LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2018 | January
    • 3. Ni anthu ati amene ali na makhalidwe ochulidwa pa 2 Timoteyo 3:2-5?

      3 M’kalata yake yopita kwa Timoteyo, mtumwi Paulo analemba kuti “masiku otsiliza” adzakhala “nthawi yapadela komanso yovuta.” Kenako, anachula makhalidwe 19 oipa amene anthu ali nawo masiku otsiliza ano. Makhalidwe amene anachula ni ofanana ndi amene ali pa Aroma 1:29-31. Koma pochula makhalidwewa m’kalata yopita kwa Timoteyo, iye anaseŵenzetsa mau ena amene sapezeka kwina kulikonse m’Malemba Acigiriki Acikhristu. Paulo anayamba kuchula makhalidwewa ni mau akuti “pakuti anthu adzakhala . . . ” Komabe, si anthu onse amene ali na makhalidwe oipa amenewa. Akhristu ali na makhalidwe abwino.—Ŵelengani Malaki 3:18.

  • Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2018 | January
    • 4. Kodi anthu odzitukumula na onyada amadziona bwanji?

      4 Paulo analemba kuti anthu adzakhala odzikonda ndi okonda ndalama. Kenako, analemba kuti anthu adzakhala odzimva, odzikweza, odzitukumula ndiponso onyada. Nthawi zambili, munthu amakhala na makhalidwe amenewa cifukwa codziona ngati wapamwamba kwambili kaamba ka maluso amene ali nawo, maonekedwe, cuma, kapena udindo wake. Anthu a makhalidwe amenewa amafuna kuti ena aziwatamanda. Katswili wina anafotokoza mmene munthu wonyada kwambili amadzionela. Analemba kuti: “Mu mtima mwake amakhala ngati ali na kaguwa, kamene amapitapo kukagwada n’kumadzilambila.” Ena amakamba kuti khalidwe lonyada n’loipa kwambili cakuti olo anthu onyadawo amaipidwanso na anthu anzawo onyada.

  • Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2018 | January
    • 8. (a) Kodi kusamvela makolo, anthu ena amakuona bwanji masiku ano? (b) Kodi Malemba amalangiza ana kucita ciani?

      8 Paulo anafotokoza mmene anthu adzayamba kucitila zinthu na anthu anzawo m’masiku otsiliza. Iye analemba kuti m’masiku otsiliza, ana adzakhala osamvela makolo. Masiku ano, mabuku ambili, mafilimu, na mapulogilamu a pa TV, amalimbikitsa ana kukhala osamvela makolo kapena kuona ngati khalidweli lilibe vuto. Koma zoona zake n’zakuti kusamvela makolo kumasokoneza mtendele wa banja, lomwe ndilo maziko ofunika a cikhalidwe ca anthu. Kuyambila kale-kale, anthu akhala akuidziŵa bwino mfundo imeneyi. Mwacitsanzo, ku Girisi, ngati munthu wamenya makolo ake, anali kulandidwa ufulu uliwonse umene anali nawo monga nzika. Ndipo m’malamulo a Aroma, kumenya tate unali mlandu waukulu kulingana na mlandu wa kupha munthu. Komanso, Malemba Aciheberi na Malemba Acigiriki Acikhristu, onse amalangiza ana kuti azilemekeza makolo awo.—Eks. 20:12; Aef. 6:1-3.

  • Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2018 | January
    • 10, 11. (a) Ni makhalidwe oipa ati amene amaonetsa kuti anthu sakonda anzawo? (b) Kodi cikondi cimene Akhristu oona ali naco pa anthu anzawo n’cacikulu motani?

      10 Paulo anachulanso makhalidwe ena oipa amene amaonetsa kuti anthu alibe cikondi pa wina na mnzake. Iye atachula za “kusamvela makolo,” anachula za kusayamika. Anthu osayamika amasuliza zabwino zimene ena amawacitila. Anakambanso kuti anthu adzakhala osakhulupilika. Adzakhala osafuna kugwilizana ndi anzawo, kapena kuti osafuna kukambilana kuti agwilizanenso na anthu amene anakangana nawo. Adzakhalanso onyoza ndi aciwembu, kapena kuti okamba mau opweteka ndi acipongwe kwa anthu anzawo, ngakhale kwa Mulungu. Komanso, anakamba kuti anthu adzakhala onenela anzawo zoipa pofuna kuwaipitsila mbili.a

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani