LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w16 April masa. 21-26
  • Pewani Kutenga Mbali m’Ndale za Dziko Loipali

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pewani Kutenga Mbali m’Ndale za Dziko Loipali
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MUZIONA MABOMA A ANTHU MMENE YEHOVA AMAWAONELA
  • KHALANI “OCENJELA” KOMA “OONA MTIMA”
  • YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI
  • TENGELANI PHUNZILO PA ZITSANZO ZA ATUMIKI A YEHOVA OKHULUPILIKA
  • Tanthauzo Lake la Kusakhalila Mbali
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kukhala Olekana Nalo Dziko
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Mmene Tingakhalile Olekana ndi Dziko
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
  • Khalanibe Okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
w16 April masa. 21-26
Wa Mboni za Yehova ali m’ndende cifukwa cokana kutenga mbali m’ndale

Pewani Kutenga Mbali m’Ndale za Dziko Loipali

“Pelekani zinthu . . . za Mulungu, kwa Mulungu.”—MATEYU 22:21.

NYIMBO: 33, 137

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi Yehova amawaona bwanji maboma a anthu?

  • Kodi tiyenela kucita ciani ngati zavuta kuti tipewe kutenga mbali m’ndale?

  • Tingaphunzile ciani kwa atumiki okhulupilika a Yehova amene sanatengemo mbali m’ndale?

1. Tingacite ciani kuti tizimvela Mulungu ndi maboma a anthu?

BAIBULO limatilamula kuti tizimvela maboma a anthu, koma limanenanso kuti tiyenela kumvela Mulungu nthawi zonse. (Machitidwe 5:29; Tito 3:1) Kodi tingacite bwanji zimenezi? Yesu anafotokoza mfundo imene imatithandiza kudziŵa amene tiyenela kumvela. Iye anakamba kuti tiyenela kupeleka “zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”[1] (Onani mau akumapeto.) (Mateyu 22:21) Timapeleka “zinthu za Kaisara kwa Kaisara” mwa kumvela malamulo a boma, kulemekeza akuluakulu a boma, ndi kupeleka msonkho. (Aroma 13:7) Koma ngati boma latilamula kucita zinthu zimene Mulungu amaletsa, timakana mwaulemu.

2. Kodi timaonetsa bwanji kuti sititenga mbali m’ndale za dzikoli?

2 Njila imodzi imene timapelekela zinthu “za Mulungu kwa Mulungu” ndi mwa kusatengako mbali m’mikangano ya ndale za dziko. Siticilikiza mbali iliyonse m’nkhani za ndale. (Yesaya 2:4) Popeza kuti Yehova walola kuti maboma a anthu azitilamulila, sitilimbana nao kapena kuwatsutsa. Komanso siticita nao zinthu zoonetsa kukonda dziko lathu. (Aroma 13:1, 2) Siticita nao makampeni ofuna kusintha boma kapena kunyengelela anthu andale kuti acite zinazake. Kuonjezela apo, sitivota pa masankho kapena kuloŵa m’zipani za ndale.

3. N’cifukwa ciani sitifunika kutenga mbali m’ndale?

3 Pali zifukwa zambili zimene Mulungu amatiuzila kuti tisamatenge mbali m’ndale. Cifukwa coyamba n’cakuti timatengela citsanzo ca Yesu, amene ‘sanali mbali ya dziko.’ Iye sanatengeko mbali m’ndale kapena m’nkhondo. (Yohane 6:15; 17:16) Cifukwa cina n’cakuti timacilikiza Ufumu wa Mulungu. Popeza kuti siticilikiza maboma a anthu, timakhala ndi cikumbumtima coyela pamene tikulalikila kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetsa mavuto onse a anthu. Zipembedzo zonama zimatenga mbali m’ndale, ndipo zimenezi zimagaŵanitsa anthu. Koma cifukwa cakuti sititenga mbali m’ndale, ndife ogwilizana ndi abale ndi alongo athu padziko lonse.—1 Petulo 2:17.

4. (a) Tidziŵa bwanji kuti mtsogolomu zidzakhala zovuta kupewa kutenga mbali m’ndale? (b) N’cifukwa ciani tifunika kukonzekela tsopano kuti tisadzatenge mbali m’ndale?

4 N’kutheka kuti m’dela limene timakhala, anthu amadziŵa kuti sititengako mbali m’ndale. Koma pamene tikuyandikila mapeto a dziko la Satanali, cidzakhala covuta kuti tipewe kutenga mbali m’ndale. Anthu masiku ano ndi “osafuna kugwilizana ndi anzawo,” ndiponso “osamva za ena,” ndipo mtsogolomu adzakhala ogaŵikana kwambili. (2 Timoteyo 3:3, 4) Abale athu ena akukumana ndi mavuto cifukwa ca kusintha kwa zinthu pa ndale m’dziko lao. Ndiye cifukwa cake tifunika kukonzekela tsopano kuti tidzakhalebe okhulupilika kwa Mulungu ngakhale panthawi yovuta. Tiyeni tikambilane zinthu zinai zimene tingacite kuti tikonzekele.

MUZIONA MABOMA A ANTHU MMENE YEHOVA AMAWAONELA

5. Kodi Yehova amawaona bwanji maboma a anthu?

5 Cinthu coyamba cimene cingatithandize kuti tisatenge mbali m’ndale ndi kuona maboma a anthu monga mmene Yehova amawaonela. Yehova atalenga anthu, sanawapatse ufulu wolamulila anzao. (Yeremiya 10:23) Iye amaona anthu onse monga banja limodzi. Koma boma lililonse limanena kuti ulamulilo wao ndiye wabwino. Izi zapangitsa magaŵano pakati pa anthu. Komanso, ngakhale maboma amene amaoneka ngati abwino, sangakwanitse kuthetsa mavuto onse a anthu. Vuto lina n’lakuti maboma amenewa amadana ndi Ufumu wa Mulungu, umene unayamba kulamulila mu 1914. Posacedwapa, Ufumu umenewu udzathetsa maboma onse a anthu.—Ŵelengani Salimo 2:2, 7-9.

Konzekelani kuti musadzatengemo mbali m’ndale mukadzakumana ndi ciyeso

6. Kodi akuluakulu a boma tiyenela kuwaona bwanji?

6 Mulungu walola kuti maboma a anthu akhalepo cifukwa cakuti amathandiza kuti m’dziko mukhaleko bata ndi mtendele. Zimenezi zimatithandiza kuti tizilalikila mosavuta uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Aroma 13:3, 4) Mulungu amatiuza kuti tizipemphelela olamulila n’colinga cakuti tikhale ndi mwai wom’lambila mwamtendele. (1 Timoteyo 2:1, 2) Ndipo anthu ena akaticitila zinthu zopanda cilungamo, tingapemphe akuluakulu a boma kuti atithandize. Izi n’zimene Paulo anacita. (Machitidwe 25:11) Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti Satana ndiye akutsogolela maboma onse a anthu, silikamba kuti iye amatsogolela wolamulila wa boma aliyense payekha. (Luka 4:5, 6) Conco, sitiyenela kupangitsa anthu ena kuganiza kuti wolamulila winawake wa boma amatsogoleledwa ndi Mdyelekezi. Baibulo limakamba kuti sitiyenela kunyoza anthu.—Tito 3:1, 2.

7. Ndi maganizo otani amene tiyenela kupewa?

7 Timamvela Mulungu mwa kupewa kukondela munthu wina wa ndale, kapena cipani ca ndale ciliconse ngakhale kuti cili ndi zolinga zabwino zimene zingatipindulitse. Nthawi zina, kucita zimenezi kungakhale kovuta. Mwacitsanzo, yelekezelani kuti anthu ena apandukila boma limene limazunza kwambili anthu, kuphatikizapo Mboni za Yehova. N’zodziŵikilatu kuti simungaloŵe m’gulu la anthu amenewo. Koma kodi mungayambe kuganiza kuti anthuwo acita bwino? Kapena mungawafunile zabwino kuti akwanitse zolinga zao? (Aefeso 2:2) Kuti tipeweletu kutenga mbali m’ndale, sitiyenela kuona kuti anthu ena a ndale ndi abwino kuposa ena. Zocita ndi zokamba zathu ziyenela kuonetsa kuti tilibe maganizo otelo.

KHALANI “OCENJELA” KOMA “OONA MTIMA”

8. Tingacite ciani kuti tikhale “ocenjela” koma “oona mtima” ngati tayesedwa kuti titenge mbali m’ndale?

8 Caciŵili cimene cingatithandize kuti tisatenge mbali m’ndale, ndi kukhala “ocenjela ngati njoka koma oona mtima ngati nkhunda.” (Ŵelengani Mateyu 10:16, 17.) Tingaonetse kuti ndife “ocenjela” mwa kuganizila mavuto amene tingakumane nao mtsogolo. Ndipo timakhala “oona mtima” mwa kupewa kutenga mbali m’ndale panthawi yovuta. Tiyeni tikambilane zinthu zina zimene tifunika kusamala nazo, ndiponso zimene tiyenela kucita kuti tipewe kutenga mbali m’zandale.

9. Ndi zinthu ziti zimene tiyenela kusamala nazo pamene tikukambilana ndi anthu?

9 Zokamba zathu. Tiyenela kukhala osamala kwambili anthu akayamba kukamba zandale. Mwacitsanzo, ngati tikukambilana za Ufumu wa Mulungu ndi munthu winawake, sitiyenela kukamba kuti tikugwilizana kapena sitikugwilizana ndi mfundo ya cipani cinacake kapena mtsogoleli winawake. M’malo mokambilana zimene anthu acita kuti athetse mavuto, gwilitsilani nchito Malemba ndi kumuuza kuti Ufumu wa Mulungu udzathetselatu mavuto onse a anthu. Ngati anthu ayamba kutsutsana pankhani inayake, monga yakuti amuna ndi akazi okhaokha azikwatilana kapena ya kucotsa mimba, auzeni zimene Mau a Mulungu amanena ndiponso zimene inu mumacita potsatila malangizo amenewo. Ngati munthu wina wakamba kuti malamulo enaake afunika kucotsedwa kapena kusinthidwa, sititengako mbali, ndipo sitimulimbikitsa kusintha maganizo ake.

Muziyelekezela zimene mwamva ndi “citsanzo ca mau olondola” ca m’Baibulo

10. Tingacite ciani kuti maganizo athu asasokonezeke ndi zimene ofalitsa nkhani amakamba?

10 Zimene ofalitsa nkhani amakamba. Nthawi zina, ofalitsa nkhani amakometsa mbali imodzi pokamba nkhani zao. Zimenezi zimacitika kwambili ngati boma ndilo limayang’anila ofalitsa nkhani. Ngati mabungwe ofalitsa nkhani kapena amtolankhani akukamba mokondela, tifunika kukhala osamala kuti tisatengele maganizo ao. Mwacitsanzo, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimakonda kumvetsela nkhani zokambidwa ndi munthu winawake cifukwa cakuti amakamba mfundo zogwilizana ndi maganizo anga pankhani za ndale?’ Kuti musatenge mbali m’zandale, pewani kuonelela kapena kuŵelenga zinthu zimene zimakometsa mbali imodzi pandale. M’malomwake, muzisankha nkhani zimene siziloŵelela m’ndale. Ndipo nthawi zonse muziyelekezela zimene mwamva ndi “citsanzo ca mau olondola” a m’Baibulo.—2 Timoteyo 1:13.

11. N’cifukwa ciani cingakhale covuta kupewa kutenga mbali m’ndale ngati timakonda kwambili zinthu zakuthupi?

11 Kukonda cuma. Ngati timaona kuti ndalama ndiponso katundu wathu n’zofunika kwambili, ndiye kuti zingakhale zovuta kupewa ndale. Pofika ca m’ma 1970, Mboni zambili ku Malawi zinathaŵa ndi kusiya katundu wao yense cifukwa cokana kuloŵa m’cipani candale. Koma comvetsa cisoni n’cakuti ena analephela kukhala ndi umoyo wosalila zambili. Mlongo wina dzina lake Ruth anati: “Ena anathaŵa nafe limodzi kupita ku dziko lina, koma pambuyo pake analoŵa m’cipani ndi kubwelela kwao cifukwa cakuti sanafune kukhala mumsasa wa othaŵa kwao.” Koma anthu ambili a Mulungu alibe maganizo otelo. Amapewa kutenga mbali m’ndale ngakhale kuti kucita zimenezo kungacititse kuti akhale ndi ndalama zocepa kapena asakhale ndi ciliconse.—Aheberi 10:34.

12, 13. (a) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu? (b) Tingadziŵe bwanji kuti tayamba kukonda kwambili dziko lathu?

12 Kunyada. Anthu ambili amakonda kunyadila mtundu wao, cikhalidwe, mzinda, kapena dziko lao. Koma Yehova saona kuti munthu wina kapena gulu lina la anthu ndi labwino kuposa lina. Iye amaona kuti tonse ndife ofanana. Yehova anapanga anthu a mitundu yosiyanasiyana, ndipo zimenezi n’zabwino ndiponso zokondweletsa. Iye amafuna kuti tizikonda cikhalidwe cathu ndi kusangalala naco. Koma amafunanso kuti tisamadzione kukhala apamwamba kwambili kuposa ena.—Aroma 10:12.

13 Sitiyenela kukonda kwambili dziko lathu kapena mtundu wathu n’kumaona kuti maiko ena ndi mitundu ina si zabwino kwenikweni. Ngati timadziona mwanjila imeneyi, zingakhale zovuta kupewa zandale. Izi zinacitikanso m’nthawi ya atumwi. Abale ena aciheberi anacitila akazi amasiye acigiriki zinthu zopanda cilungamo. (Machitidwe 6:1) Kodi tingadziŵe bwanji kuti tayamba kukhala ndi mzimu wonyada? Ngati m’bale kapena mlongo wocokela dela lina wapeleka lingalilo, kodi mumakana ndi kunena kuti, ‘Ife kuno timacita bwino kwambili kuposa kwanu?’ Ngati mumatelo, kumbukilani malangizo ofunika kwambili akuti tiyenela kukhala ‘odzicepetsa, ndi kuona ena kukhala otiposa.’—Afilipi 2:3.

YEHOVA ADZAKUTHANDIZANI

14. Kodi pemphelo lingatithandize bwanji? Nanga m’Baibulo muli citsanzo cotani coonetsa kuti zimenezi n’zoona?

14 Cinthu cacitatu cimene cingatithandize kupewa zandale, ndi kudalila Yehova. Tiyenela kupemphela kuti iye atipatse mzimu woyela, umene ungatithandize kukhala oleza mtima ndi odziletsa. Makhalidwe amenewa adzakuthandizani ngati boma lacita zinthu zacinyengo kapena zopanda cilungamo. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kudziŵa zocitika zimene zingapangitse kuti cikhale covuta kupewa zandale. M’pempheni kuti akuthandizeni kucita zinthu zoyenela pa zocitika zotelo. (Yakobo 1:5) Mungaikidwe m’ndende kapena kulangidwa m’njila inayake cifukwa cokhala wokhulupilika kwa Yehova. Ngati zimenezi zakucitikilani, pemphani Mulungu kuti akuthandizeni kukhala olimba mtima ndi kuuza ena momveka bwino cifukwa cake simutenga mbali m’ndale. Musakaikile kuti Yehova adzakuthandizani kupilila.—Ŵelengani Machitidwe 4:27-31.

Phunzilani Malemba amene adzakuthandizani kukana kutenga mbali m’ndale ndiponso amene amakamba za madalitso a m’dziko latsopano

15. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kupewa kutenga mbali m’ndale? (Onaninso bokosi lakuti “Mau a Mulungu Anawathandiza Kuti Asatenge Mbali m’Ndale.”)

15 Yehova watipatsa Baibulo kuti lizitilimbikitsa. Muziganizila Malemba amene adzakuthandizani kupewa kutenga mbali m’zandale. Yesetsani kuphunzila Malemba amenewa kuti muziwakumbukila, cifukwa cakuti adzakuthandizani panthawi imene simudzakhala ndi Baibulo. Komanso Baibulo lingakuthandizeni kukhala ndi ciyembekezo camphamvu pa malonjezo a Mulungu. Ciyembekezo camphamvu n’cofunika kwambili kuti tipilile cizunzo. (Aroma 8:25) Sankhani Malemba amene amakamba zinthu zimene mumalakalaka kudzasangalala nazo m’dziko latsopano, ndipo muziyelekezela kuti muli kale m’menemo.

TENGELANI PHUNZILO PA ZITSANZO ZA ATUMIKI A YEHOVA OKHULUPILIKA

16, 17. Tingaphunzile ciani kwa atumiki a Mulungu okhulupilika amene sanatenge mbali m’ndale? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

16 Cinthu cacinai cimene cingatithandize kuti tisatenge mbali m’ndale ndi kuganizila zitsanzo za atumiki a Yehova okhulupilika. Kale, atumiki a Mulungu ambili anali olimba mtima, ndipo anapanga zosankha zanzelu zimene zinawathandiza kuti asatenge mbali m’zandale. Ganizilani za Sadirake, Mesake ndi Abedinego, amene anakana kulambila fano loimila boma la Babulo. (Ŵelengani Danieli 3:16-18.) Nkhani ya m’Baibulo imeneyi, yathandiza abale ndi alongo ambili masiku ano kukhala olimba mtima ndi kukana kulambila mbendela ya dziko lao. Yesu sanatengeko mbali m’mikangano ya ndale imene imagaŵanitsa anthu. Iye anadziŵa kuti citsanzo cake cabwino cidzathandiza ophunzila ake. Yesu anati: “Limbani mtima. Ndaligonjetsa dziko ine.”—Yohane 16:33.

17 Abale ndi alongo ambili anakhalabe okhulupilika pamene anali kuyesedwa kuti atengeko mbali m’ndale. Ena mwa io akhala akuzunzidwa, kuikidwa m’ndende, kapena kuphedwa kumene cifukwa cokhala okhulupilika kwa Yehova. Zitsanzo zao zingatithandize kukhala olimba mtima. M’bale wina wa ku Turkey anati: “Franz Reiter anali m’bale wacinyamata amene anaphedwa cifukwa cokana kuloŵa m’gulu la asilikali a Hitler. Kalata imene analembela amai ake usiku umene anaphedwa, inaonetsa kuti anali ndi cikhulupililo colimba kwambili ndiponso kuti anali kudalila kwambili Yehova. Ine ndimafuna kutengela citsanzo cake ndikadzakumana ndi ciyeso cotelo.”[2]—Onani mau akumapeto.

18, 19. (a) Kodi abale ndi alongo mumpingo wanu angakuthandizeni bwanji kuti musatenge mbali m’ndale? (b) Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciani?

18 Abale ndi alongo mumpingo wanu angakuthandizeni kupewa kutenga mbali m’zandale. Ngati mukukumana ndi ciyeso, fotokozelani akulu. Iwo angakupatseni malangizo abwino ocokela m’Baibulo. Ndiponso ngati ena mumpingo adziŵa za vuto lanu, angakulimbikitseni. Apempheni kuti azikupemphelelani. Koma ifenso tiyenela kuthandiza abale athu ndi kuwapemphelela. (Mateyu 7:12) Kuti mupeze maina a abale amene ali m’ndende, onani nkhani ya pa jw.org ya mutu wakuti, “Mayiko Amene a Mboni za Yehova Akumangidwa Chifukwa Chotsatira Zimene Amakhulupirira,” imene ili m’cigawo cakuti MALO A NKHANI, pitani pa ZOKHUDZANA NDI MALAMULO. Sankhani maina angapo, ndipo pemphani Yehova kuti athandize abale ndi alongo amenewa kukhalabe olimba ndi okhulupilika kwa iye.—Aefeso 6:19, 20.

19 Pamene tikuyandikila mapeto a dzikoli, maboma ambili adzayamba kutikakamiza kutenga mbali m’zandale. Ndiye cifukwa cake tifunika kukonzekela kuti tidzapewe kutenga mbali m’ndale za dziko losagwilizanali.

^ [1] (ndime 1) Yesu anali kutanthauza boma pamene anakamba kuti Kaisara. Panthawiyo, Kaisara anali wolamulila ndipo ndiye anali ndi udindo wapamwamba kwambili kuposa onse.

^ [2] (ndime 17) Onani buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 662, ndi bokosi lakuti “Anafa Cifukwa Copeleka Ulemelelo kwa Mulungu” limene lili patsamba 150 m’buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulila.

Mau a Mulungu Anawathandiza Kuti Asatenge Mbali m’Ndale

“Kuganizila kwambili lemba la Miyambo 27:11, Mateyu 26:52, ndi la Yohane 13:35 kunandilimbikitsa kukana kuloŵa usilikali. Malemba amenewa anandithandizanso kukhala wodekha pamene anali kundiimba mlandu.”—Andriy, wa ku Ukraine.

“Lemba la Yesaya 2:4 linandithandiza kusatenga mbali m’ndale pamene ndinali kuyesedwa. Ndinali kuganizila za umoyo wamtendele umene tidzakhala nao m’paladaiso, pamene anthu sadzanyamulanso zida kuti aphe anzao.”—Wilmer, wa ku Colombia.

KUFOTOKOZA MAU ENA

  • Sititenga mbali pa zocitika za m’dzikoli: Sititenga mbali m’zandale kapena m’nkhondo cifukwa cakuti ndife okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani