-
Muzikhulupilila Yehova Nthawi ZonseNsanja ya Mlonda—2015 | April 15
-
-
2 Zioneka kuti panthawi yovutayi ndi pamene Paulo anaikidwa m’ndende kaciŵili ku Roma. Kodi Akristu ena anapita kukamuthandiza? Paulo anada nkhawa kuti kulibe anamuthandiza, ndiye cifukwa cake analembela Timoteyo kuti: “Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha. Ngakhale zinali conco, usakhale mlandu kwa io.” Komabe, Paulo anadziŵa kuti sanali yekha. Iye analemba kuti: “Koma Ambuye anaima pafupi ndi ine ndi kundipatsa mphamvu.” Zoonadi, Ambuye Yesu anapatsa Paulo thandizo lofunikila. Kodi thandizolo linagwila nchito? Inde, cifukwa iye anati: “Ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.”—2 Tim. 4:16, 17.a
3 Kukumbukila zimenezi kuyenela kuti kunalimbikitsa Paulo kukhulupilila kuti Yehova adzamuthandiza kupilila mavuto amene anali kukumana nao, ndiponso amene akanakumana nao mtsogolo. Ndiye cifukwa cake iye anapitiliza kunena kuti: “Ambuye adzandipulumutsa ku coipa ciliconse.” (2 Tim. 4:18) Paulo anadziŵa kuti ngakhale kuti thandizo limene anthu angapeleke lingakhale losakwanila, thandizo limene Yehova ndi Mwana wake amapeleka limakhala lokwanila.
-
-
Muzikhulupilila Yehova Nthawi ZonseNsanja ya Mlonda—2015 | April 15
-
-
“M’KAMWA MWA MKANGO”
10-12. (a) Kodi Mkristu amene akusamalila wacibale amene ali ndi matenda aakulu angakumane ndi mavuto otani? (b) Kodi kukhulupilila Yehova panthawi ya mavuto kumalimbitsa bwanji ubwenzi wathu ndi iye? Pelekani citsanzo.
10 Mukakumana ndi mavuto aakulu mungaone ngati muli pafupi kugwidwa ndi mkango kapena muli kale “m’kamwa mwa mkango” monga mmene Paulo anamvelela. Panthawiyi kukhulupilila Yehova n’kofunika kwambili ngakhale kuti kucita zimenezi kumakhala kovuta. Mwacitsanzo, yelekezelani kuti mukusamalila wacibale wanu amene akudwala matenda aakulu. Mwina mumapemphela kwa Mulungu kuti akupatseni mphamvu ndi nzelu.b Popeza kuti mukucita zonse zimene mungathe, simuyenela kukaikila kuti Yehova akukuyang’anilani ndipo adzakuthandizani kuti mupilile.—Sal. 32:8.
-
-
Muzikhulupilila Yehova Nthawi ZonseNsanja ya Mlonda—2015 | April 15
-
-
a Mau akuti “m’kamwa mwa mkango” amene Paulo anagwilitsila nchito angatanthauze mkango weniweni kapena wophiphilitsila.
-