LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kugonana?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • Phunzilo 41. Mwamuna na mkazi agwilana manja.

      PHUNZILO 41

      Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Kugonana?

      Anthu ambili amacita manyazi kukambilana nkhani ya kugonana. Koma Baibo ikamanena za kugonana imakamba mosapita m’mbali, komabe mwaulemu. Ndipo zimene imakamba zimakhala zaphindu kwa ife. Zimenezi n’zomveka cifukwa Yehova ndiye anatilenga. Iye amadziŵa zimene zingatipindulile bwino kwambili. Amatiuzanso zimene tiyenela kucita kuti timusangalatse, na zimene zingatithandize kuti tikondwele na moyo kwamuyaya.

      1. Kodi Yehova Amaiona bwanji nkhani ya kugonana?

      Kugonana ni mphatso yabwino kwambili imene Yehova anakonzela anthu. Iye amafuna kuti mwamuna na mkazi wake azisangalala nayo mphatso imeneyi. Mphatso ya kugonana imeneyi imalola okwatilana kubeleka ana. Komanso, ni njila imene aŵiliwo amaonetselana cikondi m’njila yoyenela yacibadwa, komanso yopatsa cisangalalo. Ndiye cifukwa cake Mawu a Mulungu amati: “Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.” (Miyambo 5:18, 19) Yehova amafuna kuti Akhristu okwatilana azikhala okhulupilika kwa wina na mnzake. Akatelo, adzapewelatu kucita cigololo.—Ŵelengani Aheberi 13:4.

      2. Kodi ciwelewele n’ciyani?

      Baibo imatiuza kuti “adama sadzaloŵa mu ufumu wa Mulungu.” (1 Akorinto 6:9, 10) Olemba Baibo mu Cigiriki anagwilitsa nchito liwu lakuti por-nei’a pofotokoza khalidwe la ciwelewele. Liwu lakuti por-nei’a limatanthauza (1) kugonanaa kwa anthu osakwatilana, (2) kugonana kwa anthu ofanana ziwalo (mathanyula), ndipo (3) kugona nyama. Ngati tipewa dama tidzakondweletsa Yehova, ndiponso tidzakhala na moyo waphindu.—1 Atesalonika 4:3.

      KUMBANI MOZAMILAPO

      Dziŵani mmene mungapewele zaciwelewele, komanso mapindu amene mungapeze ngati mukhala oyela m’makhalidwe.

      Yosefe akuthaŵa mkazi wa Potifara. Mkaziyo wagwila malaya a Yosefe.

      3. Thaŵani ciwelewele

      Mnyamata wina wokhulupilika, Yosefe, anakanitsitsa zakuti agone na mkazi wa mwiniwake pofuna kukhala woyela m’makhalidwe. Ŵelengani Genesis 39:1-12, na kukambilana mafunso aya:

      • N’ciyani cinalimbikitsa Yosefe kuti athaŵe? Onani vesi 9.

      • Kodi muganiza kuti Yosefe anapanga cisankho canzelu? Cifukwa ciyani?

      Kodi acinyamata masiku ano angatengele bwanji citsanzo ca Yosefe cothaŵa ciwelewele? Tambani VIDIYO.

      VIDIYO: Thawani Zaciwelewele (5:06)

      Yehova amafuna kuti tizipewa zaciwelewele. Ŵelengani 1 Akorinto 6:18, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi ni zocitika ziti zimene zingapangitse munthu kuti acite ciwelewele?

      • Kodi mungacithaŵe bwanji ciwelewele?

      4. Mukhoza kuwagonjetsa mayeselo

      Kodi n’ciyani cingapangitse kuti zikhale zovuta kupewa mayeselo ocita ciwelewele? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

      VIDIYO: Kulimbana na Mayeselo mwa Kuŵelenga Baibo (3:02)

      • Kodi m’bale wa mu vidiyo iyi, anacita ciyani atazindikila kuti maganizo ake na zocita zake zidzapangitsa kuti asakhale wokhulupilika kwa mkazi wake?

      Ngakhale kwa Akhristu okhulupilika, nthaŵi zina cimakhala covuta kusungabe maganizo awo ali oyela. Kodi mungacite ciyani kuti mupewe kumangoganizila zinthu zoipa? Ŵelengani Afilipi 4:8, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi tiyenela kumaika maganizo athu pa zinthu zotani?

      • Kodi kuŵelenga Baibo komanso kukhala wotangwanika potumikila Yehova, kungatithandize bwanji kuti tipewe mayeselo amene angaticimwitse?

      5. Malamulo a Yehova amatipindulitsa

      Yehova ndiye amadziŵa bwino zimene timafunikila. Iye amatiuza mmene tingakhalile na makhalidwe oyela komanso mapindu amene tingapeze tikatelo. Ŵelengani Miyambo 7: 7-27 kapena Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.

      VIDIYO : Wopanda Nzeru Mumtima (9:31)

      • Kodi wacinyamatayu anadziloŵetsa bwanji m’mayeselo? Onani Miyambo 7:8, 9.

      • Malinga na Miyambo 7:23, 26, khalidwe laciwelewele lingatigwetsele m’mavuto aakulu. Ngati tili na makhalidwe oyela, kodi tingapewe mavuto ati?

      • Kodi makhalidwe oyela angatithandize bwanji kukondwela na moyo kwamuyaya?

      Anthu ena amaona kuti zimene Baibo imakamba pa nkhani ya mathanyula, kapena kuti kugonana kwa anthu ofanana ziwalo, ni nkhanza. Koma Yehova Mulungu wacikondi amafuna kuti aliyense akondwele na moyo kwamuyaya. Kuti zimenezi zitheke tiyenela kusunga malamulo ake. Ŵelengani 1 Akorinto 6:9-11, na kukambilana funso ili:

      • Kwa Mulungu, kodi mathanyula ndiwo khalidwe lokha limene tiyenela kupewa?

      Kuti timukondweletse Mulungu, tonsefe tiyenela kupanga masinthidwe pa umoyo wathu. Ngati talimbikila kutelo, tidzapindula. Ŵelengani Salimo 19:8, 11, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi muganiza kuti malamulo a Yehova pa makhalidwe abwino ni ovuta kwambili kuwatsatila? N’cifukwa ciyani mwayankha conco?

      Zithunzi: 1. Mtsikana wokhumudwa wakhala pamodzi na cibwenzi cake. Iye akumwa moŵa komanso kukoka fodya na anzake mu nayitikalabu. 2. Mtsikana mmodzi-modziyo akuceza mwasangala na alongo mu Nyumba ya Ufumu.

      Yehova wathandiza anthu ambili kutsatila malamulo ake pa umoyo wawo. Inunso angakuthandizeni

      ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Palibe vuto anthu aŵili alionse kugonana, malinga ngati amakondana.”

      • Nanga inu muona bwanji?

      CIDULE CAKE

      Kugonana ni mphatso yabwino kwambili imene Yehova anapeleka kwa mwamuna na mkazi wake kuti azisangalala nayo.

      Mafunso Obweleza

      • Kodi ciwelewele cimaphatikizapo macitidwe otani?

      • Kodi n’ciyani cingatithandize kupewa mcitidwe waciwelewele?

      • Kodi timapindula bwanji ngati titsatila malamulo a Yehova pa makhalidwe abwino?

      Colinga

      FUFUZANI

      Onani cifukwa cake Mulungu amafuna kuti mwamuna na mkazi azimangitsa ukwati, m’malo mongotengana cabe.

      “Kodi Baibulo Limavomereza Kuti Mwamuna ndi Mkazi Azikhalira Limodzi Asanakwatirane?”(Nkhani ya pawebusaiti)

      Onani cifukwa cake mfundo ya m’Baibo yoletsa mathanyula siitanthauza kuti anthuwo tizidana nawo.

      “Kodi Kugonana Kwa Amuna Kapena Akazi Okhaokha N’kolakwika?” (Nkhani ya pawebusaiti)

      Dziŵani mmene malamulo a Mulungu pa nkhani ya kugonana amatitetezela.

      “Kodi Kugonana M’kamwa Kumakhaladi Kugonana?” (Nkhani ya pawebusaiti)

      Mu nkhani yakuti “Anandilandira Mwaulemu Kwambiri,” Onani cinalimbikitsa mwamuna wina wocita zamathanyula kusintha moyo wake kuti akondweletse Mulungu.

      “Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, April 1, 2011)

      a Macitidwe osayenela amenewa amaphatikizapo kugonana m’kamwa, kugonana kumbuyo, komanso kuseŵeletsa malisece a munthu wina.

  • Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Umbeta na Ukwati?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
    • Phunzilo 42. Mlongo amene ni mbeta, komanso aŵili okwatilana, akuceza mosangalala pamalo odyela.

      PHUNZILO 42

      Kodi Baibo Imati Ciyani pa Nkhani ya Umbeta na Ukwati?

      Ku madela ena, anthu amakhulupilila kuti munthu angakhale wosangalala kokha ngati waloŵa m’banja. Komabe, sikuti onse ali pa banja ali na cimwemwe, komanso sikuti mbeta zonse zilibe cimwemwe. Ndiye cifukwa cake Baibo imaonetsa kuti umbeta, komanso ukwati, zonse ni mphatso zocokela kwa Mulungu.

      1. Kodi umbeta uli na mapindu otani?

      Baibo imati: “Amene walekana ndi moyo wokhala yekha n’kulowa m’banja wacita bwino, koma amene sanalowe m’banja wacita bwino koposa.” (Ŵelengani 1 Akorinto 7:32, 33, 38.) Kodi munthu amene ni mbeta amacita “bwino koposa” pa mbali ziti? Akhristu amene ni mbeta amakhala alibe nkhawa yosamalila zosoŵa za mnzawo wa mu ukwati. Motelo, iwo amakhala na ufulu wokulilapo. Mwacitsanzo, ena amawonjezela utumiki wawo m’njila zosangalatsa, monga kupita ku madela ena kukathandiza nchito yolalikila uthenga wabwino. Coposa zonse, iwo amakhala na nthawi yoculuka yolimbitsa ubwenzi wawo na Yehova.

      2. Kodi kukwatilana mwalamulo kuli na mapindu otani?

      Monga mmene zilili na umbeta, ukwati nawonso umabweletsa mapindu abwino kwambili. Baibo imakamba kuti “awili amaposa mmodzi.” (Mlaliki 4:9) Mfundo imeneyi ni yoona maka-maka kwa Akhristu amene amagwilitsa nchito mfundo za m’Baibo mu ukwati wawo. Okwatilana mwalamulo amalonjezana kuti adzakondana, kulemekezana, komanso kusamalilana wina na mnzake. Cifukwa ca zimenezi, iwo amadzimva otetezeka kuposa aja amene amangotengana osamangitsa ukwati. Komanso ukwati walamulo umakhala malo otetezeka olelelamo ana.

      3. Kodi Yehova amauona bwanji ukwati?

      Yehova pomangitsa ukwati woyamba anati: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake.” (Genesis 2:24) Yehova amafuna kuti mwamuna na mkazi wake azikondana na kukhalila limodzi kwa moyo wawo wonse. Iye amalola kusudzulana pokhapo ngati mmodzi wa aŵiliwo wacita cigololo. Zikatelo, Yehova amalola wolakwilidwayo kusankha kuthetsa ukwatiwo kapena ayi.a (Mateyu 19:9) Cina, Yehova salola kuti Akhristu azikwatila cipali.—1 Timoteyo 3:2.

      KUMBANI MOZAMILAPO

      Onani mmene mungakhalile wacimwemwe komanso wokondweletsa Yehova, kaya ndinu mbeta kapena muli pabanja.

      4. Igwilitseni nchito mwanzelu mphatso ya umbeta

      Yesu anaona kuti umbeta ni mphatso. (Mateyu 19:11, 12) Ŵelengani Mateyu 4:23, na kukambilana funso ili:

      • Kodi Yesu anaseŵenzetsa bwanji mphatso ya umbeta wake, kutumikila Atate wake komanso kuthandiza anthu ena?

      Akhristu amene ni mbeta akhoza kusangalala na umoyo wawo mmene Yesu anacitila. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.

      VIDIYO: Akhristu Okhulupilika Omwe Sali Pabanja (3:11)

      • Kodi Akhristu amene ni mbeta angaseŵenzetse bwanji mphatso yawo imeneyo mwaphindu?

      Kodi mudziŵa?

      Baibo siikamba zaka zakubadwa zimene munthu ayenela kufikapo kuti aloŵe m’banja. Ngakhale n’conco, imalimbikitsa munthu kuti ayambe wayembekeza mpaka apitilile “pacimake pa unyamata.” Pacimake pa unyamata ni nyengo pamene cilakolako ca kugonana cimakhala camphamvu kwambili cakuti cingalepheletse wacinyamata kupanga zisankho zanzelu.—1 Akorinto 7:36.

      5. Sankhani mwanzelu munthu wokwatilana naye

      Kusankha munthu womanga naye banja ni nkhani yaikulu kwambili. Ŵelengani Mateyu 19:4-6, 9, na kukambilana funso ili:

      • N’cifukwa ciyani Mkhristu sayenela kuthamangila kuloŵa m’banja?

      Baibo ingakuthandizeni kudziŵa makhalidwe abwino a munthu amene mungakwatilane naye. Koma cofunika kwambili ni kupeza munthu amene amakonda Yehova.b Ŵelengani 1 Akorinto 7:39 na 2 Akorinto 6:14. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:

      • N’cifukwa ciyani tiyenela kukwatilana na Mkhristu mnzathu cabe?

      • Kodi muganiza kuti Yehova angamve bwanji tikakwatilana na munthu amene sakonda Mulungu?

      Nkhunzi yamphamvu na bulu wamng’ono, zonse zikuvutika m’joko.

      Mukamanga mujoko nyama ziŵili zosiyana kwambili, zonse zidzavutika. Mofananamo Mkhristu akamanga ukwati na munthu wosakhulupilila, adzakhala na mavuto ambili

      6. Kuona ukwati mmene Yehova amauonela

      Mu nthawi ya Aisiraeli akale, amuna ena anali kusudzula akazi awo pa zifukwa zadyela. Ŵelengani Malaki 2:13, 14, 16, na kukambilana funso ili:

      • N’cifukwa ciyani Yehova amadana nako kuthetsa ukwati pa zifukwa zisali za m’Malemba?

      Mayi wosweka mtima akuyang’ana mwamuna wake akucokelatu pakhomo. Mtsikana wawo wokhumudwa akukumbatila mayi ake.

      Cigololo na kusudzulana zimam’pweteka kwambili wa mu ukwati wosalakwayo komanso ana awo

      Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.

      VIDIYO: Cikwati Ni Mgwilizano wa Moyo Wonse (4:30)

      • Ngati muli pa banja na munthu wosakhulupilila, kodi mungacite ciyani kuti ukwati wanu ukhale wopambana?

      7. Sungani malamulo a Yehova mu ukwati wanu

      Pafunikila khama kuti munthu azitsatila malamulo a Yehova mu ukwati.c Ndipo Yehova amadalitsa amene amayesetsa kutelo. Tambani VIDIYO.

      VIDIYO: Mukhoza Kusunga Malamulo a Yehova a Ukwati (4:14)

      Ŵelengani Aheberi 13:4, na kukambilana mafunso aya:

      • Kodi muganiza n’zotheka kutsatila malamulo a Yehova a mu ukwati? Mwayankha conco cifukwa ciyani?

      Yehova amafuna kuti Akhristu akakwatilana kapena kusudzulana azilembetsa ku boma. M’maiko ambili, izi n’zimene malamulo amafuna. Ŵelengani Tito 3:1, na kukambilana funso ili:

      • Ngati muli pabanja, kodi mukutsimikiza kuti ukwati wanu ni wolembetsa ku boma?

      MUNTHU WINA ANGAFUNSE KUTI: “N’kwanji kumangitsa ukwati? Kodi mwamuna na mkazi sangangotengana n’kumakhalila limodzi?”

      • Kodi inu mungayankhe bwanji?

      CIDULE CAKE

      Umbeta komanso ukwati, zonse ni mphatso zocokela kwa Yehova. Anthu ali pabanja komanso mbeta, onse akhoza kukhala na umoyo wacimwemwe, malinga ngati acita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Yehova.

      Mafunso Obweleza

      • Kodi munthu ayenela kucita motani kuti agwilitsile nchito mphatso yake ya umbeta mwanzelu?

      • N’cifukwa ciyani Baibo imatilangiza kukwatilana na Mkhristu mnzathu cabe?

      • Kodi pali cifukwa cimodzi cokha citi ca m’Malemba colola kuthetsa ukwati?

      Colinga

      FUFUZANI

      Kodi kukwatila kokha “mwa Ambuye” kutanthauza ciyani?

      “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” (Nsanja ya Mlonda, July 1, 2004)

      Tambani mavidiyo aŵili amene angakuthandizeni kupanga zisankho zabwino pa nkhani ya kukhala pacibwenzi komanso ukwati.

      Kukonzekera Banja (11:53)

      Onani cifukwa cake m’bale wina akuona kuti zimene Yehova wam’patsa n’zamtengo wapatali kuposa ciliconse cimene anasiya.

      N’naganiza Kuti Mtsikanayo Angaphunzile Coonadi (1:56)

      Ni zinthu ziti zimene munthu ayenela kuganizilapo mosamala asanapange cisankho ca kusudzulana kapena kusalana na mnzake wa mu ukwati?

      “Muzilemekeza ‘Cimene Mulungu Wacimanga Pamodzi’” (Nsanja ya Mlonda, December 2018)

      a Onani Mfundo yakumapeto 4 pa nkhani ya kusalana apaukwati (separation) ngati sipanacitike cigololo.

      b Kumadela ena, makolo ndiwo amasankhila mwana wawo munthu wokwatilana naye. Zikakhala conco, makolo acikondi sayang’ana cuma cimene munthu ali naco, kapena kuchuka kwake iyayi. M’malo mwake, amafuna kudziŵa ngati munthuyo amakonda Yehova.

      c Ngati munangotengana cabe na munthu amene simunamange naye ukwati, muyenela kupanga cisankho inu mwini, cokamangitsa naye ukwati kapena kusiyana naye.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani