-
N’ciyani Cingakuthandizeni Kuti Musaleke Kuphunzila Baibo?Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
4. Ikani kuphunzila Baibo patsogolo
Nthawi zina tingakhale otangwanika kwambili na kuona kuti sitingapeze nthawi yophunzila Baibo. Kodi n’ciyani cingatithandize? Ŵelengani Afilipi 1:10, na kukambilana mafunso aya:
Kodi muganiza kuti zina mwa “zinthu zofunika kwambili” pa umoyo ni ziti?
Kodi mungacite bwanji kuti muike kuphunzila Baibo patsogolo?
Mukathila mcenga m’bekete, kenako n’kuikamo miyala, miyalayo siikwanamo ayi
Koma mukayambilila kuikamo miyala, mudzakhala malo othilamo mcenga wambili. Mofananamo, ngati mutsogoza “zinthu zofunika kwambili” pa umoyo wanu, mudzakwanitsa kuzicita na kutsalako na nthawi yocitabe zinthu zina
Tikamaphunzila Baibo timapeza zosowa zathu zauzimu—kutanthauza kuphunzila za Mulungu na kumulambila. Ŵelengani Mateyu 5:3, na kukambilana funso ili:
Kodi tikaika patsogolo kuphunzila Baibo, timapindula bwanji?
-
-
Sankhani Zosangalatsa Zovomelezeka kwa YehovaKondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
4. Gwilitsani nchito nthawi yanu mwanzelu
Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.
Ngakhale kuti m’bale wa mu vidiyo iyi sanali kutamba ciliconse coipa, kodi cinayamba kucitika kwa iye n’ciyani cifukwa cosasamala nayo nthawi yopumula?
Ŵelengani Afilipi 1:10, na kukambilana funso ili:
Kodi lembali lingatithandize bwanji kusamala nayo nthawi yocita zosangulutsa?
-