-
Sungani Mgwilizano wa MpingoKondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
3. Kodi muyenela kucita ciyani mukasemphana maganizo na Mkhristu mnzanu?
Ndife ogwilizana inde, koma sitili angwilo. Nthawi zina tingakhumudwitsane kapena kukwiyitsana wina na mnzake. Conco Mawu a Mulungu amatiuza kuti “pitilizani . . . kukhululukilana ndi mtima wonse.” Ndipo amawonjezela kuti: “Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.” (Ŵelengani Akolose 3:13) Ngakhale kuti Yehova takhala tikumukwiyitsa maulendo osaŵelengeka, iye amatikhululukilabe. Conco, iye amatiyembekezela kucita cimodzimodzi kwa abale athu. Mukazindikila kuti mwakwiyitsa munthu wina, khalani woyamba kucitapo kanthu kuti muyanjanenso.—Ŵelengani Mateyu 5:23, 24.b
-
-
Sungani Mgwilizano wa MpingoKondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
Nthawi zina timakhumudwitsa anthu ena. Zimenezi zikacitika, kodi tiyenela kucita bwanji? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila
Kodi mlongo wa mu vidiyo iyi anacita ciyani kuti asungitse mtendele?
-