-
Mfumu Imveketsa Bwino Mfundo Zokhudza Ufumu wa MulunguUfumu wa Mulungu Ukulamulila
-
-
3, 4. (a) Kodi Yesu wakhala akuphunzitsa bwanji anthu okhulupilika za Ufumu wa Mulungu? (b) Kodi tiphunzila ciani m’nkhani ino?
3 Yesu anakamba mau a pa Yohane 16:12 pausiku wake womaliza padziko lapansi. Kodi zikanatheka bwanji kuti Yesu apitilize kuphunzitsa anthu okhulupilika za Ufumu wa Mulungu pambuyo pa imfa yake? Iye anatsimikizila atumwi ake kuti: “Mzimu wa coonadi, adzakutsogolelani m’coonadi conse.”a (Yoh. 16:13) Mzimu woyela uli ngati munthu wotsogolela amene ndi woleza mtima. Yesu amagwilitsila nchito mzimu kuphunzitsa otsatila ake zinthu zilizonse zimene afunika kudziŵa ponena za Ufumu wa Mulungu panthawi yoyenela.
-
-
Mfumu Imveketsa Bwino Mfundo Zokhudza Ufumu wa MulunguUfumu wa Mulungu Ukulamulila
-
-
a Buku lina limanena kuti liu Lacigiriki limene analimasulila kuti ‘kutsogolela’ pa vesili limatanthauza “kusonyeza njila.”
-