-
Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Umbeta na Ukwati?Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
5. Sankhani mwanzelu munthu wokwatilana naye
Kusankha munthu womanga naye banja ni nkhani yaikulu kwambili. Ŵelengani Mateyu 19:4-6, 9, na kukambilana funso ili:
N’cifukwa ciyani Mkhristu sayenela kuthamangila kuloŵa m’banja?
Baibo ingakuthandizeni kudziŵa makhalidwe abwino a munthu amene mungakwatilane naye. Koma cofunika kwambili ni kupeza munthu amene amakonda Yehova.b Ŵelengani 1 Akorinto 7:39 na 2 Akorinto 6:14. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:
N’cifukwa ciyani tiyenela kukwatilana na Mkhristu mnzathu cabe?
Kodi muganiza kuti Yehova angamve bwanji tikakwatilana na munthu amene sakonda Mulungu?
Mukamanga mujoko nyama ziŵili zosiyana kwambili, zonse zidzavutika. Mofananamo Mkhristu akamanga ukwati na munthu wosakhulupilila, adzakhala na mavuto ambili
-