LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • Phunzilo 1. Baibo yotsegula.

      PHUNZILO 1

      Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?

      Tonse timafuna kudziŵa mayankho pa mafunso okhudza moyo, mavuto, imfa, komanso za kutsogolo. Timakhalanso na nkhawa zina, monga mmene tingapezele ndalama kapena mmene tingakhalile na cimwemwe m’banja. Anthu ambili apeza kuti Baibo yawathandiza kupeza mayankho pa mafunso ofunika pa umoyo, komanso yawapatsa ulangizi wothandiza kwambili. Ndithudi, Baibo ingathandize munthu aliyense.

      1. Kodi ni mafunso ena ati amene Baibo imayankha?

      Baibo imayankha mafunso ofunika kwambili aya: Kodi moyo unayamba bwanji? Nanga colinga ca moyo n’ciyani? N’cifukwa ciyani anthu osalakwa nawonso amavutika? Kodi munthu akamwalila amayenda kuti? Popeza tonse mtendele timaufuna, n’cifukwa ciyani padziko pakucitika nkhondo zambili conco? Kodi n’ciyani cidzacitike padziko lapansi m’tsogolo? Baibo imatilimbikitsa kufufuza mayankho a mafunso amenewa. Ndipo pali anthu mamiliyoni amene apeza mayankho okhutilitsa kwambili.

      2. Kodi Baibo ingatithandize bwanji kukondwela na umoyo wathu?

      Baibo imatipatsa malangizo anzelu. Mwacitsanzo, imaphunzitsa mabanja mmene angapezele cimwemwe ceni-ceni. Imatilangizanso zocita tikakhala na nkhawa, komanso mmene tingakondwele na nchito yathu. Mudzadziŵa zimene Baibo imaphunzitsa pa nkhani zimenezi, komanso zina zambili pamene tikambitsilana za m’buku lino. Inunso mudzavomeleza kuti “malemba onse [zonse zolembedwa m’Baibo] ndi . . . opindulitsa.”—2 Timoteyo 3:16.

      Buku lino silitenga malo a Baibo. Koma lidzakulimbikitsani kuti muziiŵelenga Baibo kuti muimvetsetse. Conco, muziŵelenga malemba amene aikidwa m’maphunzilo ano, ndiponso onani mmene akugwilizanila na zimene mukuphunzila.

      KUMBANI MOZAMILAPO

      Ganizilani mmene Baibo yathandizila anthu, mmenenso mungasangalalile poiŵelenga, komanso cifukwa cake kuli kofunika kuti wina akuthandizeni kuimvetsetsa.

      3. Baibo ingatiunikile njila

      Baibo ili monga toci yowala bwino. Ingatithandize kupanga zisankho zanzelu, na kudziŵilatu zimene zidzacitika kutsogolo.

      Ŵelengani Salimo 119:105, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi mlembi wa salimo ili anali kuiona bwanji Baibo?

      • Nanga inu mumaiona bwanji Baibo?

      Munthu akuyenda m’njila ya miyala mbali mwa nyanja kamdima katayamba, ndipo akuunika m’njila yake na toci yowala bwino.

      4. Baibo ikhoza kuyankha mafunso athu

      Mzimayi wina anakamba kuti Baibo inayankha mafunso amene anam’vutitsa maganizo kwa zaka zambili. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.

      VIDIYO: Musataye Mtima! (1:48)

      • Kodi mzimayi wa mu vidiyo iyi anali na mafunso otani?

      • Kodi kuphunzila Baibo kunam’thandiza bwanji?

      Baibo imatilimbikitsa kufunsa mafunso. Ŵelengani Mateyu 7:7, na kukambilana funso ili:

      • Kodi muli na mafunso abwanji amene mungakonde kupeza mayankho ake m’Baibo?

      5. Kuŵelenga Baibo kungakukondweletseni

      Anthu ambili amakondwela kuŵelenga Baibo, ndipo kumawapindulila. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.

      VIDIYO: Kuŵelenga Baibo (2:05)

      • Mu vidiyo iyi, kodi acinyamatawo nkhani ya kuŵelenga anali kuiona bwanji?

      • Nanga n’cifukwa ciyani kuŵelenga Baibo lomba amakuona mosiyana?

      Baibo imanena kuti ingatipatse malangizo otitonthoza, imatipatsanso ciyembezo. Ŵelengani Aroma 15:4, na kukambilana funso ili:

      • Pamene Baibo imalonjeza za citonthozo na kupeleka ciyembekezo, kodi zimakukopani mtima?

      6. Ena angatithandize kuimvetsetsa Baibo

      Kuwonjezela pa kuŵelenga Baibo paokha, ambili apeza kuti n’zothandizanso kuikambilana na munthu wina. Ŵelengani Machitidwe 8:26-31, na kukambilana funso ili:

      • Kodi n’ciyani cingatithandize kuimvetsetsa Baibo?—Onani mavesi 30 na 31.

      Zithunzi: 1. Mlaliki Filipo akufotokoza malemba kwa mwamuna wa ku Itiyopiya. 2. Mboni ya Yehova ikambilana Baibo na mayi pamodzi na ana ake aŵili.

      Mwamuna wa ku Itiyopiya anafunikila thandizo kuti amvetsetse Malemba. Anthu ambili masiku ano apeza kuti n’zothandiza kukambitsilana Baibo na munthu wina

      ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Kuphunzila Baibo n’kutaya cabe nthawi.”

      • Nanga inu muganiza bwanji? Cifukwa ciyani?

      CIDULE CAKE

      Baibo imatipatsa ulangizi wothandiza pa umoyo, imayankha mafunso ofunika kwambili, ndiponso imapeleka citonthozo na ciyembekezo.

      Mafunso Obweleza

      • Kodi m’Baibo tingapezemo ulangizi wotani wothandiza?

      • Nanga ni mafunso ena ati amene Baibo imayankha?

      • N’ciyani cimene mungakonde kuphunzila m’Baibo?

      Colinga

      FUFUZANI

      Ganizilani mmene ulangizi wa m’Baibo ulili wothandiza masiku ano.

      “Ziphunzitso za m’Baibo N’zothandiza Nthawi Zonse” (Nsanja ya Mlonda Na. 1 2018)

      Onani mmene Baibo inathandizila munthu amene anali na mtima wapacala kuyambila ali wamng’ono.

      Ciyambi ca Moyo Watsopano Wacimwemwe (2:53)

      Onani malangizo othandiza pa umoyo wa banja.

      “Zinsinsi 12 za Mabanja Acimwemwe” (Galamuka! Na. 2 2018)

      Onani mmene Baibo imaunikila bwino za amene akulamulila dziko lapansi, zimene anthu ambili sadziŵa.

      N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? —Vidiyo Yonse (3:14)

  • Baibo ni Uthenga wa Mulungu kwa Ife
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 1. Ngati anthu ni amene analemba Baibo, n’cifukwa ciyani timanena kuti ni Mawu a Mulungu?

      Anthu okwana ngati 40 ndiwo analemba Baibo. Inatenga zaka pafupifupi 1,600, kucokela mu 1513 B.C.E. mpaka m’ma 98 C.E. Ndipo olemba ake anali a zikhalidwe zosiyana-siyana, monga abusa, asodzi, komanso mafumu. Ngakhale n’telo, mbali zonse za Baibo zimavomelezana. Koma kodi n’zotheka bwanji? Cifukwa Baibo ni mawu a Mulungu. (Ŵelengani 1 Atesalonika 2:13.) Olemba Baibo sanalembemo maganizo awo. M’malo mwake, iwo “analankhula mawu ocokela kwa Mulungu motsogoleledwa ndi mzimu woyela.”a (2 Petulo 1:21) Mulungu anaseŵenzetsa mzimu wake woyela kutsogolela anthu amenewo kulemba maganizo ake.—2 Timoteyo 3:16.

  • Baibo ni Uthenga wa Mulungu kwa Ife
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 4. Baibo imatiululila Mwiniwake

      Tambani VIDIYO. Pambuyo pake ŵelengani 2 Timoteyo 3:16, na kukambilana mafunso aya.

      VIDIYO: Ndani Analemba Baibulo?—Mbali yake (2:48)

      • Ngati anthu ni amene analemba Baibo, n’cifukwa ciyani imachedwa Mawu a Mulungu?

      • Kodi mukhulupilila kuti zinacitikadi kuti Mulungu anaika maganizo ake mwa anthu olemba Baibo?

      Bwana akuuza kalembela maganizo ake kuti alembe, ndipo kalembelayo akulemba maganizowo m’kalata.

      Kalembela amalemba kalata, koma uthenga wa kalatayo umacokela kwa womuuza zolemba. Mofananamo, anthu analemba Baibo, koma uthenga wake unacokela kwa Mulungu

  • Baibo ni Uthenga wa Mulungu kwa Ife
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani