-
Muzicita Zinthu Mogwilizana ndi Pemphelo Lacitsanzo—Mbali 1Nsanja ya Mlonda—2015 | June 15
-
-
“ATATE WATHU WAKUMWAMBA”
4. Kodi mau akuti “Atate wathu” amatikumbutsa ciani? Nanga n’cifukwa ciani Yehova amachedwa “Atate” kwa Akristu amene ali ndi ciyembekezo cokhala pa dziko lapansi?
4 Mau akuti “Atate wathu” osati “Atate wanga,” amatikumbutsa kuti tili ‘m’gulu la abale’ amene amakondanadi. (1 Pet. 2:17) Umenewu ndi mwai waukulu kwambili. Akristu odzozedwa, amene asankhidwa ndi Mulungu kukhala ana ake amene adzakhala ndi moyo kumwamba, moyenelela amachula Yehova kuti “Atate.” (Aroma 8:15-17) Akristu amene ali ndi ciyembekezo cokhala padziko lapansi kosatha amachula Yehova kuti “Atate.” Yehova ndiye Mpatsi wa Moyo ndipo mwacikondi amapeleka zosowa kwa olambila onse oona. Awo amene ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi adzachedwa ana a Mulungu enieni, akadzakhala angwilo ndi kupyola ciyeso comaliza.—Aroma 8:21; Chiv. 20:7, 8.
-
-
Muzicita Zinthu Mogwilizana ndi Pemphelo Lacitsanzo—Mbali 1Nsanja ya Mlonda—2015 | June 15
-
-
“DZINA LANU LIYELETSEDWE”
7. Ndi mwai wotani umene anthu a Mulungu ali nao? Nanga tifunika kucita ciani ndi mwai umenewo?
7 Tili ndi mwai waukulu kwambili osati wodziŵa dzina la Mulungu cabe komanso woliimila monga “anthu ochedwa ndi dzina lake.” (Mac. 15:14; Yes. 43:10) Timapempha Atate wathu wa kumwamba kuti: “Dzina lanu liyeletsedwe.” Pempho limeneli lingakusonkhezeleni kupempha Yehova kuti akuthandizeni kupewa kucita kapena kukamba zinthu zilizonse zosalemekeza dzina lake lopatulika. Tisakhale monga anthu a m’nthawi ya atumwi amene sanali kucita zimene anali kuphunzitsa. Mtumwi Paulo anawalembela kuti: “Dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu amitundu cifukwa ca inu.”—Aroma 2:21-24.
8, 9. Pelekani citsanzo coonetsa kuti Yehova amadalitsa anthu amene amafuna kuyeletsa dzina lake.
8 Timafuna kuyeletsa dzina la Mulungu. Mwacitsanzo, mlongo wina ku Norway mwamuna wake atafa mwadzidzidzi, anatsala yekha ndi mwana wake wa zaka ziŵili. Mlongoyu anati: “Inali nthawi yovuta kwambili pa umoyo wanga.” Anaonjezela kuti: “Ndinali kupemphela tsiku lililonse pafupifupi nthawi iliyonse kuti ndikhale wolimba pa cisoni cimene ndinali naco. Komanso sindinafune kupatsa Satana mwai wotonza Yehova mwa kusankha zinthu mopanda nzelu kapena kucita zinthu mosakhulupilika. Ndinali kufunitsitsa kuyeletsa dzina la Yehova ndipo ndinali kufuna kuti mwana wanga adzaonanenso ndi atate wake m’paladaiso.”—Miy. 27:11.
9 Kodi Yehova anayankha pemphelo limeneli? Inde. Mlongo ameneyu anathandizidwa ndi okhulupilila anzake. Patapita zaka 5, iye anakwatiwa ndi mkulu. Mwana wake amene ali ndi zaka 20, tsopano ndi m’bale wobatizidwa. Mlongoyo anati: “Ndine wokondwa kwambili kuti mwamuna wangayu anandithandiza kulela mwana wanga.”
10. Kodi cofunika n’ciani kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe kothelatu?
10 Kodi cofunika n’ciani kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe kothelatu ndi kucotsedwa citonzo ciliconse? Kuti zimenezi zitheke, Yehova afunika kucitapo kanthu kuti acotse onse amene amakana ulamulilo wake mwadala. (Ŵelengani Ezekieli 38:22, 23.) Anthu adzakhala angwilo pang’ono ndi pang’ono. Tikulakalaka nthawi imene anthu onse adzalemekeza dzina la Yehova. Ndiyeno potsilizila pake, Atate wathu wa kumwamba amene ndi wacikondi adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”—1 Akor. 15:28.
-