-
Gubuduzani Maganizo Aliwonse Otsutsana ndi Kudziŵa Mulungu!Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2019 | June
-
-
1. Ni cenjezo lotani limene mtumwi Paulo anapeleka kwa Akhristu odzozedwa?
MTUMWI Paulo anacenjeza Akhristu a m’nthawi yake kuti: “Musamatengele nzelu za nthawi ino.” (Aroma 12:2) N’cifukwa ciani Paulo anapeleka cenjezo limeneli kwa anthu amene anali kale Akhristu odzipeleka kwa Mulungu komanso odzozedwa na mzimu woyela?—Aroma 1:7.
2-3. Kodi Satana amacita ciani pofuna kuwononga ubwenzi wathu na Yehova? Nanga tingathetse bwanji maganizo oipa amene ‘anazikika molimba’ mu mtima mwathu?
2 Paulo anali kuwadela nkhawa Akhristuwo cifukwa zioneka kuti ena mwa iwo anali atayamba kuyendela maganizo na nzelu za m’dziko la Satana. (Aef. 4:17-19) Zaconco zingacitikilenso aliyense wa ife masiku ano. Satana, amene ni mulungu wa nthawi ino, amaseŵenzetsa misampha yosiyana-siyana kuti awononge ubale wathu na Yehova. Mwacitsanzo, ngati tili na mtima wodzikuza kapena wofuna kuchuka, iye angatengelepo mwayi kuti atipangitse kusokoneza ubwenzi wathu na Yehova. Satana angaseŵenzetsanso zinthu zina zimene tinaphunzila pa nyumba, ku sukulu, kapena kwa anthu okhala nawo pafupi, pofuna kutipangitsa kutengela maganizo ake.
-
-
Gubuduzani Maganizo Aliwonse Otsutsana ndi Kudziŵa Mulungu!Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2019 | June
-
-
“KUSINTHA MAGANIZO ANU”
4. Ni masinthidwe otani amene ambili a ife tinapanga pamene tinayamba kuphunzila coonadi?
4 Kodi n’zinthu ziti zimene munasintha mu umoyo wanu pamene munayamba kuphunzila coonadi ca m’Baibo na kutumikila Yehova? Mosakayikila, ambili a ife tinaleka makhalidwe oipa. (1 Akor. 6:9-11) Ndipo timayamikila kwambili kuti Yehova anatithandiza kucita zimenezi.
5. N’zinthu ziŵili ziti zochulidwa pa Aroma 12:2 zimene tiyenela kucita?
5 Koma tifunika kukhalabe osamala. Olo kuti tinaleka kucita macimo akulu-akulu amene tinali kucita tisanabatizike, tiyenela kuyesetsa kupewa ciliconse cimene cingatisonkhezele kuyambanso makhalidwe amenewo. Kodi tingacite bwanji zimenezi? Paulo anati: “Musamatengele nzelu za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu.” (Aroma 12:2) Conco, pali zinthu ziŵili zimene tiyenela kucita. Coyamba, tifunika kupewa ‘kutengela’ nzelu za dzikoli. Caciŵili, tifunika ‘kusandulika’ mwa kusintha maganizo athu.
6. Kodi tiphunzilapo ciani pa mawu amene Yesu anakamba pa Mateyu 12:43-45?
6 Kusandulika kumene Paulo anakamba kumatanthauza zambili, osati kusintha cabe maonekedwe athu. Kumatanthauza kusintha mbali iliyonse ya umoyo wathu. (Onani bokosi yakuti “Kusandulika Kapena Ciphamaso Cabe?”) Tifunika kusandulika kothelatu, kutathauza kusintha zimene timaganiza mkatikati mwa mtima wathu, zolinga zathu, na zolakalaka zathu. Conco, aliyense wa ife afunika kudzifunsa kuti, ‘Kodi masinthidwe amene nikupanga mu umoyo wanga wacikhristu ni aciphamaso, kapena ni ocokeladi pansi pa mtima?’ Funso limeneli n’lofunika kwamibili. Mawu a Yesu pa Mateyu 12:43-45, amatithandiza kuona zimene tiyenela kucita kuti tisandulike. (Ŵelengani.) Zimene Yesu anakamba pa lembali zimatiphunzitsa mfundo yofunika kwambili yakuti: Kucotsa maganizo oipa mu mtima mwathu sikokwanila. Koma tifunikanso kuloŵetsamo maganizo abwino amene amakondweletsa Mulungu.
-