-
Ufumu wa Mulungu Ukulamulila Pali Pano!Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
2. Kucokela mu 1914, kodi padziko pakhala pakucitika zinthu zotani, ndipo anthu akuonetsa makhalidwe otani?
Ophunzila a Yesu anamufunsa kuti: “Kodi . . . cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciyani?” (Mateyu 24:3) Powayankha, Yesu ananenelatu zinthu zambili zodzacitika pambuyo pakuti iye wayamba kulamulila kumwamba mu Ufumu wa Mulungu. Zina mwa zocitikazo zikuphatikizapo nkhondo, njala, na zivomezi. (Ŵelengani Mateyu 24:7.) Baibo inakambilatunso kuti mu “masiku otsiliza” anthu adzakhala na makhalidwe opangitsa umoyo kukhala wovuta. (2 Timoteyo 3:1-5) Zocitika zimenezi, komanso makhalidwe a anthu amenewa, zaonekela kwambili maka-maka kuyambila mu 1914.
3. N’cifukwa ciyani zinthu zaipa kwambili conco padzikoli kucokela pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila?
Yesu atangoikidwa kukhala Mfumu, kumwamba kunabuka nkhondo pakati pa iye na Satana pamodzi na ziŵanda zake. Pa nkhondoyo Satana anagonjetsedwa. Baibo imakamba kuti “iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.” (Chivumbulutso 12:9, 10, 12) Satana ni wokwiya kwambili cifukwa akudziŵa kuti adzawonongedwa. Conco, iye amacititsa mavuto ambili komanso zopweteka padziko lapansi. Ndiye cifukwa cake zinthu zafika poipa kwambili padziko! Koma Ufumu wa Mulungu udzacotsapo mavuto onsewa.
-
-
Ufumu wa Mulungu Ukulamulila Pali Pano!Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
5. Dziko linasintha kucokela mu 1914
Yesu ananenelatu zimene zidzacitika padziko lapansi, zoonetsa kuti iye wakhala Mfumu. Ŵelengani Luka 21:9-11, na kukambilana funso ili:
Mwa zocitika zimenezi, kodi ni ziti zimene mwaonapo kapena kumvako?
Mtumwi Paulo anafotokoza mmene anthu adzakhalila m’masiku otsiliza a ulamulilo wa anthu. Ŵelengani 2 Timoteyo 3:1-5, na kukambilana funso ili:
Mwa makhalidwe amenewa, ni ati amene mukuona mwa anthu masiku ano?
-