LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kodi Muyenela Kucita Ciyani Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe?—Mbali 1
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • Palibe ukwati wangwilo. Conco, mwamuna na mkazi wake ayenela kuthandizana kuti agonjetse mavuto a mu ukwati wawo. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

      VIDIYO: Zimene Mungacite Kuti Mulimbitse Cikwati Canu (5:44)

      • Mu vidiyo imeneyi, kodi panali zizindikilo zotani zoonetsa kuti mwamuna na mkazi wake anayamba kukanganukana?

      • Koma anatenga masitepe otani kuti alimbitse ukwati wawo?

      Ŵelengani 1 Akorinto 10:24, komanso Akolose 3:13. Pambuyo poŵelenga lililonse la malemba awa, kambilanani funso ili:

      • Kodi kugwilitsa nchito uphungu wa pa lembali kungalimbitse bwanji ukwati?

      Baibo imakamba kuti tiyenela kulemekezana wina na mnzake. Kulemekeza munthu kumatanthauzanso kucita naye mokoma mtima komanso mwaulemu. Ŵelengani Aroma 12:10, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi mwamuna kapena mkazi wake ayenela kuyembekezela kuti mnzakeyo ndiye ayenela kuyamba kumulemekeza? N’cifukwa ciyani mwayankha conco

  • Sungani Mgwilizano wa Mpingo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 3. Kodi muyenela kucita ciyani mukasemphana maganizo na Mkhristu mnzanu?

      Ndife ogwilizana inde, koma sitili angwilo. Nthawi zina tingakhumudwitsane kapena kukwiyitsana wina na mnzake. Conco Mawu a Mulungu amatiuza kuti “pitilizani . . . kukhululukilana ndi mtima wonse.” Ndipo amawonjezela kuti: “Monga Yehova anakukhululukilani ndi mtima wonse, inunso teloni.” (Ŵelengani Akolose 3:13) Ngakhale kuti Yehova takhala tikumukwiyitsa maulendo osaŵelengeka, iye amatikhululukilabe. Conco, iye amatiyembekezela kucita cimodzimodzi kwa abale athu. Mukazindikila kuti mwakwiyitsa munthu wina, khalani woyamba kucitapo kanthu kuti muyanjanenso.—Ŵelengani Mateyu 5:23, 24.b

  • Sungani Mgwilizano wa Mpingo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 5. Muzikhululuka na mtima wonse komanso muzisungitsa mtendele

      Yehova amatikhululukila na mtima wonse, ngakhale kuti iye sakafunikilapo kuti tikamukhululukile. Ŵelengani Salimo 86:5, na kambilanani mafunso aya:

      • Kodi cikhululukilo ca Yehova n’cacikulu motani?

      • N’cifukwa ciyani mumayamikila kuti Yehova amakhululuka?

      • N’zocitika ziti zingapangitse kuti tisamagwilizane bwino na anthu ena?

      Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova pa nkhani ya kukhululuka kuti tikhalebe ogwilizana monga abale na alongo? Ŵelengani Miyambo 19:11, na kukambilana funso ili:

      • Ngati munthu wina wakukwiyitsani, kapena wakukhumudwitsani, kodi muyenela kucita ciyani kuti musungitse mtendele?

      Nthawi zina timakhumudwitsa anthu ena. Zimenezi zikacitika, kodi tiyenela kucita bwanji? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila

      VIDIYO: Kukhazikitsa Mtendele Kumabweletsa Madalitso (6:01)

      • Kodi mlongo wa mu vidiyo iyi anacita ciyani kuti asungitse mtendele?

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani