LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • N’ciyani Cingakuthandizeni Kuti Musaleke Kuphunzila Baibo?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • N’ciyani Cingakuthandizeni Kuti Musaleke Kuphunzila Baibo?

      Kuphunzila Baibo ni ulendo wopindulila kwambili. Koma ulendowu nthawi zina ungakhale wovutilapo, cakuti mungayambe kukayikila ngati mudzapitiliza kuphunzila Baibo. Koma n’cifukwa ciyani kulimbikilabe kuli kofunika? Ndipo n’ciyani cingakuthandizeni kupilila zovuta zimene zingakhalepo?

      1. N’cifukwa ciyani kuphunzila Baibo kuli kwaphindu?

      “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu.” (Aheberi 4:12) Baibo ni yothandiza kwambili cifukwa imakudziŵitsani maganizo a Mulungu. Ndiponso imakutsimikizilani kuti Mulungu amakukondani. Imakuthandizaninso kudziŵa zambili, ndiponso ingakupatseni nzelu zenizeni na ciyembekezo. Copambana zonse, Baibo ingakuthandizeni kukhala bwenzi la Yehova. Pamene mukuphunzila Baibo, mphamvu yake imayamba kusintha moyo wanu kukhala wabwino.

      2. N’cifukwa ciyani kuli kofunika kuzindikila phindu la coonadi ca m’Baibo?

      Mfundo za coonadi ca m’Baibo zili ngati cuma ca mtengo wapatali. Ndiye cifukwa cake Baibo imatilimbikitsa kuti “gula coonadi ndipo usacigulitse.” (Miyambo 23:23) Tikadziŵa phindu la coonadi ca m’Baibo, timalimbikilabe kuti tisaleke kuphunzila, olo pakhale zopinga.—Ŵelengani Miyambo 2:4, 5.

      3. Kodi Yehova angakuthandizeni bwanji kuti mupitilize kuphunzila?

      Pokhala Mlengi Wamphamvuzonse komanso Bwenzi, Yehova amafuna kukuthandizani kuti mum’dziŵe bwino. Iye amatha kukupatsani cilakolako, komanso mphamvu, yakuti muphunzile za iye. (Ŵelengani Afilipi 2:13) Conco, ngati nthawi zina mwacita mphwayi kuti muphunzile, kapena kugwilitsila nchito zimene mumaphunzila, iye amakhala wokonzeka kukuthandizani. Ndipo ngati mufunikila nyonga zowonjezela kuti muthane na zopinga, kapena anthu okutsutsani, iye akhozanso kukuthandizani. Pemphelani kwa Yehova nthawi zonse, kuti akuthandizeni kupitiliza kuphunzila Baibo.—1 Atesalonika 5:17.

      KUMBANI MOZAMILAPO

      Phunzilani mmene mungapitilizile kuphunzila Baibo, ngakhale mutakhala wotangwanika, kapena pamene anthu ena ayesa kukuletsani. Ndiyeno onani mmene Yehova angakuthandizileni kuti musaleke.

      4. Ikani kuphunzila Baibo patsogolo

      Nthawi zina tingakhale otangwanika kwambili na kuona kuti sitingapeze nthawi yophunzila Baibo. Kodi n’ciyani cingatithandize? Ŵelengani Afilipi 1:10, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi muganiza kuti zina mwa “zinthu zofunika kwambili” pa umoyo ni ziti?

      • Kodi mungacite bwanji kuti muike kuphunzila Baibo patsogolo?

      A. Zithunzi zoonetsa kuika miyala na mcenga m’bekete. 1. Mulu wa mcenga komanso mulu wa miyala ikulu-ikulu. 2. Bekete yothilamo mcenga wambili. 3. Miyalayo yakhala pamwamba pa mcenga ndipo ina yatsalako. B. Zithunzi: 1. Miyulu imodzimodziyo, wa mcenga komanso wa miyala. 2. Bekete imodzimodziyo koma yodzala na miyala. 3. Mcenga uloŵelela m’miyalayo, na kudzaza beketeyo mpaka pakamwa. Pangotsala tumcenga tocepa tumene situnaloŵe m’beketemo.
      1. Mukathila mcenga m’bekete, kenako n’kuikamo miyala, miyalayo siikwanamo ayi

      2. Koma mukayambilila kuikamo miyala, mudzakhala malo othilamo mcenga wambili. Mofananamo, ngati mutsogoza “zinthu zofunika kwambili” pa umoyo wanu, mudzakwanitsa kuzicita na kutsalako na nthawi yocitabe zinthu zina

      Tikamaphunzila Baibo timapeza zosowa zathu zauzimu—kutanthauza kuphunzila za Mulungu na kumulambila. Ŵelengani Mateyu 5:3, na kukambilana funso ili:

      • Kodi tikaika patsogolo kuphunzila Baibo, timapindula bwanji?

      5. Musalole kuti ena akuletseni kuphunzila

      Nthawi zina, anthu ena angayese kukulefulani kuti muleke kuphunzila Baibo. Onani citsanzo ca Francesco. Tambani VIDIYO, na kukambilana mafunso aya.

      VIDIYO: Tinafupidwa Cifukwa Copilila (5:22)

      Cocitika ca mu vidiyo yakuti ‘Tinafupidwa Cifukwa Copilila.’ Francesco alekena nawo anzake atawauza kuti sazicezanso nawo.
      • Mu vidiyo iyi, kodi anzake a Francesco, komanso a m’banja lake, anacita bwanji atawauza zimene anali kuphunzila?

      • Kodi kulimbikila kwake kunakhala na zotulukapo zabwino zotani?

      Ŵelengani 2 Timoteyo 2:24, 25, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi a m’banja mwanu komanso anzanu, amaganiza bwanji pa zimene mukuphunzila?

      • Malinga na mavesi aya, kodi mungayankhe bwanji ngati munthu wina ayesa kukuletsani kuphunzila Baibo? N’cifukwa ciyani mungayankhe conco?

      6. Dalilani Yehova kuti akuthandizeni

      Pamene timuyandikila Yehova, cikhumbo cathu cofuna kumukondweletsa cimakula. Ngakhale n’telo, cingakhale covuta kusintha zinthu pa umoyo wathu kuti tikhale na umoyo umene Mulungu amafuna. Ngati inunso muona kuti n’zovuta, musataye mtima. Yehova adzakuthandizani. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.

      VIDIYO: Yehova Amatithandiza Kusintha Umoyo Wathu (3:56)

      • Mu vidiyo iyi, kodi Jim anasintha ciyani pa umoyo wake kuti akondweletse Yehova?

      • N’ciyani cimakukondweletsani pa citsanzo cake?

      Ŵelengani Aheberi 11:6, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi Yehova adzawacitila ciyani anthu amene ‘amam’funafuna na mtima wonse’—inde, aja amene amalimbikila kum’dziŵa na kucita zimene akufuna?

      • Ndipo muganiza Yehova amamva bwanji akaona kuti mumalimbikila kuphunzila Baibo?

      MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “N’cifukwa ciyani mumaphunzila Baibo na Mboni za Yehova?”

      • Kodi mungamuyankhe bwanji?

      CIDULE CAKE

      Ngakhale kuti kuphunzila Baibo kungakhale kovuta nthawi zina, kungakuthandizeni kuti mukondwele na moyo kwamuyaya. Pitilizani kudalila Yehova, ndipo adzakudalitsani.

      Mafunso Obweleza

      • N’cifukwa ciyani mfundo za m’Baibo n’zamtengo wapatali kwa inu?

      • Kodi muyenela kucita ciyani ‘mukatsimikizila zinthu zofunika kwambili’?

      • N’cifukwa ciyani muyenela kupempha Yehova kuti akuthandizeni kupitiliza kuphunzila Baibo?

      Colinga

      FUFUZANI

      Onani njila zinayi zimene zathandiza anthu ambili kuseŵenzetsa nthawi yawo mwanzelu.

      “Kodi Mungatani Kuti Muzigwilitsa Nchito Bwino Nthawi” (Galamuka! February 2014)

      Onani mmene Yehova anathandizila mzimayi wina, amene mwamuna wake sanali kumvetsa cimene iye anali kucitila khama pofuna kukondweletsa Mulungu.

      Yehova Amatithandiza pa Mavuto (5:05)

      Onani mmene mwamuna wina anapindulila cifukwa ca kucilimika kwa mkazi wake.

      N’naika Coonadi pa Mayeso (6:30)

      Anthu ena amakamba kuti Mboni za Yehova kuti zimapasula mabanja. Koma kodi n’zoona zimenezi?

      “Kodi Mboni za Yehova Zimapasula Mabanja Kapena Zimamangiliza?” (Nkhani ya pawebusaiti)

  • Pitanibe Patsogolo Kuuzimu
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 3. Kodi Yehova adzakuthandizani bwanji kuti mupitebe patsogolo?

      Baibo imakamba kuti: “Mulungu . . . adzamalizitsa kukuphunzitsani. Adzakulimbitsani, ndi kukupatsani mphamvu.” (1 Petulo 5:10) Tonsefe timakumana na mayeselo otikopa. Koma Yehova amatithandiza kuti tisagonje ku mayeselo amenewo. (Salimo 139:23, 24) Iye akulonjeza kuti adzalimbikitsa cifuno canu cakuti mum’tumikile mokhulupilika.—Ŵelengani Afilipi 2:13.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani