-
N’ciyani Cingakuthandizeni Kuti Musaleke Kuphunzila Baibo?Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
5. Musalole kuti ena akuletseni kuphunzila
Nthawi zina, anthu ena angayese kukulefulani kuti muleke kuphunzila Baibo. Onani citsanzo ca Francesco. Tambani VIDIYO, na kukambilana mafunso aya.
Mu vidiyo iyi, kodi anzake a Francesco, komanso a m’banja lake, anacita bwanji atawauza zimene anali kuphunzila?
Kodi kulimbikila kwake kunakhala na zotulukapo zabwino zotani?
Ŵelengani 2 Timoteyo 2:24, 25, na kukambilana mafunso aya:
Kodi a m’banja mwanu komanso anzanu, amaganiza bwanji pa zimene mukuphunzila?
Malinga na mavesi aya, kodi mungayankhe bwanji ngati munthu wina ayesa kukuletsani kuphunzila Baibo? N’cifukwa ciyani mungayankhe conco?
-
-
Kodi Ena Mungawauzeko Bwanji Uthenga Wabwino?Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
Pouzako ena uthenga wabwino, musamangoganizila zimene mufuna kukamba, muziganilanso mozikambila. Ŵelengani 2 Timoteyo 2:24, komanso 1 Petulo 3:15, na kukambilana mafunso aya:
Kodi mungaseŵenzetse bwanji mfundo zili pa mavesi aya pouzako ena za m’Baibo?
Ngati acibale anu ena kapena anzanu sakuvomeleza zimene mukukamba, kodi muyenela kucita ciyani? Ndipo muyenela kupewa kucita ciyani?
N’cifukwa ciyani ni bwino kukambilana nawo mwaulemu, m’malo mowaumiliza kuti akhulupilile zimene mukukamba?
-