,” liu limeneli limanena za nthawi pamene iye adzabwela kudzapeleka ciweluzo pamapeto a dongosolo lino la zinthu.d (Mat. 24:30, 42, 44) Conco, ‘kufika’ kapena ‘kubwela’ kwa Yesu kochulidwa m’fanizo la kapolo wokhulupilika, kudzacitika pa nthawi ya cisautso cacikulu.
17. Kodi zinthu za Yesu zimaphatikizapo ciani?
17 Kodi ‘zinthu zonse’ za Yesu zimaphatikizapo ciani? Yesu sanali kunena zinthu zake za padziko lapansi cabe pamene ananena kuti “zonse.” Iye ali ndi ulamulilo waukulu kumwamba. Yesu anati: “Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mat. 28:18; Aef. 1:20-23) Zinthu zake panthawi ino zimaphatikizapo Ufumu wa Mesiya, umene wakhala ufumu wake kuyambila mu 1914. Ndipo mtsogolo iye adzalamulila pamodzi ndi otsatila ake odzozedwa mu Ufumu umenewu.—Chiv. 11:15.
18. N’cifukwa ciani Yesu adzasangalala kupatsa kapolo wokhulupilika nchito yoyang’anila zinthu zake zonse?
18 Malinga ndi zimene takambilana, kodi taphunzilapo ciani? Pamene Yesu adzabwela kudzaweluza pa nthawi ya cisautso cacikulu, iye adzapeza kuti kapolo wokhulupilika wakhala akupeleka cakudya ca kuuzimu ca panthawi yake mokhulupilika kwa anchito apakhomo. Ndiyeno Yesu adzasangalala kupatsa kapolo ameneyu nchito yaciŵili imene ndi kuyang’anila zinthu zake zonse. Awo amene amapanga gulu la kapolo wokhulupilika adzapatsidwa nchito imeneyi, akadzalandila mphoto yao yakumwamba, yokhala olamulila anzake a Kristu.
19. Kodi kapolo wokhulupilika adzalandila mphatso yaikulu kumwamba kuposa odzozedwa ena? Fotokozani.
19 Kodi kapolo wokhulupilika adzalandila mphatso yaikulu kumwamba kuposa odzozedwa ena? Iyai. Anthu ocepa angalonjezedwe mphoto, koma pambuyo pake ingagaŵidwenso kwa ena. Mwacitsanzo, ganizilani zimene Yesu anauza atumwi ake okhulupilika 11 usiku wakuti mawa adzaphedwa. (Ŵelengani Luka 22:28-30.) Iye analonjeza kagulu kocepa ka amuna kameneko kuti kadzalandila mphoto yabwino cifukwa cokhala okhulupilika, ndipo adzalamulila naye mu Ufumu wake. Koma patapita zaka, iye anaonetsa kuti a 144,000 onse adzakhala pamipando yacifumu ndi kulamulila mu Ufumu wake. (Chiv. 1:1; 3:21) Mofananamo, pa lemba la Mateyu 24:47, Yesu analonjeza kuti abale odzozedwa ocepa amene amapanga kapolo wokhulupilika, adzaikidwa kuti aziyang’anila zinthu zake zonse. Koma a 144,000 onse adzalamulila naye mu ulamulilo wake waukulu kumwamba.—Chiv. 20:4, 6.
20. N’cifukwa ciani Yesu anaika kapolo wokhulupilika? Ndipo inu mwatsimikiza mtima kucita ciani?
20 Mwa kugwilitsila nchito kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, Yesu amatsatila njila imene anagwilitsila nchito m’nthawi ya atumwi. Njila imeneyo ndi kudyetsa anthu ambili mwa kugwilitsila nchito anthu ocepa. Yesu anaika kapolo wokhulupilika ameneyu kuti otsatila ake oona, kaya ndi odzozedwa kapena a nkhosa zina, nthawi zonse azilandila cakudya ca kuuzimu ca panthawi yake m’masiku otsiliza ano. Tiyeni tipitilizebe kuonetsa kuti timayamikila makonzedwe amenewa mwa kucilikiza mokhulupilika abale odzozedwa amene amapanga kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.—Aheb. 13:7, 17.
MAU AKUMAPETO: (Mau awa aŵelengedwe monga mau a munsi poŵelenga ndime zake.)
[Mau apansi]
a Ndime 2: Nthawi ina zimenezi zisanacitike, Yesu ananena fanizo lofanana ndi limeneli. M’fanizo limenelo, iye anacha “kapolo” kuti “mtumiki,” ndi “anchito apakhomo” kuti “gulu la atumiki ake.”—Luka 12:42-44.
b Ndime 6: ‘Kubwela’ kwa Kristu (Mu Cigiriki, erʹkho·mai) ndi kosiyana ndi “kukhalapo” kwake (pa·rou·siʹa). Kukhalapo kwake kosaoneka kunayamba iye asanabwele kudzaweluza.
c Ndime 12: Onani nkhani yakuti “Dziŵani Kuti Ine Ndili Pamodzi ndi Inu Masiku Onse,” m’magazini ino patsamba 11-12 ndime 7 mpaka 10.
d Ndime 16: Onani nkhani yakuti “Tiuzeni, Kodi Zinthu Zimenezi Zidzacitika Liti?” m’magazini ino, patsamba 7-8, ndime 14 mpaka 18.
[Bokosi papeji 28]
Kodi Mwazimvetsetsa Mfundo Zimenezi?
“Kapolo wokhulupilika ndi wanzelu”: Kagulu kocepa ka abale odzozedwa amene mwacindunji amakonza cakudya ca kuuzimu ndi kucigaŵila m’nthawi ya kukhalapo kwa Kristu. Masiku ano, abale odzozedwa amenewa ndi Bungwe Lolamulila
“Anchito ake apakhomo”: Anthu onse amene amapatsidwa cakudya ca kuuzimu, kaya ndi odzozedwa kapena a nkhosa zina
“Anamuika kuti aziyang’anila anchito ake apakhomo”: Mu 1919, Yesu anasankha abale odzozedwa oyenelela kuti akhale kapolo wake wokhulupilika ndi wanzelu
“Adzamuika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse”: Anthu amene amapanga gulu la kapolo adzapatsidwa nchito imeneyi akalandila mphoto yao kumwamba. Iwo pamodzi ndi a 144,000 ena onse, adzalamulila ndi Kristu mu ulamulilo wake waukulu kumwamba
[Cithunzi papeji 27, 28]
Kaya ciyembekezo cathu ndi ca kumwamba kapena ca padziko lapansi, tonse ndife anchito apakhomo ndipo timafunikila cakudya ca kuuzimu ca panthawi yake cofanana
[Bokosi papeji 30]
“Ngati Kapolo Woipayo . . .”
Yesu wapatsa udindo waukulu kwambili kwa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu. Udindo umenewo ndi kuyang’anila anchito ake apakhomo ndi kupeleka cakudya ca kuuzimu panthawi yake. Yesu anadziŵa kuti amene ali ndi udindo waukulu, adzaimbidwa mlandu waukulu ngati alephela kugwila bwino nchito yao. (Luka 12:48) Conco, iye anamaliza fanizo lake la kapolo wokhulupilika ndi wanzelu ndi cenjezo lamphamvu.
Yesu anacenjeza za kapolo woipa amene anganene mumtima mwake kuti ambuye akucedwa, ndi kuyamba kumenya akapolo anzake. Yesu anakamba kuti, pamene ambuye adzabwela adzapatsa kapolo woipayo “cilango coopsa.”—Ŵelengani Mateyu 24:48-51.
Kodi Yesu anali kunena kuti m’masiku otsiliza kudzakhala gulu la kapolo woipa? Iyai. N’zoonekelatu kuti anthu ena aonetsa mzimu wofanana ndi wa kapolo woipa amene Yesu anafotokoza. Anthu amenewa tingawache kuti ampatuko, kaya anali odzozedwa kapena a “khamu lalikulu.”(Chiv. 7:9) Koma io sapanga kagulu ka kapolo woipa. Yesu sananene kuti adzaika kapolo woipa. Mau ake amenewa ndi cenjezo kwa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.
Onani kuti Yesu anayamba cenjezo limeneli ndi liu lakuti “ngati.” Katswili wina ananena kuti, m’Malemba acigiriki, nkhani imeneyi “ingatanthauze zocitika zongoyelekezela.” M’mau ena Yesu anali kunena kuti: ‘Ngati kapolo wokhulupilika ndi wanzelu angayambe kuzunza akapolo ena mwa njila imeneyi, ambuye akadzabwela adzam’patsa cilango coopsa.’ (Onaninso Luka 12:45.) Komabe, gulu lonse la kapolo wokhulupilika ndi wanzelu lakhalabe maso, ndipo lapitiliza kupeleka cakudya ca kuuzimu conona.
Abale odzozedwa amene amatumikila monga kapolo wokhulupilika amadziŵa kuti adzayankha mlandu kwa Ambuye wao cifukwa ca mmene amasamalilila anchito ake apakhomo. Colinga cacikulu ca abale odzozedwa amenewa ndi kukwanilitsa udindo wao mokhulupilika kuti Ambuye wao akadzabwela akawauze kuti ‘mwacita bwino kwambili.’
[Cithunzi papeji 31]
A 144,000 onse adzalamulila ndi Yesu mu ulamulilo wake waukulu kumwamba
(Onani ndime 19)