LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kodi Zikondwelelo Zonse Zimam’sangalatsa Mulungu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • Ŵelengani Aefeso 5:10, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi tiyenela kutsimikizila za ciyani pofuna kupanga cisankho cakuti tikondwelele holide kapena ayi?

      • Kodi kwanuko ni maholide ati amene anthu amakondwelela?

      • Kodi inu muona kuti maholide amenewo amakondweletsa Yehova?

      Mwacitsanzo, kodi munayamba mwaganizapo za mmene Mulungu amaonela masiku a kubadwa? Baibo sichulako wolambila Yehova aliyense amene anakondwelelapo tsiku la kubadwa. Zikondwelelo ziŵili zokha za tsiku la kubadwa zimene limachula zinali za anthu osam’tumikila. Ŵelengani Genesis 40:20-22 na Mateyu 14:6-10. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:

      • Kodi pa zikondwelelo za tsiku la kubadwa ziŵili izi panacitika cinthu cofanana cotani?

      • Malinga na nkhani za m’Baibo zimenezi, kodi muganiza Yehova amakuona bwanji kukondwelela tsiku la kubadwa?

      Komabe mungadzifunse kuti, ‘Kodi zimam’khudza Yehova nikakondwelela tsiku la kubadwa kapena holide iliyonse yosagwilizana na Malemba?’ Ŵelengani Ekisodo 32:1-8. Pambuyo pake, tambani VIDIYO na kukambilana mafunso otsatila.

      VIDIYO: Maholide na Zikondwelelo Zosakondweletsa Mulungu (5:07)

      • N’cifukwa ciyani tiyenela kutsimikizila kuti izi Yehova amazivomeleza?

      • Ndipo tingacite motani zimenezo?

      Mafunso otithandiza kudziŵa ngati cikondwelelo cimasangalatsa Mulungu

      • Kodi cikondwelelo cimeneci n’cozikika mu ziphunzitso zosemphana na Malemba? Fufuzani, pezani kuti cinayambila poti.

      • Kodi cimapeleka ulemu wopambanitsa kwa anthu, ku magulu a anthu kapena ku cizindikilo ca dziko monga mbendela? Ife timalemekeza Yehova kuposa wina aliyense, ndipo timakhulupilila kuti iye adzacotsapo mavuto onse padziko lapansi.

      • Kodi miyambo yake, komanso zocitika zolowetsedwamo, zimasemphana na mfundo za m’Baibo? Tiyenela kukhalabe oyela m’makhalidwe athu.

  • Sankhani Zosangalatsa Zovomelezeka kwa Yehova
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • Phunzilo 53. Tate, mayi, pamodzi na mtsikana wawo akudya mapopukoni pamene akutamba TV.

      PHUNZILO 53

      Sankhani Zosangalatsa Zovomelezeka kwa Yehova

      Yehova ni “Mulungu wacimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Iye amafuna kuti nafenso tizikhala na umoyo wacimwemwe komanso wosangalatsa. Ndipo amakondwela tikamapatula nthawi yakuti tipumuleko. Mu phunzilo lino, tiona mmene tingagwilitsile nchito nthawi yathu yosanguluka m’njila yabwino komanso yovomelezeka kwa Yehova.

      1. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani posankha zosangalatsa?

      Kodi mumakonda kucita ciyani pamene mukupumula? Ena amakonda kungokhala panyumba—akuŵelenga buku, kumvela nyimbo, kutamba filimu, kapena kuyang’ana zinthu pa intaneti. Ena amakonda kucita zinthu pamodzi na anzawo monga—kupita kokayenda, kukanyaya, kapena kucita maseŵelo. Ciliconse cimene cingakhale makonda athu, tiyeni tionetsetse kuti tikusankha zosangalatsa ‘zovomelezeka kwa Ambuye.’ (Aefeso 5:10) M’pofunika kuimvetsetsa mfundo imeneyi, cifukwa m’zosangalatsa zambili masiku ano, mumakhalanso zinthu zimene Yehova amadana nazo monga ciwawa, zaciwelewele, kapena zamizimu. (Ŵelengani Salimo 11:5.) Kodi n’ciyani cingatithandize kupanga zisankho zanzelu pa nkhani ya zosangalatsa?

      Tikasankha mabwenzi okonda Yehova, angatithandize kwambili posankha zosangalatsa. Monga tinaonela m’Phunzilo 48, “munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.” Koma ngati timakonda kuceza na anthu amene sakonda malamulo a Mulungu, ‘tidzapeza mavuto.’—Miyambo 13:20.

      2. N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala nayo nthawi imene timathela pa zosangalatsa?

      Ngakhale titasankha zosangalatsa zabwino, tiyenelabe kusamala kuti zisatidyele nthawi yoculuka kwambili. Tikapanda kusamala tidzasoŵa nthawi yocita zinthu zofunika kwambili. Baibo imatilimbikitsa ‘kugwilitsa nchito bwino nthawi yathu.’—Ŵelengani Aefeso 5:15, 16.

      KUMBANI MOZAMILAPO

      Dziŵani mmene mungapangile zisankho zabwino pa nkhani ya zosangalatsa.

      3. Pewani zosangalatsa zoipa

      N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala posankha zosangalatsa? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

      VIDIYO: Kodi Niyenela Kusankha Zosangalatsa Zabwanji? (4:39)

      • Kodi maseŵelo a m’nthawi zamakedzana ofika mpaka kuphana, akufanana bwanji na zosangalatsa zina zamakono?

      • Mu vidiyo imeneyi, kodi Danny anaphunzilapo ciyani pa zosangalatsa?

      Ŵelengani Aroma 12:9, na kukambilana funso ili:

      • Kodi lemba limeneli lingakuthandizeni bwanji posankha zosangalatsa?

      Kodi ni zinthu ziti zimene Yehova amadana nazo? Ŵelengani Miyambo 6:16, 17, komanso Agalatiya 5:19-21. Pambuyo poŵelenga lililonse la malembawa, kambilanani funso ili:

      • Pa zimene zachulidwa pa lembali, ni zinthu ziti zofala m’zosangalatsa za masiku ano?

      Mmene mungasankhile zosangalatsa mwanzelu

      Dzifunseni kuti:

      • Ciphatikizapo ciyani? Kodi m’cosangalatsa cimeneci muli zinthu zimene Yehova amadana nazo?

      • Cimacitika nthawi yanji? Kodi cimabwela pa nthawi yoyenela kucita zinthu zofunika kwambili?

      • Muli anthu otani? Kodi anthu a m’cosangalatsa cimeneco ni osakonda Yehova, amene angakhale mayanjano oipa kwa ine?

      Ni cinthu canzelu kutalikilana naco cinthu coopsa ciliconse. Conco, tiyenelanso kukhala kutali na cosangalatsa ciliconse cimene tikuona kuti sicingakhale cabwino kwa ife

      Motoka ikuyendela m’mphepete mwenimweni mwa msewu wa kumbali kwa phili. Kumbuyo kwake yayamba kale kutsetselekela kuphompho.

      4. Gwilitsani nchito nthawi yanu mwanzelu

      Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

      VIDIYO: N’ciani Cimakulandani Nthawi? (2:45)

      • Ngakhale kuti m’bale wa mu vidiyo iyi sanali kutamba ciliconse coipa, kodi cinayamba kucitika kwa iye n’ciyani cifukwa cosasamala nayo nthawi yopumula?

      Ŵelengani Afilipi 1:10, na kukambilana funso ili:

      • Kodi lembali lingatithandize bwanji kusamala nayo nthawi yocita zosangulutsa?

      5. Sankhani zosangalatsa zoyenela

      Ngakhale kuti zosangalatsa zina sizovomelezeka kwa Yehova, pali zinthu zambili zimene tingacite zosangalatsa. Ŵelengani Mlaliki 8:15, komanso Afilipi 4:8, na kukambilana funso ili:

      • Kodi mungachuleko zosangalatsa zabwino zimene mumakonda?

      Zithunzi: Anthu a misinkhu yosiyana-siyana akusangalala na zosangulutsa zabwino. 1. Mtsikana akumvela nyimbo kwinaku akujambula zithunzi. 2. Anyamata atatu akuseŵela mpila wa manja. 3. Anyamata aŵili akuchova njinga. 4. Wacicepele akupanga motoka yoseŵeletsa. 5. Mwamuna akuimba ng’oma. 6. Mnyamata akucita seŵelo la pavidiyo na atate ake. 7. Mkazi akujambula cithunzi.

      Zilipo zosangalatsa komanso zosangulutsa zabwino

      ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Palibe vuto kutamba zosangalatsa mmene muli zaciwawa, zaciwelewele, kapena zamizimu, malinga inu simucitako zinthu zimenezo.”

      • Nanga inu muganiza bwanji?

      CIDULE CAKE

      Yehova amafuna kuti tizisankha zosangalatsa zabwino zotikondweletsa.

      Mafunso Obweleza

      • Kodi Mkhristu ayenela kupewa zosangalatsa zotani?

      • N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala nayo nthawi yotayila pa zosangalatsa?

      • N’cifukwa ciyani muyenela kusankha zosangalatsa zovomelezeka kwa Yehova?

      Colinga

      FUFUZANI

      Onani kuti ndani ali na udindo wotisankhila zosangalatsa.

      “Kodi Muli ndi Lamulo Loletsa Mavidiyo Ena, Mabuku Ena Ndiponso Nyimbo Zina?” (Nkhani ya pawebusaiti)

      Onani mmene mungapangile zisankho zabwino, pa nkhani ya zosangulutsa zimene mungacite panthawi yopumula.

      “Kodi Zimene Mumachita pa Nthawi Yosangalala Zimakhala Zopindulitsa?” (Nsanja ya Olonda, October 15, 2011)

      Mu nkhani yakuti “Ndinasiya Ngakhale Kudana ndi Azungu,” onani mmene munthu wina anasinthila zosangalatsa zake.

      “Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, February 1, 2010)

      Onani mmene mayi akupangila cisankho canzelu pa zosangalatsa zophatikizapo zamizimu.

      Pewani Zosangalatsa Zoonetsa Zamizimu (2:02)

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani