LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Khalani Woona Mtima pa Zinthu Zonse
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 3. Kodi pali mapindu otani tikakhala oona mtima?

      Tikadziŵika kukhala munthu woona mtima, anthu amatidalila. Tidzathandiza aliyense kudzimva wotetezeka mu mpingo monga banja lokondana. Komanso timakhala na cikumbumtima cabwino. Kuona mtima kwathu ‘kumakometselanso ciphunzitso ca mpulumutsi wathu, Mulungu.’ Ndiponso kumathandiza aja amene si mboni kufuna kum’tumikila Yehova.—Tito 2:10.

  • Cifukwa Cake Tiyenela Kusamala na Mavalidwe Komanso Maonekedwe Athu
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • 3. Kodi anthu ena angakopeke bwanji na kulambila koona cifukwa ca maonekedwe athu?

      Ngakhale kuti timayesetsa kuvala moyenela panthawi iliyonse, tiyenela kusamala kwambili maka-maka pokasonkhana ku mpingo, kapena polalikila. Sitifuna kunyozetsa uthenga wofunika kwambili umene timatengela anthu. M’malo mwake, timafuna kuti maonekedwe athu azikokela anthu ku coonadi, kotelo kuti “akometsele ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu.”—Tito 2:10.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani