-
Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Zimene MuyembekezelaNsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2016 | October
-
-
2 Nawonso anthu amene ali kumbali ya dziko la Satana amakhala na ciyembekezo, koma amakayikila ngati zimene akuyembekezela zingacitike. Mwacitsanzo, ochova njuga mamiliyoni ambili amayembekezela kuti tsiku lina adzawina ndalama zambili, koma sakhala otsimikiza kuti angawinedi. Komabe, cikhulupililo ceni-ceni ni “ciyembekezo cotsimikizika” cimene Akhiristu ali naco. (Aheb. 11:1) Mwina mungadzifunse kuti, kodi ciyembekezo cingakhale bwanji cotsimikizika? Nanga ni mapindu abwanji amene mungapeze ngati mwakhala na cikhulupililo colimba pa zimene muyembekezela?
3. Kodi cikhulupililo ca Mkhiristu woona cimazikidwa pa mfundo iti?
3 Cikhulupililo si khalidwe limene anthu ocimwa amabadwa nalo, ndipo silibwela lokha. Mzimu woyela wa Mulungu ndiwo umathandiza Mkhiristu kukhala na cikhulupililo. (Agal. 5:22) Baibo sikamba kuti Yehova ali na cikhulupililo kapena kuti afunika kukhala na cikhululupilo. Popeza Yehova ni Wamphamvuyonse ndipo ni wanzelu zonse, palibe cingamulepheletse kukwanilitsa malonjezo ake. Atate wathu Wakumwamba ndi wotsimikiza kuti adzakwanilitsadi malonjezo ake, ndipo kwa iye zili ngati kuti akwanilitsidwa kale. Ndiye cifukwa cake anakamba kuti: “Zakwanilitsidwa!” (Ŵelengani Chivumbulutso 21:3-6.) Cikhulupililo ca Mkhiristu cimazikidwa pa mfundo yakuti Yehova ni “Mulungu wokhulupilika,” amene amakwanilitsa zimene walonjeza.—Deut. 7:9.
PHUNZILANI PA ZITSANZO ZA ANTHU AKALE ACIKHULUPILILO
4. Ni ciyembekezo canji cimene amuna ndi akazi akale acikhulupililo anali naco?
4 Chaputa 11 ca buku ya Aheberi cimachula maina 16 a amuna ndi akazi amene anali na cikhulupililo. Wolemba buku limeneli anakamba za iwo ndi ena kuti “anacitilidwa umboni cifukwa ca cikhulupililo cawo.” (Aheb. 11:39) Onse anali na “ciyembekezo cotsimikizika” cakuti Mulungu adzapeleka mbeu imene idzaphwanya Satana na kukwanilitsa colinga cake ca poyamba. (Gen. 3:15) Pamene Yesu Khiristu, amene ni “mbeu” yolonjezedwa, anatsegula njila yamoyo wakumwamba, anthu okhulupilika amenewa anali atafa kale. (Agal. 3:16) Koma cifukwa cakuti Yehova salephela kukwanilitsa malonjezo ake, anthu amenewa adzaukitsidwa na kukhala ndi moyo wangwilo m’paradaiso padziko lapansi.—Sal. 37:11; Yes. 26:19; Hos. 13:14.
-
-
Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Zimene MuyembekezelaNsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2016 | October
-
-
7. Kuti atithandize kukhala na cikhulupililo colimba, Yehova watipatsa ciani mokoma mtima? Nanga tifunika kucita nazo bwanji?
7 Pofuna kutithandiza kuti tikhalebe na cikhulupililo colimba, Yehova mokoma mtima watipatsa mau ake Baibo. Kuti tikhale osangalala ndi kuti zinthu ‘zitiyendele bwino,’ tifunika kuŵelenga Mau a Mulungu tsiku lililonse ngati zingatheke. (Sal. 1:1-3; ŵelengani Machitidwe 17:11.) Ndiyeno, mofanana ndi alambili a Yehova akale, tifunika kupitiliza kusinkha-sinkha malonjezo a Mulungu ndi kumvela malamulo ake. Ifenso Yehova watidalitsa. Iye amatipatsa cakudya cauzimu coculuka kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Conco, ngati tiyamikila zimene tiphunzila m’zofalitsa zimene Yehova watipatsa, tidzafanana ndi anthu okhulupilika akale amene anali na “ciyembekezo cotsimikizika” ca Ufumu.
-