-
Kodi Mukuyesetsa Kufika pa Ucikulile Umene Kristu Anafikapo?Nsanja ya Mlonda—2015 | September 15
-
-
2 Munthu akaphunzila za Yehova ndi kubatizidwa, amapitiliza kukulitsa ubwenzi wake ndi Mulungu. Colinga cake n’cakuti akhale Mkristu wokhwima. Kukhwima kumeneku sikutanthauza kukula kwa kuthupi. Koma kumatanthauza kukhwima kuuzimu ndi kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova. Mtumwi Paulo anafuna kuti Akristu a ku Efeso akhale ofikapo kuuzimu. Iye anawalimbikitsa kukhala ogwilizana m’cikhulupililo ndi kupitiliza kuphunzila za Kristu kuti akhale ‘anthu acikulile, ofika pa msinkhu waucikulile umene Kristu anafikapo.’—Aefeso 4:13.
3. Kodi mpingo wa ku Efeso umafanana bwanji ndi atumiki a Yehova masiku ano?
3 Mpingo wa ku Efeso utakhazikitsidwa, mtumwi Paulo analembela kalata Akristu a kumeneko. Ambili mumpingowo anatumikila kwa nthawi yaitali, ndipo anali Akristu ofikapo kuuzimu. Komabe, panali ena amene anali kufunika kulimbitsa ubwenzi wao ndi Yehova. Mofananamo, masiku ano abale ndi alongo ambili atumikila Yehova kwa nthawi yaitali, ndipo ndi Akristu ofikapo kuuzimu. Ngakhale n’conco, pali ena amene akalibe kufikapo kuuzimu. Mwacitsanzo, anthu masauzande amabatizidwa caka ciliconse. Iwo afunikilabe kufikapo kuuzimu. Nanga bwanji za inu?—Akolose 2:6, 7.
-
-
Kodi Mukuyesetsa Kufika pa Ucikulile Umene Kristu Anafikapo?Nsanja ya Mlonda—2015 | September 15
-
-
5 Mkristu wofikapo amatsatila ‘mapazi a Yesu mosamala kwambili.’ (1 Petulo 2:21) Yesu anakamba kuti munthu ayenela kukonda Yehova ndi mtima wake wonse, moyo wake wonse, ndi maganizo ake onse. Ndipo ayenelanso kukonda mnzake mmene amadzikondela yekha. (Mateyu 22:37-39) Mkristu wofikapo amayesetsa kumvela malangizo amenewo. Mmene amakhalila umoyo wake zimaonetsa kuti ubwenzi wake ndi Yehova, ndiponso kukonda ena, ndi zofunika kwambili kwa iye.
-