LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • Tsanzilani Cikhulupililo ca Mose
    Nsanja ya Mlonda—2014 | April 1
    • 1, 2. (a) Kodi Mose anapanga cosankha cotani ali ndi zaka 40? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) N’cifukwa ciani Mose anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu?

      MOSE anadziŵa kuti akanakhala ndi tsogolo labwino m’dziko la Iguputo. Dzikolo linali ndi nyumba zazikulu zokongola ndipo linali lotukuka. Iye anakulila m’banja lacifumu ndipo “anaphunzila nzelu zonse za Aiguputo.” Mwacionekele, iye anaphunzila luso losiyanasiyana, zinthu zakuthambo, masamu, ndi sayansi. (Mac. 7:22) Zikanakhala zosavuta kuti iye akhale ndi cuma, ulamulilo ndi udindo, zinthu zimene Aiguputo ena sakanakhala nazo.

      2 Komabe, ali ndi zaka 40, Mose anapanga cosankha cimene cinadabwitsa banja lacifumu laciiguputo limene linali kum’sunga. Iye sanasankhe ngakhale umoyo wa Aiguputo wamba, koma anasankha kukhala pamodzi ndi akapolo. N’cifukwa ciani anasankha zimenezo? Cifukwa cakuti Mose anali ndi cikhulupililo. (Ŵelengani Aheberi 11:24-26.) Cifukwa ca cikhulupililo, Mose sanaike maganizo ake pa zinthu zooneka ndi maso. Iye anali kukhulupililabe “Wosaonekayo,” Yehova, ndi malonjezo ake.—Aheb. 11:27.

  • Tsanzilani Cikhulupililo ca Mose
    Nsanja ya Mlonda—2014 | April 1
    • 4. Kodi Mose anazindikila ciani pankhani ya ‘zosangalatsa zaucimo’?

      4 Cifukwa ca cikhulupililo, Mose anazindikila kuti ‘zosangalatsa zaucimo’ zinali zosakhalitsa. Mwina anthu ena anadabwa kuona kuti dziko la Iguputo, mmene anthu anali kucita zamatsenga ndi kukhulupilila mizimu, linakhala ufumu wamphamvu padziko lonse koma anthu a Yehova anali akapolo m’dzikolo. Komabe, Mose anali ndi cidalilo cakuti Mulungu akanasintha zinthu. Ngakhale kuti anthu amene anali kufuna kukhutilitsa zilakolako zao zinthu zinali kuwayendela bwino, Mose anali kukhulupilila kuti oipa adzaonongedwa. Conco, iye sananyengedwe ndi ‘zosangalatsa zosakhalitsa zaucimo.’

      5. N’ciani cingatithandize kukaniza ‘zosangalatsa zosakhalitsa zaucimo’?

      5 Kodi tingakanize bwanji ‘zosangalatsa zosakhalitsa zaucimo’? Tiyenela kudziŵa kuti zosangalatsa zaucimo n’zosakhalitsa. Cikhulupililo cidzatithandiza kudziŵa kuti “dziko likupita limodzi ndi cilakolako cake.” (1 Yoh. 2:15-17) Ndipo tiyenela kukumbukila zimene zidzacitikila anthu ocimwa osalapa. Iwo ali ‘pamalo otelela . . . mapeto ao ndi oopsa.’ (Sal. 73:18, 19) Mukayesedwa kuti mucite chimo, dzifunseni kuti, ‘Kodi zimenezi zidzakhudza bwanji tsogolo langa?’

Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
Tulukani
Loŵani
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani