-
“Cipulumutso Canu Cikuyandikila”Nsanja ya Mlonda—2015 | July 15
-
-
14, 15. Ndi nchito yosonkhanitsa iti imene idzayamba Gogi wa Magogi akadzayamba kuukila anthu a Mulungu? Nanga n’ciani cidzacitika pa nthawi yosonkhanitsa imeneyi?
14 Kodi cidzacitika n’ciani Gogi wa Magogi akadzayamba kuukila anthu a Mulungu? Mabuku a Mateyo ndi Maliko amanena kuti: “[Mwana wa munthu] adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa pamodzi osankhidwa ake kucokela kumphepo zinai, kucokela kumalekezelo ake a dziko lapansi kukafika kumalekezelo a m’mlengalenga.” (Maliko 13:27; Mat. 24:31) Kusonkhanitsa kumeneku sikukutanthauza kusonkhanitsa koyamba kwa Akristu odzozedwa kapena kuwadinda cidindo comaliza. (Mat. 13:37, 38) Iwo adzadindidwa cidindo comaliza cisautso cacikulu cisanayambe. (Chiv. 7:1-4) Nanga Yesu anali kukamba za kusonkhanitsa kuti? Kusonkhanitsa kumeneku kudzacitika panthawi imene otsalila a 144,000 adzalandila mphoto yao yakumwamba. (1 Ates. 4:15-17; Chiv. 14:1) Zimenezi zidzacitika panthawi inayake Gogi wa Magogi atayamba kale kuukila anthu a Mulungu. (Ezek. 38:11) Apa m’pamene mau a Yesu adzakwanilitsidwa, akuti: “Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambili ngati dzuŵa mu ufumu wa Atate wao.”—Mat. 13:43.b
15 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti odzozedwa ‘adzakwatulidwa’ kupita kumwamba ndi thupi la nyama? Anthu ambili a m’Machalichi Acikristu amakhulupilila kuti, Akristu adzatengedwa ndi matupi ao. Ndiponso amaganiza kuti Yesu adzabwela ndipo adzamuona ndi maso ao akulamulila. Koma Baibulo limanena momveka bwino kuti “cizindikilo ca Mwana wa munthu” cidzaonekela kumwamba ndipo Yesu adzabwela “pamitambo ya kumwamba.” (Mat. 24:30) Mau amenewa akusonyeza kuti kubwela kwake kudzakhala kosaonekela ndi maso. Kuonjezela apo, “mnofu ndi magazi sizingaloŵe ufumu wa Mulungu.” Motelo odzozedwa akalibe kutengedwa kupita kumwamba, coyamba ‘adzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethila kwa diso, pa kulila kwa lipenga lomaliza.’c (Ŵelengani 1 Akorinto 15:50-53.) Conco, sitimanena kuti Akristu odzozedwa ‘adzakwatulidwa’ cifukwa cakuti anthu amalimva molakwika liuli. Koma adzatengedwa m’kanthawi kocepa.
-
-
“Cipulumutso Canu Cikuyandikila”Nsanja ya Mlonda—2015 | July 15
-
-
c Matupi a nyama a odzozedwa amene adzakhala ndi moyo panthawiyo sadzatengedwa kupita kumwamba. (1 Akor. 15:48, 49) Yesu sanapite kumwamba ndi thupi la nyama, naonso odzozedwa sadzapita kumwamba ndi matupi ao a nyama.
-