LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
    • 6. (a) Malinga ndi mau a Paulo, n’cifukwa ciani nchito yopeleka thandizo ndi mbali ya kulambila kwathu? (b) Fotokozani mmene nchito yathu yopeleka thandizo imacitikila padziko lonse masiku ano. (Onani chati cakuti “Pakacitika Ngozi,” patsamba 214.)

      6 Paulo anathandiza Akristu a ku Korinto kuzindikila kuti nchito yopeleka thandizo ndi mbali ya kulambila Yehova, ndiponso kuti ndi mbali ya utumiki wao kwa Iye. Onani kuti iye anakamba kuti Akristu amene amapeleka thandizo amacita zimenezo cifukwa ‘cogonjela uthenga wabwino wonena za Kristu.” (2 Akor. 9:13) Conco, cimene cimalimbikitsa Akristu kuthandiza anzao ndi mtima wao wofuna kutsatila zimene Kristu anaphunzitsa. Paulo ananena kuti zinthu zabwino zimene Akristu amacitila abale ao zimaonetsa “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (2 Akor. 9:14; 1 Pet. 4:10) Conco, ponena za nchito yothandiza abale athu amene akuvutika, magazini ya Nsanja ya Olonda ya December 1, 1975 inati: “Tisakaikile kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Kristu amaona utumikiwu kukhala wofunika kwambili.” Zoonadi, nchito yopeleka thandizo ndi mbali yofunika kwambili ya utumiki wopatulika.—Aroma 12:1, 7; 2 Akor. 8:7; Aheb. 13:16.

  • Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
    • 7, 8. Kodi colinga coyamba ca utumiki wathu wopeleka thandizo n’ciani? Fotokozani.

      7 Kodi colinga ca utumiki wathu wopeleka thandizo pa nthawi yamavuto n’ciani? Paulo anayankha funso limenelo m’kalata yake yaciŵili yopita kwa Akorinto. (Ŵelengani 2 Akorinto 9:11-15.) Palembali, Paulo anafotokoza zolinga zitatu zimene timakwanilitsa tikamacita “utumiki wothandiza anthu” panthawi ya mavuto. Tiyeni tikambilane zolinga zimenezi.

      8 Coyamba, utumiki umenewu umalemekeza Yehova. Onani kuti pa mavesi asanu a pa 2 Akorinto 9:11-15, Paulo anagwilitsila nchito mau angapo othandiza abale kuona mmene utumiki wopeleka thandizo umakhudzila Yehova Mulungu. Iye anawakumbutsa kuti utumikiwu umacititsa “anthu kuyamika Mulunguyo” ndiponso “kupeleka mapemphelo oculuka oyamika Mulungu.” (vesi 11 ndi 12) Anafotokozanso kuti nchito yopeleka thandizo imalimbikitsa Akristu ‘kulemekeza Mulungu’ ndi kuyamikila ‘kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.’ (vesi 13 ndi 14) Ndiyeno Paulo anamaliza nkhani yake yonena za kupeleka thandizo ndi mau akuti: “Tikuyamika Mulungu.”—Vesi 15; 1 Pet. 4:11.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani