LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Muziwathandiza Alongo Mumpingo
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2020 | September
    • Yesu wakhala pansi pamene akuphunzitsa anthu. Marita na Mariya akhala pansi pafupi na Yesu ndipo akumumvetsela. Zithunzi: 1. Banja lapita kukacezela mlongo wodwala wacikulile ku nyumba kwake. Mwamuna akukamba na mlongo wacikulile wodwalayo pamene mkazi wake akuika zinthu zimene amubweletsela. 2. M’bale wina na mkazi wake akucita kulambila kwa pabanja pamodzi na mlongo wina na mwana wake wamng’ono. 3. M’bale akuthandiza alongo aŵili kusintha wilo ku motoka yawo.

      Mofanana na Yesu, timawadela nkhawa mwacikondi alongo athu okhulupilika (Onani ndime 6-9)e

      6. Kodi lemba la Luka 10:38-42, lionetsa kuti Yesu anathandiza bwanji Marita na Mariya?

      6 Yesu anali kupatula nthawi yoceza na alongo ake auzimu, ndipo anali bwenzi labwino kwa iwo. Ganizilani ubwenzi umene unalipo pakati pa iye na Mariya komanso Marita, alongo amene mwacidziŵikile anali osakwatiwa. (Ŵelengani Luka 10:38-42.) N’zoonekelatu kuti mwa zokamba na zocita zake, Yesu anapangitsa alongowo kukhala omasuka. Mwacitsanzo, Mariya anamasuka kukhala pansi pafupi na iye monga wophunzila wake.c Nayenso Marita ataona kuti Mariya sakumuthandiza nchito, anamasuka kuuza Yesu dandaulo lake. Panthawi ya maceza imeneyo, Yesu anaphunzitsa azimayi aŵiliwa mfundo zofunika zauzimu. Ndipo iye anaonetsa kuti anali kuwakonda azimayiwa pamodzi na mlongo wawo Lazaro, mwa kupita kukawacezela pa nthawi zina. (Yoh. 12:1-3) Conco, n’zosadabwitsa kuti Lazaro atadwala kwambili, Mariya na Marita anamasuka kupempha thandizo kwa Yesu.—Yoh. 11:3, 5.

  • Muziwathandiza Alongo Mumpingo
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2020 | September
    • c Buku lina limati: “Ophunzila anali kukhala pafupi na mphunzitsi wawo. Ophunzila akhama, anali kukonzekela kuti akaphunzila akakhale aphunzitsi—nchito imene akazi sanali kuloledwa kugwila. . . . Conco amuna ambili aciyuda akanadabwa kuona Mariya atakhala pansi pafupi na Yesu ali na mtima wofuna kuphunzitsidwa na iye.”

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani