LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Anthu a Yehova “Aleke Kucita Zosalungama”
    Nsanja ya Mlonda—2014 | July 15
    • 9. “Mafunso opusa ndi opanda nzelu” anaukhudza bwanji mpingo wacikristu woyambilila?

      9 Baibulo lili ndi malangizo acindunji okhudza zosalungama zimene Akristu ayenela kuleka kapena kukana. Mwacitsanzo, m’mau ake a patsogolo pa lemba la 2 Timoteyo 2:19, Paulo anauza Timoteyo kuti “asamakangane pa mau” ndi kuti “azipewa nkhani zopeka.” (Ŵelengani 2 Timoteyo 2:14, 16, 23.) Anthu ena mumpingo anali kulimbikitsa ziphunzitso zampatuko. Ndipo ena anali kuyambitsa maganizo opotoka. Ngakhale kuti anthuwo sanali kutsutsa malemba mwacindunji, io anali kucititsa magaŵano. Anacititsa kuti anthu mumpingo ayambe kukangana pa mau ndipo mumpingo munaloŵa mzimu woipa. Ndiye cifukwa cake Paulo anawagogomezela kuti ‘azikana mafunso opusa ndi opanda nzelu.’

      10. Tiyenela kucitanji tikakumana ndi ampatuko?

      10 Masiku ano, anthu a Yehova sakumana ndi ampatuko mumpingo. Komabe, tisazengeleze kukaniza ziphunzitso zilizonse zosagwilizana ndi malemba. Ndi kupanda nzelu kukangana ndi ampatuko kaya pamaso m’pamaso, pa webusaiti yao, kapena mwanjila ina iliyonse. Ngakhale pamene colinga ndico kuthandiza winawake, kukambitsilana kwa conco n’kosafunika malinga n’zimene tangokambitsilana. M’malo mwake, monga anthu a Yehova tiyenela kupewelatu ampatuko.

      11. N’ciani cingayambitse ‘mafunso opanda nzelu’? Nanga akulu mu mpingo angaonetse bwanji citsanzo cabwino?

      11 Kupatulapo mpatuko, pali zinthu zina zimene zingaononge mtendele wa mpingo. Mwacitsanzo, nkhani yosankha zosangulutsa ingayambitse “mafunso opusa ndi opanda nzelu.”Ngati ena mumpingo akonda zosangulutsa zosagwilizana ndi miyezo ya makhalidwe a Yehova, akulu sayenela kulekelela makhalidwe amenewo pofuna kupewa mikangano. (Sal. 11:5; Aef. 5:3-5) Komabe, ayenela kusamala kuti asazilimbikitsa maganizo ao. Iwo ayenela kutsatila uphungu wa oyang’anila acikristu wakuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, . . . Osati mocita ufumu pa anthu amene ali coloŵa cocokela kwa Mulungu, koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.”—1 Pet. 5:2, 3; ŵelengani 2 Akorinto 1:24.

  • Anthu a Yehova “Aleke Kucita Zosalungama”
    Nsanja ya Mlonda—2014 | July 15
    • 13 Mfundo za m’Baibulo zimene takambilana sizigwila cabe nchito pankhani yokhudza zosangulutsa. Kusiyana maganizo pankhani ya kavalidwe ndi maonekedwe, thanzi, zakudya, ndi nkhani zina zaumwini, kungayambitsenso mikangano. Komabe, ngati palibe mfundo za m’Baibulo zimene zanyalanyazidwa, anthu a Yehova amapewa kukangana ndi ena pankhani zimenezi. Iwo amadziŵa kuti “kapolo wa Ambuye sayenela kukangana ndi anthu, koma ayenela kukhala wodekha kwa onse.”—2 Tim. 2:24.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani