LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 June tsa. 8
  • Makolo, Thandizani Ana Anu Kuti Apambane

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Makolo, Thandizani Ana Anu Kuti Apambane
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Inu Makolo—Thandizani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 2
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kukonda Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kodi Ana Anu Adzatumikilabe Yehova Akakula?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 June tsa. 8
Yosefe na Mariya akuphunzitsa Yesu ndi ana awo ena panthawi ya kudya

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Makolo, Thandizani Ana Anu Kuti Apambane

Makolo oopa Mulungu amafunitsitsa kuti ana awo ayambe kutumikila Yehova mokhulupilika. Kuti izi zitheke, makolo afunika kukhomeleza mfundo za m’Baibo m’mitima ya ana awo kungoyambila ali akhanda. (Deut. 6:7; Miy. 22:6) Ndithudi, kucita zimenezi kumafuna kudzimana. Ndipo kudzimanako kumakhala na mapindu ambili.—3 Yoh. 4.

Makolo angaphunzile zambili kwa Yosefe na Mariya. Iwo “caka ndi caka . . . anali kukonda kupita ku Yerusalemu, ku cikondwelelo ca Pasika,” olo kuti kucita zimenezi kunali kulila mphamvu na ndalama. (Luka 2:41) Mwacionekele, Yosefe na Mariya anali kuona kuti cofunika kwambili m’banja mwawo ni kuika zinthu zauzimu patsogolo. Mofananamo, makolo masiku ano angatsogolele ana awo pa njila yoyenelela mwa kuwaphunzitsa pa mpata uliwonse umene angapeze mwa zokamba na citsanzo cawo.—Sal. 127:3-5.

KODI MUDZIŴA?

Ngakhale kuti abale ake a Yesu analeledwa m’banja lauzimu, sanali kumukhulupilila Yesu kufikila atamwalila. (Yoh. 7:5; Mac. 1:14) Pambuyo pake, Yakobo na Yuda, abale ake a Yesu, analemba mabuku a m’Baibo odziŵika na maina awo.

TAMBANI VIDIYO YAKUTI SANALEKELELE MWAYI ULIWONSE WA UTUMIKI, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILA:

  • Kodi m’bale Jon na mlongo Sharon Schiller anakwanitsa bwanji kuika zinthu za Ufumu patsogolo polela ana awo?

  • N’cifukwa ciani makolo afunika kuphunzitsa na kulangiza mwana aliyense mogwilizana na mmene alili?

  • Kodi makolo angawakonzekeletse bwanji ana awo kuti asagonje ku zinthu zoyesa cikhulupililo cawo?

  • Ni zida ziti za gulu la Yehova zimene munaseŵenzetsapo pothandiza ana anu kukula mwauzimu?

Banja la m’bale Schiller

Muziika zinthu zauzimu patsogolo m’banja mwanu

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani