Muzilemekeza “Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi”
“Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.”—MALIKO 10:9.
1, 2. Kodi Aheberi 13:4 imatilimbikitsa kucita ciani?
KODI mumakonda kulemekeza Yehova? N’zosacita kufunsa! Iye ni woyeneladi kumulemekeza, ndipo analonjeza kuti tikamamulemekeza, nayenso adzatilemekeza. (1 Sam. 2:30; Miy. 3:9; Chiv. 4:11) Yehova amafunanso kuti tizilemekeza anthu ena. Mwacitsanzo, anatilamula kuti tizilemekeza akulu-akulu a boma. (Aroma 12:10; 13:7) Koma palinso cinthu cina cimene tiyenela kucilemekeza kwambili. Cinthu cimeneco ni cikwati.
2 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatilana pakhale posaipitsidwa.” (Aheb. 13:4) Pamenepa, Paulo sanali kungofotokoza mmene cikwati ciyenela kukhalila. Koma anali kupeleka malangizo. Anali kulangiza Akhristu kuti ayenela kuona cikwati kukhala colemekezeka, komanso camtengo wapatali. Kodi umu ni mmene imwe mumaonela cikwati, maka-maka canu ngati muli pa banja?
3. Ni malangizo ofunika ati amene Yesu anapeleka okhudza cikwati? (Onani pikica pamwambapa.)
3 Ngati tilemekeza cikwati, ndiye kuti tikutengela citsanzo cabwino kwambili ca Yesu. Iye anali kulemekeza cikwati. Pamene Afarisi anafunsa Yesu za kusudzulana, iye anawakumbutsa mawu amene Mulungu anakamba pa cikwati coyamba, akuti: “Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, ndipo aŵiliwo adzakhala thupi limodzi.” Kenako, Yesu anakamba kuti: “Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.”—Ŵelengani Maliko 10:2-12; Gen. 2:24.
4. Kodi Yehova anakhazikitsa lamulo lanji lokhudza cikwati?
4 Apa Yesu anaonetsa kuti Mulungu ndiye anayambitsa cikwati, ndipo anagogomeza kuti ciyenela kukhala mgwilizano wacikhalile. Mulungu sanauze Adamu na Hava kuti ngati afuna angasudzulane na kuthetsa cikwati cawo. Lamulo limene Mulungu anakhazikitsa pa cikwati ca mu Edeni, linali lakuti cikwati ciyenela kukhala ca anthu ‘aŵili,’ mwamuna mmodzi na mkazi mmodzi. Ndipo aŵiliwo ayenela kukhala pa mgwilizano wacikhalile.
KUSINTHA KWA KANTHAWI KOKHUDZA CIKWATI
5. Kodi imfa imakhudza bwanji cikwati?
5 Monga tidziŵila, kucimwa kwa Adamu kunasintha zinthu zambili. Mwacitsanzo, kunabweletsa imfa, imene imakhudza cikwati. Pofotokoza zakuti Akhristu sali pansi pa Cilamulo ca Mose, mtumwi Paulo anakambako za mmene imfa imakhudzila cikwati. Iye anakamba kuti imfa imathetsa cikwati, komanso kuti mkazi kapena mwamuna wofeledwa amakhala na ufulu wokwatilanso.—Aroma 7:1-3.
6. Kodi Cilamulo ca Mose cinaonetsa bwanji mmene Mulungu amaonela cikwati?
6 Cilamulo cimene Mulungu anapatsa Aisiraeli cinali na malangizo okhudza cikwati. Cinali kulola anthu kukwatila cipali. Mcitidwe umenewu unalipo kale pamene Mulungu anali kupeleka Cilamulo kwa Aisiraeli. Koma Mulungu anapeleka malangizo oletsa amuna kucitila nkhanza akazi awo. Mwacitsanzo, ngati Mwisiraeli wakwatila kapolo, ndipo pambuyo pake n’kukwatila mkazi wina waciŵili, sanafunike kuleka kupatsa mkazi woyambayo cakudya, zovala, na mangawa a m’cikwati. Mulungu anali kufuna kuti azimuteteza na kumusamalila mkaziyo. (Eks. 21:9, 10) N’zoona kuti sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. Koma izi zitiphunzitsa kuti Yehova amaona cikwati kukhala camtengo wapatali. Kodi zimenezi sizikulimbikitsani kulemekeza cikwati?
7, 8. (a) Malinga na Deuteronomo 24:1, kodi Cilamulo ca Mose cinali kulola okwatilana kusudzulana pa cifukwa citi? (b) Nanga Yehova amakuona bwanji kusudzulana?
7 Nanga m’Cilamulo munali malangizo otani pa nkhani ya kusudzulana? Olo kuti Mulungu sanali kufuna kuti mwamuna na mkazi azisudzulana, nthawi zina anali kulola mwamuna kusudzula mkazi wake ngati “wam’peza ndi vuto linalake.” (Ŵelengani Deuteronomo 24:1.) Cilamulo sicinafotokoze mwacindunji kuti “vuto” limenelo linali ciani maka-maka. Koma liyenela kuti linali vuto lalikulu ndi locititsa manyazi, osati colakwa cacing’ono ayi. (Deut. 23:14) Koma pofika m’nthawi ya Yesu, Ayuda ambili anali kusudzulana “pa cifukwa ciliconse.” (Mat. 19:3) Mwacionekele, ise sitingafune kutengela khalidwe loipa limeneli.
8 Zimene mneneli Malaki analemba zimatithandiza kudziŵa mmene Mulungu amaonela nkhani ya kusudzulana. M’nthawi yake, amuna ambili aciisiraeli anali kusudzula akazi a pa unyamata wawo popanda zifukwa zomveka, mwina n’colinga cakuti akwatile kamtsikana kacikunja. Malaki anafotokoza mmene Mulungu anali kuonela khalidweli. Analemba kuti: “Ine [Mulungu] ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.” (Mal. 2:14-16) Izi n’zogwilizana na zimene Mulungu anakamba zokhudza cikwati coyamba. Iye anati: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Gen. 2:24) Pambuyo pake, Yesu anatilimbikitsa kuona cikwati mmene Atate wake amacionela. Anati: “Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.”—Mat. 19:6.
PALI MAZIKO AMODZI CABE A CISUDZULO
9. Kodi mawu a Yesu a pa Maliko 10:11, 12 atanthauza ciani?
9 Mwina tingafunse kuti: ‘Kodi pali maziko alionse a cisudzulo amene amapatsa Mkhristu ufulu wokwatilanso?’ Yesu anafotokoza maganizo ake pa nkhaniyi. Anati: “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatila wina, wacita cigololo molakwila mkaziyo. Ndipo ngati mkazi wasiya mwamuna wake, ndiyeno n’kukwatiwa ndi wina, wacita cigololo.” (Maliko 10:11, 12; Luka 16:18) Conco, n’zoonekelatu kuti Yesu anali kulemekeza cikwati, ndipo anali kufuna kuti enanso azicilemekeza. Malinga n’zimene Yesu anakamba, ngati Mkhristu wasudzula mwamuna kapena mkazi wake wosalakwa n’kukakwatila wina, ndiye kuti wacita cigololo. Zili conco cifukwa kusudzulana pa zifukwa zina, kupatulapo dama, sikuthetsa cikwati pa maso pa Mulungu. Iye amaonabe aŵiliwo kukhala “thupi limodzi.” Komanso Yesu anakamba kuti, ngati mwamuna wasudzula mkazi wake wosalakwa, amaika mkaziyo pa mayeselo ocita cigololo. Motani? M’masiku amenewo, mkazi akasudzulidwa anali kukakamizika kukwatiwanso kuti azipeza zofunikila mu umoyo. Cikwati cotelo n’cigololo.
10. Kodi maziko a cisudzulo amene amapatsa Mkhristu ufulu wokwatilanso ni ati?
10 Yesu anafotokoza maziko a cisudzulo pamene anati: “Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatila wina wacita cigololo, kupatulapo ngati wamusiya cifukwa ca dama [M’Cigiriki, por·nei’a].” (Mat. 19:9) Pa Ulaliki wake wa pa Phili, Yesu anaichulanso mfundo imeneyi. (Mat. 5:31, 32) Pa nthawi zonse ziŵilizi, Yesu anachula liwu lakuti “dama.” Dama limaphatikizapo makhalidwe onse oipa okhudzana ndi zakugonana, monga cigololo, uhule, kugonana kwa anthu osakwatilana, mathanyula [kugonana kwa amuna kapena akazi okha-okha], komanso kugonana ndi nyama. Conco, ngati mwamuna wokwatila wacita cigololo, mkazi wake angasankhe kum’sudzula kapena kum’khululukila. Ngati mkaziyo wasankha kum’sudzula, ndiye kuti pa maso pa Mulungu, cikwatico catha.
11. N’cifukwa ciani nthawi zina Mkhristu angasankhe kukhululukila mnzake wa m’cikwati olo kuti pali maziko a m’Malemba a cisudzulo?
11 Komabe, Yesu sanakambe kuti ngati wina m’cikwati wacita dama (por·nei’a), ndiye kuti kulibe kucitila mwina koma kum’sudzula basi. Mwacitsanzo, mkazi angasankhe kukhalabe m’cikwati na mwamuna wake amene wacita cigololo. Zingakhale kuti amamukondabe mwamunayo, ndipo ni wokonzeka kumukhululukila na kuthandizana naye kukonzanso cikwati cawo. Komanso ngati wasankha kum’sudzula mwamunayo, koma osakwatiwanso, angakumane na zovuta zina. Mwacitsanzo, kodi adzapeza bwanji zosoŵa zakuthupi? Nanga bwanji za cilako-lako cake cakugonana? Komanso, kodi adzathana bwanji na vuto la kusungulumwa? Nanga bwanji ngati pali ana? Kodi kusudzulana kudzapangitsa kuti cikhale covuta kuwaphunzitsa coonadi? (1 Akor. 7:14) Conco, n’zoonekelatu kuti munthu wokhulupilika amene wasankha kusudzula mnzake wam’cikwati angakumane na mavuto aakulu ndithu.
12, 13. (a) Kodi m’cikwati ca Hoseya munali mavuto anji? (b) N’cifukwa ciani Hoseya anakatenganso mkazi wake Gomeri? Nanga izi zitiphunzitsa ciani pa nkhani ya cikwati?
12 Nkhani ya Hoseya itiphunzitsa zambili za mmene Mulungu amaonela cikwati. Mulungu analamula Hoseya kuti akakwatile mkazi, dzina lake Gomeri. Ndipo anakamba kuti mkaziyo “adzacita dama,” komanso kuti adzakhala “ndi ana cifukwa ca dama” lakelo. Gomeri “anatenga pakati ndipo anabelekela [Hoseya] mwana wamwamuna.” (Hos. 1:2, 3) Patapita zaka, Gomeri anabalanso mwana wamkazi ndi wamwamuna, ndipo mwacionekele onse anali ana am’cigololo. Olo kuti iye anacita cigololo mobweleza-bweleza, Hoseya sanam’sudzule. Pamapeto pake, mkaziyo anasiya Hoseya na kukakhala kapolo. Koma Hoseya anakam’gula na kubwela nayenso pa nyumba. (Hos. 3:1, 2) Apa Yehova anali kuseŵenzetsa Hoseya pocitila cithunzi zimene iye anacita pokhululukila mobweleza-bweleza Aisiraeli osakhulupilika, amene anali kucita cigololo cauzimu. Kodi tingaphunzilepo ciani pa nkhaniyi?
13 Ngati Mkhristu wokwatila wacita cigololo, mnzake wosalakwayo amafunika kupanga cosankha. Yesu anakamba kuti wosalakwayo angasankhe kum’sudzula mnzakeyo n’kukakwatilana na wina. Koma ngati afuna, angasankhe kumukhululukila. Kucita zimenezi sikulakwa. Hoseya anam’tenganso mkazi wake Gomeri. Mkaziyo atabwelelanso kwa Hoseya, sanafunike kugona na mwamuna aliyense. Ngakhale Hoseya ‘sanagone naye’ kwa kanthawi. (Hos. 3:3) Koma pambuyo pake, iye ayenela kuti anayambanso kukhala naye malo amodzi mkaziyo. Kucita izi kunacitila cithunzi zimene Mulungu anacita pololela kukhululukila anthu ake na kupitiliza kukhala nawo pa ubwenzi wapadela. (Hos. 1:11; 3:3-5) Kodi zimenezi zitiphunzitsa ciani pa nkhani ya cikwati masiku ano? Mkhristu wokhulupilika akayambanso kukhala malo amodzi na mnzake wa m’cikwati amene anacita dama, zimaonetsa kuti wamukhululukila. (1 Akor. 7:3, 5) Zikakhala conco, sipakhalanso maziko a cisudzulo. Ndipo aŵiliwo amafunika kuthandizana kukonza cikwati cawo. Akatelo, amasonyeza kuti amaona cikwati mmene Mulungu amacionela.
LEMEKEZANI CIKWATI OLO PAMENE MULI MAVUTO AAKULU
14. Malinga na 1 Akorinto 7:10, 11, n’ciani cingacitike m’cikwati?
14 Akhristu tonse tiyenela kulemekeza cikwati, monga mmene Yesu na Yehova amacitila. Komabe, cifukwa ca kupanda ungwilo, ena amalephela kucita zimenezi. (Aroma 7:18-23) Conco, n’zosadabwitsa kuti Akhristu ena m’nthawi ya atumwi, anali na mavuto aakulu m’vikwati vawo. Paulo analemba kuti “mkazi asasiye mwamuna wake.” Ngakhale n’telo, Akhristu ena anali kupatukana ndithu.—Ŵelengani 1 Akorinto 7:10, 11.
Ngati n’cikwati canu muli mavuto, kodi mungacite ciani kuti cisathe? (Onani palagilafu 15)
15, 16. (a) Kodi okwatilana ayenela kucita ciani ngakhale kuti m’cikwati cawo muli mavuto? N’cifukwa ciani afunika kutelo? (b) Kodi malangizo amenewa amagwila nchito bwanji ngati wina m’cikwati si Mboni?
15 Palembali, Paulo sanachule mavuto amene anacititsa anthu ena okwatilana kupatukana. Koma mwacionekele vuto silinali lakuti mwamuna anacita ciwelewele, cifukwa mkazi akanakhala na ufulu wom’sudzula n’kukakwatiwa na wina. Paulo analemba kuti mkazi amene wasiya mwamuna wake, ayenela kukhala “conco wosakwatiwa. Apo ayi, abwelelane ndi mwamuna wakeyo.” Conco, Mulungu amaonabe aŵiliwo monga thupi limodzi. Paulo anapeleka malangizo akuti mosasamala kanthu za mavuto amene okwatilana ali nawo, ngati vuto si cigololo, ayenela kukambilana kuti apitilize kukhala limodzi. Iwo angapemphe malangizo a m’Baibo kwa akulu mu mpingo. Akulu satengela mbali pa nkhaniyo, koma amapeleka malangizo a m’Malemba othandiza.
16 Nanga bwanji ngati Mkhristu ali m’cikwati na munthu amene si Mboni? Kodi m’cikwati mukabuka mavuto, ndiye kuti ni bwino kungopatukana naye? Monga taonela kale, Malemba amakamba kuti dama cabe ndiwo maziko a cisudzulo. Koma safotokoza mavuto amene angakhale maziko a kupatukana. Paulo analemba kuti: “Mkazi amene mwamuna wake ndi wosakhulupilila, koma mwamunayo akulola kukhala naye, asamusiye mwamuna wakeyo.” (1 Akor. 7:12, 13) Malangizo amenewa amagwilanso nchito masiku ano.
17, 18. N’cifukwa ciani Akhristu ena amasankha kusapatukana na mnzawo wa m’cikwati olo kuti akukumana na mavuto aakulu?
17 Nthawi zina, “mwamuna wosakhulupilila” angacite zinthu zoonetsa kuti safuna ‘kukhalabe naye’ mkazi wake. Akhoza kumam’citila nkhanza kwambili, cakuti angaone kuti moyo wake uli paciopsezo. Mwinanso mwamunayo angamakane kusamalila mkaziyo pamodzi ndi ana. Kapenanso angamacite zinthu zolepheletsa mkaziyo kutumikila Yehova mokhulupilika. Zikakhala conco, alongo ena amasankha kupatukana na mwamuna wawo, cifukwa zocita zake zimaonetsa kuti safuna ‘kukhalabe naye’ mlongoyo. Koma alongo ena amene amakumana na mavuto ofananawo, amasankha kukhalabe naye mwamuna wotelo. Iwo amapilila na kuyesetsa kucita mbali yawo kuti akonze zinthu. Cifukwa ciani amatelo?
18 Anthu akapatukana, cikwati cawo cimakhala kuti cikalipo. Ndipo monga takambila kale, ngati anthu apatukana, aliyense wa iwo amakumana na zovuta zinazake. Mtumwi Paulo anafotokoza ubwino wina umene umakhalapo ngati okwatilana asankha kuti asapatukane. Analemba kuti: “Mwamuna wosakhulupilila amayeletsedwa cifukwa ca mkazi wake, ndiponso mkazi wosakhulupilila amayeletsedwa cifukwa ca m’baleyo, apo ayi, ana anu akanakhala osayela, koma tsopano ndi oyela.” (1 Akor. 7:14) Akhristu ambili okhulupilika anapitilizabe kukhala na mnzawo wa m’cikwati wosakhulupilila, olo kuti anali kukumana na mavuto aakulu. Iwo anadzionela okha ubwino wocita zimenezi, pamene mnzawoyo anakhala Mboni.—Ŵelengani 1 Akorinto 7:16; 1 Pet. 3:1, 2.
19. N’cifukwa ciani mu mpingo wa Mboni za Yehova muli vikwati vambili volimba?
19 Yesu anapeleka malangizo pa nkhani ya kusudzulana. Ndipo mtumwi Paulo, mouzilidwa analemba malangizo okhudza kupatukana. Yesu na Paulo anali kufuna kuti atumiki a Mulungu azilemekeza cikwati. Masiku ano, mu mpingo wacikhristu pa dziko lonse muli abale na alongo ambili amene ali na vikwati volimba ndipo amakhala mwacimwemwe. Mwacionekele, ngakhale mu mpingo mwanu muli mabanja ambili acimwemwe. M’mabanja amenewo muli abale okhulupilika amene amakonda akazi awo, komanso alongo odzipeleka amene amakonda amuna awo. Izi zimaonetsa kuti n’zotheka cikwati kukhala colemekezeka. Paja Mulungu anati: “Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo aŵiliwo adzakhala thupi limodzi.” Ndithudi, n’zokondweletsa kwambili kuti masiku ano pali mabanja ambili-mbili amene amaonetsa kuti mawu a Mulungu amenewa ni oona.—Aef. 5:31, 33.