LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kodi Yesu Ndani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 4. Yesu si Mulungu Wamphamvuzonse

      Baibo imaphunzitsa kuti ngakhale kuti Yesu ni munthu wauzimu wamphamvu kumwamba, iye amagonjela kwa Atate wake, Yehova Mulungu. Tikunena zimenezi cifukwa ciyani? Tambani VIDIYO kuti muone zimene Baibo imakamba zokhudza udindo wa Yesu pouyelekezela na udindo wa Mulungu Wamphamvuzonse.

      VIDIYO: Kodi Yesu Khristu ni Mulungu? (3:22)

      Malemba otsatilawa adzatithandiza kumvetsa ubale umene ulipo pakati pa Yehova na Yesu. Pambuyo poŵelenga lemba lililonse, kambilanani mafunso ali pansi pake.

      Ŵelengani Luka 1:30-32.

      • Kodi mngelo anaufotokoza motani ubale uli pakati pa Yesu na Yehova Mulungu “Wam’mwambamwamba”?

      Ŵelengani Mateyu 3:16, 17.

      • Pa ubatizo wa Yesu, kodi mawu ocokela kumwamba anati ciyani?

      • Nanga muganiza mawuwo anali a ndani?

      Ŵelengani Yohane 14:28.

      • Kodi pakati pa tate na mwana wake, amakhala wamkulu ndani, pa msinkhu na ulamulilo?

      • Pamene Yesu anachula Yehova kuti Atate, kodi zitiuza ciyani?

      Ŵelengani Yohane 12:49.

      • Kodi Yesu amaganiza kuti iye na Atate wake ni olingana? Nanga inu muganiza bwanji?

  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciyani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • Phunzilo 31. Yesu Khristu Mfumu yakumwamba pamaso pa ulemelelo wa Yehova.

      PHUNZILO 31

      Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciyani?

      Nkhani yaikulu m’Baibo ni yokhudza Ufumu wa Mulungu. Yehova adzagwilitsa nchito Ufumu umenewo kukwanilitsa cifunilo cake ca poyamba cokhudza dziko lapansi. Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciyani? Tidziŵa bwanji kuti pali pano ukulamulila? Nanga n’ciyani cimene wacitapo kale? Kodi udzacita ciyani m’tsogolo? Mafunso aya adzayankhidwa m’phunzilo lino, komanso m’maphunzilo aŵili otsatila.

      1. Kodi Ufumu wa Mulungu n’ciyani? Nanga Mfumu yake ndani?

      Ufumu wa Mulungu ni boma limene Yehova Mulungu analikhazikitsa. Mfumu yake ni Yesu Khristu, ndipo akulamulila kucokela kumwamba. (Mateyu 4:17; Yohane 18:36) Baibo imakamba za Yesu kuti: “Iye adzalamulila monga Mfumu . . . kwamuyaya.” (Luka 1:32, 33) Monga Mfumu yoikidwa na Mulungu kumwamba, Yesu adzalamulila anthu onse padziko lapansi.

      2. Kodi ndani akulamulila pamodzi na Yesu?

      Yesu sakulamulila yekha. Anthu ocokela “mu fuko lililonse, cinenelo ciliconse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse. . . . adzakhala mafumu olamulila dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:9, 10) Ni angati amene adzalamulila na Khristu? Kucokela pamene Yesu anali padziko lapansi, Akhristu mamiliyoni akhala otsatila ake. Koma anthu okwana 144,000 okha ni amene amapita kumwamba kukalamulila na Yesu. (Ŵelengani Chivumbulutso 14:1-4.) Akhristu ena otsalawa adzakhala nzika za Ufumuwo.—Salimo 37:29.

      3. Kodi Ufumu wa Mulungu umapambana bwanji maboma a anthu?

      Ngakhale olamulila atayesesa bwanji kucita zabwino, alibe mphamvu zokwanitsa kucita zonse zimene afuna. Ndipo m’kupita kwa nthawi, angaloŵedwe m’malo na olamulila ena adyela osafuna kuthandiza anthu. Koma Yesu, monga Mfumu yoikidwa na Mulungu, sadzaloŵedwa m’malo na wina aliyense. Mulungu wakhazikitsa “Ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.” (Danieli 2:44) Yesu adzalamulila dziko lonse lapansi, ndipo sadzakondela munthu aliyense. Iye ni wacikondi, wokoma mtima, komanso wacilungamo. Adzaphunzitsa anthu kukhalanso na makhalidwe amenewa—kucitilana zinthu mwacikondi, mokoma mtima, komanso mwacilungamo.—Ŵelengani Yesaya 11:9.

      KUMBANI MOZAMILAPO

      Pezani cifukwa cake Ufumu wa Mulungu umapambana maboma onse a anthu.

      Yesu Khristu akulamulila dziko lapansi ali pa mpando wake wacifumu kumwamba. Olamulila anzake nawonso akhala pamipando yawo yacifumu kumbuyo kwake. Ulemelelo wa Yehova ukuwala kumbuyo kwawo.

      4. Ufumu wa Mulungu ni boma limene lidzalamulile dziko lonse lapansi

      Yesu Khristu ali na mphamvu zambili zolamulila, kuposa wolamulila aliyense m’mbili yonse ya anthu. Ŵelengani Mateyu 28:18, na kukambilana funso ili:

      • Kodi ulamulilo wa Yesu umapambana bwanji ulamulilo wa munthu aliyense?

      Maboma a anthu amasintha-sintha, ndipo boma lililonse limalamulila cabe mbali yocepa ya dziko lapansi. Nanga bwanji za Ufumu wa Mulungu? Ŵelengani Danieli 7:14, na kukambilana mafunso aya:

      • N’cifukwa ciyani zili bwino kuti Ufumu wa Mulungu “sudzawonongedwa”?

      • Ndipo n’cifukwa ciyani zili bwino kuti udzalamulila dziko lonse lapansi?

      5. Maulamulilo a anthu ayenela kuloŵedwa m’malo

      N’cifukwa ciyani Ufumu wa Mulungu uyenela kuloŵa m’malo maboma a anthu? Tambani VIDIYO, na kukambilana mafunso otsatilawa.

      VIDIYO: Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?—Mbali Yake (1:41)

      • Kodi ulamulilo wa anthu wabweletsa mavuto otani?

      Ŵelengani Mlaliki 8:9, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi muona kuti Ufumu wa Mulungu ufunikadi kuloŵa m’malo maboma a anthu? Cifukwa ciyani?

      6. Ufumu wa Mulungu uli na olamulila amene amatimvetsetsa

      Cifukwa cakuti Yesu, Mfumu yathu, anakhalapo munthu, iye amatha kutimvela “cisoni pa zofooka zathu.” (Aheberi 4:15) Amuna na akazi okhulupilika okwana 144,000, amene adzalamulile pamodzi na Yesu, Yehova amawasankha kucokela mu “fuko lililonse, cinenelo ciliconse, mtundu uliwonse, ndi dziko lililonse.”—Chivumbulutso 5:9.

      • Kodi n’zokulimbikitsani kudziŵa kuti Yesu na olamulila anzake amatimvetsetsa pa mavuto amene timakumana nawo? Cifukwa ciyani?

      Amuna komanso akazi odzozedwa a panthawi zosiyana-siyana ndiponso a mitundu yosiyana-siyana.

      Yehova wasankha amuna na akazi kucokela mu zikhalidwe zosiyana-siyana kuti akalamulile pamodzi na Yesu

      7. Ufumu wa Mulungu uli na malamulo abwino kuposa maboma a anthu

      Maboma amapanga malamulo amene colinga cake ni kupindulila nzika zawo na kuziteteza. Ufumu wa Mulungu nawonso uli na malamulo amene nzika zake ziyenela kutsatila. Ŵelengani 1 Akorinto 6:9-11, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi muganiza dziko lidzakhala bwanji pamene munthu aliyense azikatsatila malamulo a Mulungu?a

      • Kodi muganiza n’zomveka Yehova kuyembekezela nzika za Ufumu wake kumvela malamulo ake? Cifukwa ciyani?

      • N’ciyani cionetsa kuti anthu osamvela malamulo a Mulungu akhoza kusintha?—Onani vesi 11.

      Wapolisi akuimitsa mamotoka mu msewu pamalo owolokela anthu ambili.

      Maboma amakhazikitsa malamulo oteteza nzika zawo kuti azipindulile. Koma malamulo a Ufumu wa Mulungu ni opambana pa kuteteza nzika zake na kuzipindulila

      ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Ufumu wa Mulungu uli mu mtima wa munthu”

      • Nanga inu muganiza bwanji?

      CIDULE CAKE

      Ufumu wa Mulungu ni boma lenileni kumwamba, limene lidzalamulila dziko lonse lapansi.

      Mafunso Obweleza

      • Kodi amene adzakhale olamulila mu Ufumu wa Mulungu ndani?

      • N’cifukwa ciyani Ufumu wa Mulungu umapambana boma lililonse la anthu?

      • Kodi Yehova amayembekezela zotani kwa nzika za Ufumu wake?

      Colinga

      FUFUZANI

      Onani zimene Yesu anaphunzitsa za kumene Ufumu wa Mulungu uli.

      “Kodi Ufumu wa Mulungu Uli mu Mtima Mwanu?” (Nkhani ya pawebusaiti)

      N’cifukwa ciyani Mboni za Yehova zimasankha kukhulupilika ku Ufumu wa Mulungu, m’malo mwa ulamulilo wa anthu?

      Kudzipeleka ku Ufumu wa Mulungu (1:43)

      Onani zimene Baibo imafotokoza zokhudza anthu okwana 144,000 amene Yehova amawasankha kukalamulila pamodzi na Yesu.

      “Ndani Amapita Kumwamba?” (Nkhani ya pawebusaiti)

      N’ciyani cinapangitsa mzimayi wina m’ndende kukhulupilila kuti ni Mulungu yekha angabweletse cilungamo padziko lapansi?

      “Kumene Ndinadziwira Yemwe Adzathetse Kupanda Chilungamo” (Galamukani! November 2011)

      a Ena a malamulo amenewo tidzawakambilana mu Cigawo 3.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani