LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Makolo Thandizani Ana Anu Kupeza ‘Nzelu Zowathandiza Kuti Akapulumuke’
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2017 | December
    • 3. (a) Kodi Timoteyo anaphunzila bwanji cikhristu? Nanga anacita bwanji na zimene anaphunzilazo? (b) Kodi Paulo analangiza Timoteyo pa mbali zitatu ziti zokhudza kuphunzila?

      3 Timoteyo ayenela kuti anaphunzila Cikhristu m’caka ca 47 C.E., pa ulendo woyamba wa mtumwi Paulo wokacezela Akhristu a ku Lusitara. Ngakhale kuti pa nthawiyo Timoteyo anali wacicepele, iye anali kuseŵenzetsa zimene anaphunzila. Patapita zaka ziŵili, anayamba kuyenda na Paulo. Zaka 16 pambuyo pake, Paulo analembela Timoteyo kalata na kumuuza kuti: “Pitiliza kutsatila zimene unaphunzila ndi zimene unakhulupilila pambuyo pokhutila nazo, cifukwa ukudziŵa anthu amene anakuphunzitsa. Kuyambila pamene unali wakhanda, wadziŵa malemba oyela [Malemba Aciheberi] amene angathe kukupatsa nzelu zokuthandiza kuti udzapulumuke kudzela m’cikhulupililo cokhudza Khristu Yesu.” (2 Tim. 3:14, 15) Pamenepa, Paulo anachula zinthu zitatu, (1) kudziŵa malemba oyela, (2) kukhulupilila pambuyo pokhutila na zimene anaphunzila, ndi (3) kupeza nzelu zomuthandiza kuti akapulumuke kudzela m’cikhulupililo cokhudza Khristu Yesu.

  • Makolo Thandizani Ana Anu Kupeza ‘Nzelu Zowathandiza Kuti Akapulumuke’
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2017 | December
    • “UNAKHULUPILILA PAMBUYO POKHUTILA NAZO”

      5. (a) Kodi ‘kukhulupilila pambuyo pokhutila nazo’ kumatanthauzanji? (b) Tidziŵa bwanji kuti Timoteyo anakhutila na uthenga wabwino wokamba za Yesu?

      5 Kudziŵa malemba oyela n’kofunika. Komabe, kuphunzitsa ana coonadi kumafuna zambili kuposa kuwauza cabe za anthu na zocitika za m’Baibo. Kumbukilani kuti Timoteyo ‘anakhulupilila pambuyo pokhutila’ na zimene anaphunzila. M’citundu coyambilila, mau akuti ‘kukhulupilila pambuyo pokhutila,’ amatanthauza “kukhala wosakayikila kuti zinazake n’zoona.” Timoteyo anadziŵa Malemba Aciheberi kuyambila ali wakhanda. Koma m’kupita kwa nthawi, iye anakhulupilila kuti Yesu anali Mesiya cifukwa ca umboni wokhutilitsa umene anapeza. Cikhulupililo ca Timoteyo cinalimba, cakuti anabatizika na kukhala wophunzila wa Yesu. Kenako, anayamba kugwila nchito ya umishonale na Paulo.

      6. Kodi mungam’thandize bwanji mwana wanu kuti akhutile na zimene amaphunzila m’Mau a Mulungu na kuzikhulupilila?

      6 Kodi mungawathandize bwanji ana anu kukhutila na zimene amaphunzila na kuzikhulupilila ngati mmene Timoteyo anacitila? Coyamba, muzikhala oleza mtima. Pamatenga nthawi kuti munthu akhulupilile zimene amaphunzila. Komanso, ngati inu mumakhulupilila zinazake, sizitanthauza kuti nawonso ana anu adzazikhulupilila. Mwana aliyense amafunika kuseŵenzetsa ‘luntha lake la kuganiza’ kuti akhulupilile coonadi ca m’Baibo. (Ŵelengani Aroma 12:1.) Koma imwe monga kholo, muli na udindo waukulu wom’thandiza mwanayo, maka-maka ngati amakonda kufunsa mafunso. Tiyeni tikambilane citsanzo ca kholo lina.

      7, 8. (a) Kodi kholo lina lacikhristu limaonetsa bwanji kuleza mtima pophunzitsa mwana wake? (b) N’cifukwa ciani na imwe muona kuti mufunika kukhala woleza mtima na mwana wanu?

      7 Thomas, m’bale amene ali na mwana wa zaka 11 anati: “Nthawi zina, mwana wanga amafunsa mafunso monga akuti, ‘Kodi n’kutheka kuti Yehova anaseŵenzetsa cisanduliko polenga zamoyo padziko?’ kapena, ‘N’cifukwa ciani siticitako zinthu zina zimene anthu ena amacita, monga kuvota, kuti tikonze zinthu padzikoli?’ Nthawi zina, nimacita kudzigwila kuti nisangomuyankha na mfundo imodzi yacindunji. Nimadziŵa kuti munthu sakhuta na nthongo imodzi. Mwana amafunika kumufotokozela zinthu pang’ono ndi pang’ono kuti akakhutile.”

      8 Monga mmene Thomas anaonela, kuphunzitsa mwana kumafuna kuleza mtima. Ndipo kuleza mtima n’kofunika kwa Akhristu onse. (Akol. 3:12) Thomas anazindikila kuti mwana angafunike kukamba naye nkhani zina mobweleza-bweleza kuti afike pokhutila. Conco, iye amafotokoza Malemba momveka bwino kwa mwanayo kuti am’thandize kukhulupilila zimene akuphunzila. Thomas anati: “Maka-maka pa nkhani zofunika kwambili, ine na mkazi wanga timafuna kudziŵa ngati mwana wathu akumvetsetsa na kukhulupilila zimene tikumuphunzitsa. Conco, akamafunsa mafunso, timaona kuti zili bwino. Kukamba zoona, timakhalako na nkhawa ngati iye avomeleza zilizonse popanda kufunsa mafunso.”

      9. Kodi mungakhomeleze bwanji Mau a Mulungu mwa ana anu?

      9 Ngati makolo apitiliza kuphunzitsa ana awo moleza mtima, pang’ono ndi pang’ono anawo adzadziŵa “m’lifupi ndi m’litali ndi kukwela ndi kuzama,” kwa coonadi. (Aef. 3:18) Muyenela kuwaphunzitsa zinthu zogwilizana na msinkhu wawo ndiponso luso lawo lomvetsa zinthu. M’kupita kwa nthawi, adzayamba kukhulupilila zimene akuphunzila, ndipo adzakhala okonzeka kuteteza cikhulupililo cawo pamaso pa ena, kuphatikizapo anzawo a ku sukulu. (1 Pet. 3:15) Mwacitsanzo, kodi ana anu angakwanitse kuseŵenzetsa Baibo pofotokoza zimene zimacitika munthu akamwalila? Kodi zimene Baibo imakamba pankhaniyi amazikhulupilila?a Kukhomeleza Mau a Mulungu mwa ana anu kumafuna kukhala woleza mtima, koma kuli na mapindu ambili.—Deut. 6:6, 7.

      10. N’ciani cina cofunika pophunzitsa ana anu?

      10 Citsanzo canu n’cofunikanso kwambili pothandiza ana anu kukhulupilila zimene amaphunzila. Stephanie, amene ni kholo la ana atatu, anati: “Kucokela pamene ana anga anali aang’ono, nakhala nikudzifunsa kuti, ‘Kodi nimawauza ana anga cifukwa cake ine nimakhulupilila kuti Yehova aliko, amatikonda komanso kuti mfundo zake n’zabwino? Kodi ana anga amaona kuti ine nimam’kondadi Yehova?’ Siningayembekezele ana anga kukhulupilila zinthu zimene ine sinizikhulupilila.”

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani