LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lff phunzilo 23
  • Ubatizo ni Khomo la ku Madalitso Oculuka!

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ubatizo ni Khomo la ku Madalitso Oculuka!
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Ubatizo Ni Wofunika kwa Mkhristu Aliyense
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Kodi Ndimwe Wokonzeka Kubatizika?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Kodi Ubatizo Ndi Wofunika Bwanji Paubwenzi Wanu ndi Mulungu?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Sankhani Kutumikila Yehova
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
lff phunzilo 23
Phunzilo 23. Mzimayi akubatizika kukhala Mboni ya Yehova pomizidwa thupi lonse m’madzi.

PHUNZILO 23

Ubatizo ni Khomo la ku Madalitso Oculuka!

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Yesu anaphunzitsa kuti, kuti munthu akhale Mkhristu afunika kubatizika. (Ŵelengani Mateyu 28:19, 20.) Kodi ubatizo n’ciyani? Nanga munthu ayenela kucita ciyani kuti abatizike?

1. Kodi ubatizo uyenela kucitika bwanji?

Mawu Acigiriki omasulidwa kuti “kubatiza” amatanthauza “kumiza m’madzi.” Pamene Yesu anabatizika, anamizidwa mu mtsinje wa Yorodano, kenako ‘anavuuka m’madzimo.’ (Maliko 1:9, 10) Mofananamo, Akhristu oona amabatizika mwa kumizidwa thupi lonse m’madzi.

2. Kodi munthu amaonetsa ciyani akabatizika?

Munthu akabatizika, amaonetsa kuti wadzipatulila kwa Yehova Mulungu. Kodi munthu amadzipatulila bwanji? Asanabatizike, ali kwa yekha, amapemphela kwa Yehova kumuuza kuti akufuna kum’tumikila kwa moyo wake wonse. Amalonjeza Yehova kuti azilambila iye yekha basi, komanso kuti kucita cifunilo ca Mulungu ndiko kudzakhala cinthu cofunika kopambana pa umoyo wake. Cina, amasankha ‘kudzikana yekha . .  . na kutsatila mosalekeza’ ziphunzitso za Yesu, komanso citsanzo cake. (Mateyu 16:24) Mwa kudzipatulila na kubatizika, iye adzakhala pa ubale wolimba na Yehova, komanso alambili anzake.

3. Kodi munthu ayenela kucita ciyani asanabatizike?

Mufunika kuphunzila za Yehova na kulimbitsa cikhulupililo canu mwa iye. (Ŵelengani Aheberi 11:6.) Pamene cidziŵitso canu na cikhulupililo canu zikuwonjezeka, naconso cikondi canu pa Yehova cidzakulilako. Ndipo mosakaika konse, mudzafuna kuuzako ena za iye komanso kukhala na umoyo wogwilizana na malamulo ake. (2 Timoteyo 4:2; 1 Yohane 5:3) Munthu akayamba ‘kuyenda mogwilizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti am’kondweletse pa ciliconse,’ angasankhe kupatulila moyo wake kwa Mulungu na kubatizika.—Akolose 1:9, 10.a

KUMBANI MOZAMILAPO

Onani zimene tiphunzilapo pa ubatizo wa Yesu, komanso zimene munthu ayenela kucita kuti atenge sitepe yofunika imeneyi.

4. Maphunzilo amene titengapo pa ubatizo wa Yesu

Ŵelengani Mateyu 3:13-17, kuti mudziŵe mfundo zowonjezeleka pa ubatizo wa Yesu. Kenaka kambilanani mafunso aya:

  • Kodi Yesu anali khanda pamene anali kubatizika?

  • Kodi anabatizika motani? Kodi anangomuwaza madzi?

Yesu anayamba kugwila nchito imene Mulungu anam’patsa padziko lapansi pamene anabatizika. Ŵelengani Luka 3:21-23, komanso Yohane 6:38, na kukambilana funso ili:

  • Yesu atangobatizika, kodi ni nchito iti imene anaika patsogolo pa umoyo wake?

5. Ubatizo ni colinga cimene mungakwanilitse

Mungakhale na nkhawa mukaganizila nkhani yodzipatulila na kubatizika. Komabe, mungapite patsogolo pang’ono-m’pang’ono, mpaka mutaona kuti ndinu wokonzeka tsopano kupanga cisankho cimeneci. Kuti muone anthu ena amene anacita zimenezi, tambani VIDIYO.

VIDIYO: Kupalana Ubwenzi na Yehova (1:11)

Ŵelengani Yohane 17:3, komanso Yakobo 1:5, na kukambilana funso ili:

  • N’ciyani cingathandize munthu kukonzekela kukabatizika?

A. Mzimayi akudzipatulila kwa Mulungu m’pemphelo. B. Mzimayi ameneyo akubatizika kukhala Mboni ya Yehova pomizidwa thupi lonse m’madzi.
  1. Timadzipatulila mwa kuuza Yehova m’pemphelo kuti tifuna kum’tumikila kwa moyo wathu wonse

  2. Pa ubatizo wanu, mumaonetsa onse opezekapo kuti munadzipatulila kale kwa Mulungu

6. Tikabatizika timaloŵa m’banja la Yehova

Tikabatizika, timaloŵa m’banja la padziko lonse. Olo kuti timacokela kosiyana-siyana, komanso tili na zikhalidwe zosiyana-siyana, tili na cikhulupililo cimodzi, ndipo timatsatila mfundo za Yehova zimodzi-modzi za makhalidwe abwino. Ŵelengani Salimo 25:14, komanso 1 Petulo 2:17, na kukambilana funso ili:

  • Malinga na Malemba aya, kodi munthu amapindula bwanji akabatizika?

Cithunzi: Mlongo wobatizika ni wacimwemwe poganizila ubale wabwino umene ali nawo na anthu ena mu mpingo. 1. Akudandaulilako mlongo wina. 2. Akuthandiza mlongo wacikulile kuyenda. 3. Akudya cakudya pamodzi na mabwenzi a misinkhu yosiyana-siyana. 4. Akulalikila mwamuna wina mothandizidwa na mlongo mnzake. 5. Akudzijambula pikicha pamodzi na Mboni ziŵili za mafuko ena pa msonkhano wacigawo.

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Sindine wokonzeka kuti nibatizike.”

  • Ngati ni mmene inunso mumaonela, kodi muganiza kuti ubatizo ni cinthu cofunikabe kwa inu?

CIDULE CAKE

Yesu anaphunzitsa kuti Akhristu ayenela kubatizika. Kuti munthu afike pobatizika, afunika coyamba alimbitse cikhulupililo cake mwa Yehova, azitsatila malamulo a Mulungu pa umoyo wake, komanso adzipatulile kwa Mulungu.

Mafunso Obweleza

  • Kodi ubatizo uyenela kucitika bwanji, ndipo n’cifukwa ciyani ni wofunika kwambili?

  • Kodi ubatizo ni cizindikilo coonetsa ciyani?

  • Kodi ni masitepe ati amene amafikitsa munthu pa kudzipatulila, pambuyo pake n’kubatizika?

Colinga

FUFUZANI

Dziŵani ubatizo woyenela komanso wosayenela.

“Kodi Ubatizo N’chiyani?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onaninso masitepe othandiza munthu kupita patsogolo kuti akabatizike

“Kukonda Yehova na Kum’yamikila Kudzakusonkhezelani Kubatizika” (Nsanja ya Mlonda, March 2020)

Ŵelengani cimene cinasonkhezela munthu wina kupanga cisankho cakuti abatizike.

“Anali Kufuna Kuti Nione Ndekha Kuti Zoona ni Ziti” (Nsanja ya Mlonda, February 1, 2013)

Onani cifukwa cake ubatizo ni colinga cofunika kwambili, komanso mmene mungaukonzekelele.

“Kodi Niyenela Kubatizika?” (Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, mutu 37)

a Ngati munthu anabatizika kale kucipembedzo cina, ayenela kubatizikanso. Cifukwa ciyani? Cifukwa cipembedzo cimeneco sicinam’phunzitse coonadi ca m’Baibo. Kuti tikhale ogwilizana m’cikhulupililo cimodzi cozikika pa coonadi, tiyenelanso kubatizika ubatizo umodzi wozikika pa coonadi.—Onani Machitidwe 19:1-5; Aefeso 4:5; komanso Phunzilo 13.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani