-
Mmene Tingapangile Zisankho ZabwinoKondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
3. Lolani kuti Baibo ikutsogoleleni
Kodi mfundo za m’Baibo zingatitsogolele motani popanga zisankho? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.
Kodi ufulu wodzisankhila zocita n’ciyani?
Nanga n’cifukwa ciyani Yehova anatipatsa ufulu wodzisankhila zocita?
Kodi iye anatipatsa ciyani cotithandiza kugwilitsa nchito bwino ufulu wodzisankhila zocita?
Kuti muone citsanzo ca mfundo za m’Baibo, ŵelengani Aefeso 5:15, 16. Ndiyeno kambilanani mmene mungagwilitse “nchito bwino nthawi yanu” kuti . . .
muziŵelenga Baibo nthawi zonse.
mukhale mnzake wa mu ukwati wabwino, kholo labwino, kapena mwana womvela.
muzipezeka pa misonkhano ya mpingo.
-
-
Sankhani Zosangalatsa Zovomelezeka kwa YehovaKondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
2. N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala nayo nthawi imene timathela pa zosangalatsa?
Ngakhale titasankha zosangalatsa zabwino, tiyenelabe kusamala kuti zisatidyele nthawi yoculuka kwambili. Tikapanda kusamala tidzasoŵa nthawi yocita zinthu zofunika kwambili. Baibo imatilimbikitsa ‘kugwilitsa nchito bwino nthawi yathu.’—Ŵelengani Aefeso 5:15, 16.
-
-
Sankhani Zosangalatsa Zovomelezeka kwa YehovaKondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
4. Gwilitsani nchito nthawi yanu mwanzelu
Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.
Ngakhale kuti m’bale wa mu vidiyo iyi sanali kutamba ciliconse coipa, kodi cinayamba kucitika kwa iye n’ciyani cifukwa cosasamala nayo nthawi yopumula?
Ŵelengani Afilipi 1:10, na kukambilana funso ili:
Kodi lembali lingatithandize bwanji kusamala nayo nthawi yocita zosangulutsa?
-