LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Oyang’anila Oweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
    • 11 Abale oikidwa kukhala oyang’anila amaonetsa kuti ni odziletsa m’zocita zawo, komanso pocita zinthu na ena. Sacita zinthu mopitilila malile. Amadziŵika kukhala acikatikati, komanso a khalidwe lodziletsa. Ucikatikati wawo umaonekela pa zinthu monga kudya, kumwa, maseŵela, makonda ake, komanso zosangalatsa. Ni acikatikatinso pa nkhani ya moŵa, kuti asanenezedwe za kuledzela kapena ucidakwa. Munthu akakhuta moŵa, sakwanitsa kudziletsa bwino-bwino, ndipo sangathe kuyang’anila zinthu zauzimu za mpingo.

  • Oyang’anila Oweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
    • 13 Woyang’anila ayenela kukhala wololela. Ayenela kucita zinthu molimbikitsa mgwilizano pakati pawo monga akulu, komanso kucilikiza bungwe la akulu. Sayenela kudziona kukhala wofunika kuposa anzake, kapena kuyembekezela zambili kwa ena. Pokhala wololela, woyang’anila saumilila maganizo ake, kuona monga ndiye amaganiza bwino kuposa akulu anzake. Amazindikila kuti akulu ena angakhale na makhalidwe kapena maluso ena amene iye alibe. Mkulu amaonetsa kuti ni wololela ngati mfundo zake zimazikidwa pa Malemba, potengela citsanzo ca Yesu Khristu. (Afil. 2:2-8) Mkulu sayenela kukhala wokonda kukangana na anzake kapena waciwawa. Ayenela kuonetsa ulemu kwa ena, powaona kukhala omuposa. Sakhala na mzimu wa zimene ndanena-ndanena, nthawi zonse woumilila kuti ena atsatile maganizo ake. Asakhale wa mtima wapacala, (wokwiya msanga), koma wamtendele pocita zinthu na anthu ena.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani