LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ‘Mulungu Anakondwela Naye’
    Nsanja ya Mlonda (Yogawila)—2017 | No. 1
    • “ANASAMUTSIDWA KUTI ASAFE MOZUNZIKA”

      Kodi Inoki anafa bwanji? Tingakambe kuti imfa yake inali yodabwitsa kwambili komanso yocititsa cidwi kuposa umoyo wake. Buku la Genesis limakamba cabe kuti: “Inoki anayendabe ndi Mulungu woona. Kenako iye sanaonekenso, cifukwa Mulungu anam’tenga.” (Genesis 5:24) Kodi Mulungu anatenga Inoki m’njila yabwanji? Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Mwa cikhulupililo, Inoki anasamutsidwa kuti asafe mozunzika, moti sanapezeke kwina kulikonse cifukwa Mulungu anamusamutsa. Pakuti asanasamutsidwe, Mulungu anamucitila umboni kuti akukondwela naye.” (Aheberi 11:5) Kodi mtumwi Paulo anatanthauza ciani pamene anakamba kuti Inoki “anasamutsidwa kuti asafe mozunzika”? Mabaibo ena amakamba kuti Mulungu anatenga Inoki kupita naye kumwamba. Koma zimenezo si zoona. Takamba conco cifukwa Baibo imaonetsa kuti Yesu Khiristu ndiye anali woyamba kuukitsidwa kuti akakhale kumwamba.—Yohane 3:13.

      Nanga Baibo itanthauza ciani pamene ikamba kuti Inoki “anasamutsidwa kuti asafe mozunzika”? Yehova ayenela kuti anacotsa moyo wa Inoki pang’no-pang’ono kuti asaphedwe mwankhanza ndi adani ake. Koma izi zikalibe kucitika, “Mulungu anamucitila umboni kuti akukondwela naye.” Kodi Mulungu anacita bwanji zimenezo? Inoki atatsala pang’ono kufa, mwina Mulungu anamuonetsa masomphenya a dziko lapansi la paradaiso. Inoki anagona mu imfa ali na umboni umenewu wakuti Yehova akukondwela naye. Polemba za Inoki komanso amuna ndi akazi ena okhulupilika, mtumwi Paulo anati: “Onsewa anafa ali ndi cikhulupililo.” (Aheberi 11:13) N’kutheka kuti pambuyo pake, adani a Inoki anafuna-funa mtembo wake, koma ‘sanaupeze kwina kulikonse.’ Mwina Yehova anabisa mtembo wa Inoki n’colinga cakuti anthu asauseŵenzetse pocilikiza kulambila konama, kapena kuugwilitsila nchito m’njila zina zolakwika.b

      Mogwilizana ndi mfundo za m’Malemba zimenezi, tiyeni tiyelekezele kuti tikuona mmene moyo wa Inoki unathela. Koma tikumbukile kuti zimenezi n’zongoyelekezela cabe. Iye anali kuthawa ndipo analema ngako. Adani ake anali kumupitikitsa ali wokwiya kwambili cifukwa ca uthenga wake wa ciweluzo. Ndiyeno, Inoki anapeza malo obisalapo ndipo anapumula kwa kanthawi, koma anadziŵa kuti adaniwo amupezabe. Anadziŵanso kuti watsala pang’ono kuphedwa mwankhanza. Conco, pamene anali kupumula anapemphela kwa Mulungu wake. Atapemphela, mtima wake unakhala pansi. Ndiyeno, Inoki anaona masomphenya ocititsa cidwi. Zimene anaona zinali kuoneka monga zeni-zeni cakuti anaiwalilatu mavuto onse amene anali kukumana nawo.

      Inoki wabisala m’phanga ndipo adani ake apitilila

      Inoki ayenela kuti anali pafupi kuphedwa mwankhanza na adani ake pamene Yehova anamusamutsa

      N’kutheka kuti m’masomphenyawo, iye anaona dziko losiyana kwambili na limene anali kukhalamo. Dzikolo linali lokongola monga munda wa Edeni. Koma munalibe akerubi oletsa anthu kuloŵamo. M’dzikolo munali amuna ndi akazi ambili, ndipo onse anali athanzi ndi amphamvu. Iwo anali kukhala mwamtendele. Munalibe cidani kapena anthu ozunza anzawo cifukwa ca cipembedzo, zinthu zimene zinali zofala m’nthawi ya Inoki. Ataona zimenezi, Inoki anazindikila kuti Yehova amam’konda ndi kukondwela naye. Iye anadziŵa kuti dziko limenelo ndiwo malo abwino amene anafunika kukhalamo, ndiponso kuti mtsogolo kudzakhala kwawo kweni-kweni. Pamene mtendele wa m’maganizo mwake unali kuwonjezeleka, Inoki anagona tulo twa imfa.

      Inoki ni wakufa mpaka lelo, koma Yehova, Mulungu amene amakwanitsa kukumbukila ciliconse, akali kumukumbukilabe. Monga mmene Yesu analonjezela, tsiku lidzafika pamene onse amene Mulungu akuwakumbukila adzamva mau a Khiristu, ndipo adzauka ndi kukhala m’dziko lokongola ndi lamtendele.—Yohane 5:28, 29.

  • ‘Mulungu Anakondwela Naye’
    Nsanja ya Mlonda (Yogawila)—2017 | No. 1
    • b N’zimenenso Mulungu anacita ndi mtembo wa Mose ndi wa Yesu. Iye anaonetsetsa kuti mitembo yawo ndi yotetezeka n’colinga cakuti anthu asaiseŵenzetse molakwika.—Deuteronomo 34:5, 6; Luka 24:3-6; Yuda 9.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani