-
Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kugonana?Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
4. Mukhoza kuwagonjetsa mayeselo
Kodi n’ciyani cingapangitse kuti zikhale zovuta kupewa mayeselo ocita ciwelewele? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.
Kodi m’bale wa mu vidiyo iyi, anacita ciyani atazindikila kuti maganizo ake na zocita zake zidzapangitsa kuti asakhale wokhulupilika kwa mkazi wake?
Ngakhale kwa Akhristu okhulupilika, nthaŵi zina cimakhala covuta kusungabe maganizo awo ali oyela. Kodi mungacite ciyani kuti mupewe kumangoganizila zinthu zoipa? Ŵelengani Afilipi 4:8, na kukambilana mafunso aya:
Kodi tiyenela kumaika maganizo athu pa zinthu zotani?
Kodi kuŵelenga Baibo komanso kukhala wotangwanika potumikila Yehova, kungatithandize bwanji kuti tipewe mayeselo amene angaticimwitse?
-
-
Kodi Mungamukondweletse Bwanji Yehova na Malankhulidwe Anu?Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
3. Kodi n’ciyani cingatithandize kumalankhula m’njila yolimbikitsana?
Kambili zinthu zimene timakambapo, zimaonetsa zimene zili mumtima mwathu na m’maganizo mwathu. (Luka 6:45) Conco, tiyenela kudzizoloŵeza kumaganizila zinthu zolungama, zoyela, zacikondi, komanso zoyamikilika. (Afilipi 4:8) Kuti maganizo athu azikhazikika pa zinthu zimenezi, tiyenela kusankha mwanzelu zosangalatsa komanso mabwenzi. (Miyambo 13:20) Cinanso cingatithandize ni kuyamba taganiza tisanalankhule. Ganizilani mmene mawu anu angakhudzile anthu ena. Baibo imakamba kuti: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizila ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzelu limacilitsa.”—Miyambo 12:18.
-