LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Kodi Mukuyembekezela “Mzinda Wokhala Ndi Maziko Eni-eni”?
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2020 | August
    • Abulahamu akuthandiza Sara kutsika pa ngamila. Kumbuyo kwake, atumiki ake angapo akugwila nchito zawo za tsiku na tsiku.

      Kodi Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali kukhulupilila malonjezo a Yehova? (Onani ndime 5)

      5. Tidziŵa bwanji kuti Abulahamu anali kuyembekezela mzinda wokhazikitsidwa na Mulungu?

      5 Kodi Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali kuyembekezela mzinda, kapena kuti Ufumu wokhazikitsidwa na Mulungu? Coyamba, iye sanakhale nzika ya ufumu uliwonse pano padziko lapansi. Abulahamu anali kusamuka-samuka. Anasankha kusakhala pamalo amodzi, ndiponso sanacilikize mfumu iliyonse ya umunthu. Kuwonjezela apo, iye sanayese kukhazikitsa ufumu wake-wake. M’malomwake, anapitiliza kumvela Yehova na kumuyembekezela kuti adzakwanilitsa lonjezo lake. Mwa kucita zimenezi, Abulahamu anaonetsa kuti anali na cikhulupililo cacikulu mwa Yehova. Tsopano, tiyeni tikambilane mavuto ena amene iye anakumana nawo, na kuona zimene tingaphunzilepo pa citsanzo cake.

  • Kodi Mukuyembekezela “Mzinda Wokhala Ndi Maziko Eni-eni”?
    Nsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2020 | August
    • 7. N’cifukwa ciani Abulahamu anafunika kudalila Yehova kuti adzamuteteza pamodzi na banja lake?

      7 Abulahamu anafunika kudalila Yehova kuti adzamuteteza pamodzi na banja lake. Cifukwa ciani? Kumbukilani kuti iye na Sara anasiya nyumba yabwino komanso yotetezeka mu mzinda wa Uri, n’kukakhala ku dela la kumidzi ku Kanani. Kumeneko, Abulahamu na banja lake sanalinso otetezeka cifukwa kunalibe mipanda kapena ngalande zakuya zamadzi. Apa zinali zosavuta adani kuwaukila.

      8. Kodi Abulahamu panthawi ina anakumana na vuto lotani?

      8 Abulahamu anali kucita cifunilo ca Mulungu. Ngakhale n’conco, pa nthawi ina anasoŵa cakudya copatsa banja lake. Anavutika na njala yoopsa imene inagwa m’dziko la Kanani limene Yehova anamuuza kuti akakhalemo. Njalayo inafika poipa kwambili moti Abulahamu anasamuka pamodzi na banja lake n’kukakhala ku Iguputo kwa kanthawi. Koma ali kumeneko, wolamulila wa dzikolo Farao, anatenga mkazi wa Abulahamu kuti akhale wake. Tangoganizilani nkhawa imene Abulahamu anali nayo. Koma nkhawa imeneyo inatha pamene Yehova analamula Farao kuti abweze Sara kwa Abulahamu.—Gen. 12:10-19.

      9. Ni mavuto ati a m’banja amene Abulahamu anakumana nawo?

      9 Cinanso, m’banja la Abulahamu munali mavuto. Mkazi wake wokondedwa Sara sanali kubeleka. Kwa zaka zambili, iwo anangolipilila vuto limeneli. Potsilizila pake, Sara anapeleka mdzakazi wake Hagara kwa Abulahamu kuti awabelekele ana. Koma Hagara atakhala na pakati pa Isimaeli, anayamba kupeputsa Sara. Zinthu zinafika povuta kwambili cakuti Sara anathamangitsa Hagara panyumbapo.—Gen. 16:1-6.

      10. Ni zocitika ziti zokhudza Isimaeli na Isaki zimene zikanapangitsa kuti cikhale covuta kwa Abulahamu kukhulupilila Yehova?

      10 Pamapeto pake, Sara anakhala na pakati, ndipo anabelekela Abulahamu mwana wamwamuna amene anamucha Isaki. Abulahamu anali kuwakonda ana ake onse aŵili, Isimaeli na Isaki. Koma cifukwa cakuti Isimaeli anali kucitila nkhanza Isaki, Abulahamu anakakamizika kucotsa Isimaeli na Hagara panyumbapo. (Gen. 21:9-14) Patapita zaka zambili, Yehova analamula Abulahamu kuti amupeleke nsembe Isaki. (Gen. 22:1, 2; Aheb. 11:17-19) Pa zocitika zonsezi, Abulahamu anali kukhulupilila kuti Yehova adzakwanilitsa zimene analonjeza zokhudza ana ake.

      11. N’cifukwa ciani Abulahamu anafunika kuyembekezela Yehova moleza mtima?

      11 Panthawi yonseyi, Abulahamu anaphunzila kuyembekezela Yehova moleza mtima. Iye ayenela kuti anali na zaka zoposa 70 pamene anacoka mumzinda wa Uri pamodzi na banja lake. (Gen. 11:31–12:4) Ndipo kwa zaka pafupi-fupi 100, anali kukhala m’matenti m’madela osiyana-siyana a dziko la Kanani. Abulahamu anamwalila ali na zaka 175. (Gen. 25:7) Koma iye sanaone kukwanilitsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti adzapeleka dziko limene anayendamo kwa mbadwa zake. Ndipo anafa asanaone mzinda kapena kuti Ufumu umene Mulungu anakhazikitsa. Ngakhale n’conco, Malemba amati Abulahamu anamwalila ali “wokalamba, . . . ndi wokhutila.” (Gen. 25:8) Ngakhale kuti iye anakumana na mavuto ambili, anakhalabe na cikhulupililo colimba ndiponso anayembekezela Yehova mwacimwemwe. Kodi anakwanitsa bwanji kupilila? Anakwanitsa cifukwa pa umoyo wake wonse, Yehova anali kumuteteza na kumusamalila monga bwenzi lake.—Gen. 15:1; Yes. 41:8; Yak. 2:22, 23.

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani