-
Gubuduzani Maganizo Aliwonse Otsutsana ndi Kudziŵa Mulungu!Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2019 | June
-
-
“MUKHALE ATSOPANO MU MPHAMVU YOYENDETSA MAGANIZO ANU”
7. Tingacite ciani kuti tisinthe umunthu wathu wamkati?
7 Kodi n’zotheka kusintha umunthu wathu wamkati kapena mphamvu yoyendetsa maganizo athu? Mawu a Mulungu amati: “Munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu ndipo umatsatila zofunika pa cilungamo ceniceni ndi pa kukhulupilika.” (Aef. 4:23, 24) Conco, n’zotheka kusintha umunthu wathu wamkati. Koma pamafunika khama. Tiyenela kuyesetsa kupondeleza zilakolako zoipa na kupewa makhalidwe oipa. Koma tiyenela kucita zoposa pamenepo. Tiyenelanso kusintha “mphamvu yoyendetsa maganizo” athu. Kucita izi kumaphatikizapo kusintha zolakalaka zathu, zizoloŵezi, na zolinga zathu. Kuti izi zitheke, timafunika kucita khama nthawi zonse.
8-9. Kodi citsanzo ca m’bale wina cionetsa bwanji kufunika kosintha umunthu wathu wamkati?
8 Ganizilani za m’bale wina amene anali wa ndewu asanakhale Mboni. Ataleka ndewu na kumwa moŵa, anabatizika. Zimenezi zinapeleka umboni wabwino kwa anthu a m’dela limene iye anali kukhala. Atangobatizika kumene, tsiku lina madzulo anakumana na ciyeso. Munthu wina wokolewa anafika ku nyumba kwa m’baleyo na kumuwopseza kuti amumenya. Poyamba, m’baleyo anayesetsa kuugwila mtima. Koma pamene mwamunayo anakamba mawu onyoza dzina la Yehova, m’baleyo anakwiya kwambili. Iye anatuluka m’nyumba na kumenya mwamunayo. Kodi m’baleyu anali na vuto lanji? Ngakhale kuti kuphunzila Baibo kunamuthandiza kuti aleke kukonda ndewu, m’baleyu anali asanasinthe mphamvu yoyendetsa maganizo ake. M’mawu ena, tingakambe kuti iye anali asanasinthe umunthu wake wamkati.
9 Koma m’baleyo sanabwelele m’mbuyo. (Miy. 24:16) Mothandizidwa na akulu, anapitiliza kukula mwauzimu. Ndipo m’kupita kwa nthawi, anakhala mkulu. Patapita zaka, iye anakumananso na ciyeso cina cofanana ndi ca poyamba cija. Tsiku lina madzulo ali pa Nyumba ya Ufumu, kunabwela munthu wina wokolewa amene anafuna kumenya mmodzi wa akulu. Kodi m’baleyo anacita ciani? Modekha komanso modzicepetsa, anakambilana na munthu wokolewayo na kum’pelekeza ku nyumba kwake. N’ciani cinathandiza m’baleyo kucita zinthu mosiyana na mmene anacitila poyamba paja? Iye anali atasintha mphamvu yoyendetsa maganizo ake. Anali atasintha umunthu wake wamkati na kukhala munthu wamtendele ndiponso wodzicepetsa. Izi zinacititsa kuti Yehova atamandike.
10. Kodi tifunika kucita ciani kuti tisinthe umunthu wathu wamkati?
10 Kusintha kumeneku sikucitika tsiku limodzi, ndipo kumafuna khama. Tingafunike ‘kuyesetsa mwakhama’ kwa zaka zambili kuti tisinthe. (2 Pet. 1:5) Kungokhala “m’coonadi” kwa nthawi yaitali, pakokha sikokwanila. Timafunika kucita zonse zimene tingathe kuti tisinthe umunthu wathu. Lomba tiyeni tikambilane zinthu zingapo zofunika kwambili zimene zingatithandize kupanga masinthidwe amenewa.
ZIMENE TINGACITE KUTI TISINTHE MPHAMVU YOYENDETSA MAGANIZO ATHU
11. Kodi pemphelo limatithandiza bwanji kusintha mphamvu yoyendetsa maganizo athu?
11 Cinthu coyamba cofunika kwambili cimene tiyenela kucita ni kupemphela. Tifunika kupemphela monga mmene wamasalimo anacitila. Iye anati: “Lengani mtima wolungama mkati mwanga, ndipo ikani maganizo atsopano ndi okhazikika mwa ine.” (Sal. 51:10) Tiyenela kuzindikila kuti tifunika kusintha mphamvu yoyendetsa maganizo athu na kupempha Yehova kuti atithandize. N’cifukwa ciani ndife otsimikiza kuti Yehova angatithandize kusintha? Ganizilani zimene Yehova anakamba ponena za Aisiraeli ouma mtima a m’nthawi ya Ezekieli. Iye anati: “Ndidzawapatsa mtima umodzi ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa iwo . . . n’kuwapatsa mtima wamnofu,” [kutanthauza mtima womvela Mulungu.] (Ezek. 11:19) Yehova anali wokonzeka kuthandiza Aisiraeli ouma mtimawo kusintha. Ndipo ni wokonzekanso kutithandiza.
12-13. (a) Malinga na Salimo 119:59, kodi tiyenela kusinkha-sinkha za ciani? (b) Nanga tiyenela kudzifunsa mafunso ati?
12 Cinthu caciŵili cofunika kwambili ni kusinkha-sinkha. Pamene tiŵelenga mosamala Mawu a Mulungu tsiku lililonse, tiyenela kupatula nthawi yosinkha-sinkha, kapena kuti kuganizila mozama pa zimene tawelengazo, n’colinga cakuti tizindikile maganizo oipa na zilakolako zosayenela zimene tifunika kusintha. (Ŵelengani Salimo 119:59; Aheb. 4:12; Yak. 1:25) Tiyenela kudzipenda kuti tione ngati tayamba kutengeka na nzelu za dzikoli. Tiyenelanso kuvomeleza modzicepetsa zofooka zathu na kugwililapo nchito zolimba kuti tiwongolele.
13 Mwacitsanzo, dzifunseni kuti: ‘Kodi niliko na kamtima ka nsanje kapena kaduka? (1 Pet. 2:1) ‘Kodi nimadziona kuti ndine wapamwamba kuposa ena cifukwa ca maphunzilo amene n’nacita, cuma cimene nili naco, kapena cifukwa ca kumene n’nakulila?’ (Miy. 16:5) ‘Kodi nimaona ena kukhala osanunkha kanthu cifukwa cakuti alibe zinthu zofanana ndi zimene ine nili nazo, kapena cifukwa ni a mtundu wina?’ (Yak. 2:2-4) ‘Kodi nimakopeka na zinthu za m’dziko la Satanali?’ (1 Yoh. 2:15-17) ‘Kodi nimakopeka na zosangalatsa zaciwelewele kapena zaciwawa?’ (Sal. 97:10; 101:3; Amosi 5:15) Kuganizila mafunso amenewa, kudzatithandiza kuzindikila mbali zimene tifunika kugwililapo nchito. Ngati tiyesetsa kuthetsa maganizo oipa amene ‘anazikika molimba’ mumtima mwathu, tidzakondweletsa Atate wathu wakumwamba.—Sal. 19:14.
14. N’cifukwa ciani kusankha mabwenzi abwino n’kofunika kwambili?
14 Kusankha mabwenzi abwino ni mbali yacitatu yofunika kwambili. Mwacibadwa, anthufe timakonda kutengela zocita za anzathu. (Miy. 13:20) Kaya tili ku nchito kapena ku sukulu, nthawi zambili timakhala ndi anthu amene sangatilimbikitse kukhala na maganizo okondweletsa Mulungu. Komabe, tingapeze mabwenzi abwino ku misonkhano yathu. Kumeneko, n’kumene timalimbikitsidwa pa “cikondi ndi nchito zabwino.”—Aheb. 10:24, 25.
-