LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kodi Uthenga Wabwino Umalalikidwa Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 6. Timamvela lamulo la Mulungu lakuti tizilalikila

      Pa nthawi ya Akhristu oyambilila, adani a Yesu anayesa kuletsa otsatila ake kulalikila. Koma Akhristu oyambililawo anateteza ufulu wawo wolalikila mwa kutsimikizila kuti nchito yawo yolalikila niyololeka mwalamulo. (Afilipi 1:7) Masiku anonso Mboni za Yehova zimacita cimodzi-modzi.a

      Tambani VIDIYO.

      VIDIYO: Kukhalila Kumbuyo Uthenga Wabwino Mwalamulo (2:28)

      Ŵelengani Machitidwe 5:27-42, na kukambilana funso ili:

      • N’cifukwa ciyani sitingaleke kulalikila?—Onani mavesi 29, 38, komanso 39.

  • Tanthauzo Lake la Kusakhalila Mbali
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • Tanthauzo la Kusakhalila Mbali

      Yesu anaphunzitsa otsatila ake kuti sayenela kukhala “mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19) Izi zikutanthauza kusakhalila mbali m’ndale za dziko kapena pankhondo. Kunena zoona, nthawi zina si cinthu capafupi kusakhalila mbali. Zili conco cifukwa anthu ena amatinyodola cifukwa ca kutelo. Koma kodi tingacite bwanji kuti tisamakhalile mbali, komano n’kukhala wokhulupilikabe kwa Yehova Mulungu?

      1. Kodi Akhristu oona amaaona motani maboma a anthu?

      Akhristu amalemekeza boma. Timacita zimene Yesu ananena kuti: “Pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara.” Mwa ici, timamvela malamulo a boma monga a kukhoma misonkho. (Maliko 12:17) Baibo imatiuza kuti maboma a anthu alipo cabe cifukwa Yehova anawalola kulamulila. (Aroma 13:1) Conco, timadziŵa kuti maboma a anthu ali na ulamulilo inde, koma ulamulilo wawo ni wocepelapo. Ciyembekezo cathu maka-maka cagona mwa Mulungu amene adzacotsapo mavuto onse a anthu kupyolela mu Ufumu wake wakumwamba.

      2. Kodi tingaonetse bwanji kuti sitimakhalila mbali?

      Potengela citsanzo ca Yesu, ifenso sitiyenela kutengako mbali m’ndale za dziko. Anthu ataona kuti Yesu wacita cozizwitsa, anayesa kumulonga ufumu padziko lapansi, koma iye sanalole zimenezo. (Yohane 6:15) Cifukwa ciyani? Iye anakamba kuti, “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Pokhala otsatila a Yesu, ifenso sitikhalila mbali m’njila iliyonse. Mwacitsanzo, sitipita ku nkhondo. (Ŵelengani Mika 4:3.) Inde, zizindikilo za maiko monga mbendela timazilemekeza. Ngakhale n’telo, sitizipangila saliyuti cifukwa n’cimodzi-modzi na kuzilambila. (1 Yohane 5:21) Ndipo tikabwela ku nkhani zandale, sitikhalila mbali cipani ciliconse, kapena aliyense woimilila pa masankho. Mwa njila zimenezi komanso zina, timaonetsa kuti ndife wokhulupilika kwathunthu ku boma la Mulungu—Ufumu wake.

      KUMBANI MOZAMILAPO

      Onani zocitika zimene zingatiike pa mayeso pankhani ya kusakhalila mbali na mmene mungapangile zisankho zokondweletsa Yehova.

      Mwamunayu sakufuna kukhalila mbali. Iye sakumvetsela kwa andale opikisana polankhula ku magulu a anthu.

      3. Akhristu oona sakhalila mbali m’nkhani za dziko

      Yesu Khristu pamodzi na otsatila ake anatisiila citsanzo cabwino kwambili. Ŵelengani Aroma 13:1, 5-7, komanso 1 Petulo 2:13, 14. Pambuyo pake, tambani VIDIYO na kukambilana mafunso otsatila.

      VIDIYO: Akhristu Oona Satengela Mbali—Mbali 1 (4:28)

      • N’cifukwa ciyani maboma a anthu tiyenela kuwalemekeza?

      • Ndipo tingaonetse kuwamvela m’njila ziti?

      Pa nthawi ya nkhondo, maiko ena anganene kuti sakhalila mbali, koma kuseli amakhala akuthandizila maiko amene akumenyana. Kodi kusakhalila mbali kwazoona n’kotani? Ŵelengani Yohane 17:16. Pambuyo pake, tambani VIDIYO na kukambilana funso lotsatila.

      VIDIYO: Akhristu Oona Satengela Mbali —Mbali 2 (3:11)

      • Kodi kusakhalila mbali kumatanthauza ciyani?

      Bwanji ngati olamulila a dziko atiuza kucita cinthu cina cosemphana na lamulo la Mulungu? Ŵelengani Machitidwe 5:28, 29. Pambuyo pake, tambani VIDIYO na kukambilana mafunso otsatila.

      VIDIYO: Akhristu Oona Satengela Mbali —Mbali 3 (1:18)

      • Pakakhala kuwombana pakati pa lamulo la anthu na lamulo la Mulungu, kodi tiyenela kumvela lamulo la ndani?

      • Kodi mungaganizileko zocitika zilizonse pamene Akhristu sayenela kumvela maboma a anthu?

      4. Musamakhalile mbali m’maganizo komanso m’zocita

      Ŵelengani 1 Yohane 5:21. Pambuyo pake, tambani VIDIYO na kukambilana mafunso otsatila.

      VIDIYO: Cimene Akhristu Oona Afunikila Kukhala Olimba Mtima—Kuti Asamatengeko Mbali M’zandale (2:49)

      • Mu vidiyo imeneyi, n’cifukwa ciyani Ayenge sanaloŵeko cipani ca ndale, kapena kucitako mwambo wokweza dziko lake, monga kucitako mwambo wotamanda mbendela?

      • Kodi muganiza kuti iye anapanga cisankho canzelu?

      Ni zocitika zina ziti zingakuikeni pa mayeso pankhani ya kusakhalila mbali? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

      VIDIYO: Zimene Tingaphunzile mu Nsanja ya Mlonda—Pewani Kutengako Mbali m’Ndale za Dziko Loipali (5:16)

      • Kodi tingapewe bwanji kukhalila mbali pamene maiko akupikisana pa zocitika za maseŵelo?

      • Kodi tingapewe bwanji kukhalila mbali pamene anthu andale apanga zigamulo zimene ifenso zimatikhudza?

      • Tikapanda kusamala, kodi tingayambe bwanji kukhalila mbali cifukwa ca nkhani za panyuzi kapena anthu amene timaceza nawo?

      Zithunzi: 1. Gulu la anthu okwiya atanyamula zizindikilo pocita cionetselo. 2. Mwamuna uyu wanyamula mbendela, akusangalala pacocitika ca maseŵelo. 3. Mwana wa sukulu akukamba mawu olumbilila kukhulupilika ku dziko lake. 4. Msilikali wanyamula mfuti. 5. Andale aŵili ali pa msutsano. 6. Mzimayi akuponya voti yake m’bokosi yovotela.

      Kodi Mkhristu ayenela kupewa kukhalila mbali pa nkhani ziti m’maganizo komanso m’zocita zake?

      MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “N’cifukwa ciyani simucitako mwambo wotamanda mbendela kapena kuimbako nyimbo ya fuko?”

      • Kodi inu mungayankhe bwanji?

      CIDULE CAKE

      Akhristu amayesetsa kusakhalila mbali pankhani zandale m’maganizo mwawo, m’zokamba zawo, ngakhalenso m’zocita zawo.

      Mafunso Obweleza

      • Kodi tiyenela kucita motani ku maboma a anthu?

      • N’cifukwa ciyani tiyenela kupewelatu kukhalila mbali m’nkhani zandale?

      • Kodi n’zocitika ziti zingatiike pamayeso pa nkhani ya kusakhalila mbali?

      Colinga

      FUFUZANI

      Kodi tingafunike kudzimana zinthu zotani kuti tipewe kukhalila mbali?

      Yehova Sanatigwilitsepo Mwala (3:14)

      Kodi mabanja angakonzekele bwanji mayeso pankhani ya kusakhalila mbali?

      Kusatenga Mbali M’zandale pa Miyambo na Zikondwelelo za Dziko (4:25)

      N’cifukwa ciyani kuteteza dziko lanu sindiwo ulemu wopambana umene munthu angalandile?

      “Zinthu Zonse N’zotheka ndi Mulungu” (5:19)

      Pa nkhani yosankha nchito, ganizilani mmene mungapewele kukhala mbali ya dziko.

      “Yense Adzasenza Katundu Wake wa Iye Mwini” (Nsanja ya Olonda, March 15, 2006)

  • Mukhoza Kupilila Pamene Mukuzunzidwa
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 5. Pitilizani kulambila Yehova pamene mukuzunzidwa

      Pamafunika kulimba mtima kuti titumikile Yehova pamene ena akutiletsa kutelo. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

      VIDIYO: Kulimba Mtima pa Nthawi ya Cizunzo (6:27)

      • Mu zitsanzo za mu vidiyo imeneyi, kodi cakulimbikitsani n’ciyani?

      Ŵelengani Machitidwe 5:27-29, komanso Aheberi 10:24, 25. Pambuyo poŵelenga lililonse la malembawa, kambilanani funso ili:

      • N’cifukwa ciyani sitiyenela kuleka kulambila Yehova, ngakhale pamene boma laletsa nchito yathu yolalikila, kapena kusonkhana kwathu?

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani