LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Yehova Adzakucilikizani
    Nsanja ya Mlonda—2015 | December 15
    • 13. N’ciani cimene tiyenela kukumbukila tisanauze munthu malangizo okhudza thanzi kapena ifeyo tisanatsatile malangizo amene tapatsidwa?

      13 Masiku ano, Akristu anzathu sangaticilitse mozizwitsa. Komabe, abale athu ena pofuna kutithandiza angatipatse malangizo okhudza thanzi ngakhale kuti sitinawapemphe. Malangizo ena amene angatipatse angakhale abwino. Mwacitsanzo, Paulo anauza Timoteyo kuti azimwako vinyo pang’ono. Timoteyo anali ndi vuto la m’mimba. Mwina vutoli linabwela cifukwa ca madzi oipa amene anali kumwa.a (Onani mau a munsi.) (Ŵelengani 1 Timoteyo 5:23.) Komabe, tifunika kukhala osamala. Mkristu mnzathu angatiuze kuti timwe mankhwala ena ake a kucipatala kapena azitsamba. Angatiuzenso kuti tizidya kapena kupewa kudya zakudya zina. Iye angakambe kuti wacibale wake anali ndi vuto ngati lathu, ndipo anacila atacita zimenezo. Koma zimenezi sizitanthauza kuti ifenso tidzacila tikatsatila malangizowo. Tizikumbukila kuti mankhwala angathe kubweletsa mavuto aakulu ngakhale kuti anthu ambili amawagwilitsila nchito.—Ŵelengani Miyambo 27:12.

  • Yehova Adzakucilikizani
    Nsanja ya Mlonda—2015 | December 15
    • a Buku lina linakamba kuti asayansi apeza kuti tuzilombo twa thaifodi ndi tuzilombo twina toyambitsa matenda, tumafa mwamsanga akatusakaniza ndi vinyo.—The Origins and Ancient History of Wine.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani