LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2018 | January
    • 9. N’ciani cingathandize ana kuti azimvela makolo awo?

      9 Ana angapewe kutengela khalidwe losamvela makolo mwa kuganizila zabwino zimene makolo awo amawacitila. Cina cimene cingawalimbikitse kucita izi, ni kukumbukila kuti kumvela ni lamulo locokela kwa Mulungu, Atate wa ife tonse. Ndipo ngati ana amakamba zabwino ponena za makolo awo, angathandize ana anzawo kuti azilemekezanso makolo awo. Ngati makolo saonetsa cikondi cacibadwa kwa ana awo, cingakhale covuta kuti anawo aziwamvela na mtima wonse. Koma ngati ana amaona kuti makolo awo amawakondadi, amalimbikitsidwa kuwamvela ngakhale pamene aona kuti n’zovuta kutelo. Mnyamata wina, dzina lake Austin anati: “N’nali na mtima wosafuna kumvela. Koma makolo anga anali kunipatsa malamulo amene ningakwanitse kuwatsatila, anali kunifotokozela cifukwa cake anipatsa malamulowo, na kumakamba nane momasuka. Izi zinanithandiza kukhala womvela. N’nali kuona kuti amanikonda, ndipo zimenezo zinanilimbikitsa kuti nizicita zinthu zowakondweletsa.”

      10, 11. (a) Ni makhalidwe oipa ati amene amaonetsa kuti anthu sakonda anzawo? (b) Kodi cikondi cimene Akhristu oona ali naco pa anthu anzawo n’cacikulu motani?

      10 Paulo anachulanso makhalidwe ena oipa amene amaonetsa kuti anthu alibe cikondi pa wina na mnzake. Iye atachula za “kusamvela makolo,” anachula za kusayamika. Anthu osayamika amasuliza zabwino zimene ena amawacitila. Anakambanso kuti anthu adzakhala osakhulupilika. Adzakhala osafuna kugwilizana ndi anzawo, kapena kuti osafuna kukambilana kuti agwilizanenso na anthu amene anakangana nawo. Adzakhalanso onyoza ndi aciwembu, kapena kuti okamba mau opweteka ndi acipongwe kwa anthu anzawo, ngakhale kwa Mulungu. Komanso, anakamba kuti anthu adzakhala onenela anzawo zoipa pofuna kuwaipitsila mbili.a

  • Muziona Kusiyana Pakati pa Anthu
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2018 | January
    • a Liu la Cigiriki limene linamasulidwa kuti “onenela anzawo zoipa,” kapena kuti “woneneza” ni di·aʹbo·los. M’Baibo, liu limeneli limagwilitsidwa nchito monga dzina la Satana, amene amanenela Mulungu zoipa.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani