-
Kodi Baibo Imakamba Ciyani pa Zanchito Komanso Ndalama?Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
2. Kodi ndalama tiyenela kuziona bwanji?
Baibo imavomeleza kuti ‘ndalama zimateteza.’ Koma imaticenjezanso kuti ndalama pazokha sizingatipatse cimwemwe. (Mlaliki 7:12) Mwa ici, timalangizidwa kusakonda ndalama, koma kukhala ‘okhutila na zimene tili nazo panthawiyo.’ (Ŵelengani Aheberi 13:5.) Tikamakhala okhutila na zimene tili nazo, timapewa msampha wofuna-funa ndalama nthawi zonse. Timapewanso nkhongole zosafunikila. (Miyambo 22:7) Ndiponso timapewa njuga na zoopsa zake, komanso mabizinesi ofuna kulemela msanga-msanga.
-
-
Kodi Baibo Imakamba Ciyani pa Zanchito Komanso Ndalama?Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
-
-
5. Tikakhutila na zimene tili nazo timapindula
Anthu oculuka amayesa kudziunjikila ndalama zambili-mbili. Koma Baibo imalimbikitsa zosiyana. Ŵelengani 1 Timoteyo 6:6-8, na kukambilana funso ili:
Kodi Baibo imatilimbikitsa kucita ciyani?
Olo tikhale na zocepa tingakhale acimwemwe. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.
Olo kuti mabanja aya alibe ndalama zambili, n’ciyani cimawapangitsa kukhala acimwemwe?
Koma bwanji ngati tili nazo kale zambili koma tikufunanso zowonjezela? Yesu anapeleka fanizo loonetsa kuopsa kwa zimenezi. Ŵelengani Luka 12:15-21, na kukambilana funso ili:
Kodi mwaphunzila ciyani m’fanizo la Yesu? —Onani vesi 15.
Ŵelengani na kuyelekezela Miyambo 10:22 na 1 Timoteyo 6:10. Ndiyeno kambilanani mafunso aya:
Kodi muganiza cofunika kwambili n’ciyani? Kukhala pa ubwenzi na Yehova kapena kukhala na ndalama zambili? Mwayankha conco cifukwa ciyani?
Kodi kufuna-funa ndalama nthawi zonse, kumabweletsa mavuto otani?
-