-
Ubatizo ni Khomo la ku Madalitso Oculuka!Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
3. Kodi munthu ayenela kucita ciyani asanabatizike?
Mufunika kuphunzila za Yehova na kulimbitsa cikhulupililo canu mwa iye. (Ŵelengani Aheberi 11:6.) Pamene cidziŵitso canu na cikhulupililo canu zikuwonjezeka, naconso cikondi canu pa Yehova cidzakulilako. Ndipo mosakaika konse, mudzafuna kuuzako ena za iye komanso kukhala na umoyo wogwilizana na malamulo ake. (2 Timoteyo 4:2; 1 Yohane 5:3) Munthu akayamba ‘kuyenda mogwilizana ndi zimene Yehova amafuna, kuti am’kondweletse pa ciliconse,’ angasankhe kupatulila moyo wake kwa Mulungu na kubatizika.—Akolose 1:9, 10.a
-
-
Ubatizo ni Khomo la ku Madalitso Oculuka!Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
a Ngati munthu anabatizika kale kucipembedzo cina, ayenela kubatizikanso. Cifukwa ciyani? Cifukwa cipembedzo cimeneco sicinam’phunzitse coonadi ca m’Baibo. Kuti tikhale ogwilizana m’cikhulupililo cimodzi cozikika pa coonadi, tiyenelanso kubatizika ubatizo umodzi wozikika pa coonadi.—Onani Machitidwe 19:1-5; Aefeso 4:5; komanso Phunzilo 13.
-
-
Kodi Ndinu Wokonzeka Kubatizika?Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
1. Kodi muyenela kudziŵa zoculuka motani kuti mubatizike?
Kuti mubatizike, muyenela ‘kudziŵa coonadi molondola.’ (1 Timoteyo 2:4) Izi sizitanthauza kuti muyenela kudziŵa mayankho onse pa mafunso onse a m’Baibo kuti mubatizike, ayi. Ngakhale Akhristu amene anabatizika zaka zambili kumbuyoku akali kuphunzilabe zinthu zambili m’Baibo. (Akolose 1:9, 10) Mungofunikila kudziŵa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo. Ndipo akulu mu mpingo wanu adzakuthandizani kuona ngati mwadziŵa zokwanila kuti mukabatizike.
-