-
Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Zimene MuyembekezelaNsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2016 | October
-
-
10. Ni zitsanzo ziti za atumiki a Mulungu amene sanataye cikhulupililo? Nanga n’ciani cinawalimbikitsa kucita zimenezo?
10 M’caputa 11 ca Aheberi, mtumwi Paulo anachula mayeselo amene atumiki a Mulungu ambili osachulidwa maina anapilila. Mwacitsanzo, mtumwiyu anakamba za akazi acikhulupililo amene ana awo anafa. Pambuyo pake anawalandilanso pamene anaukitsidwa. Ndiyeno, anakambanso za anthu amene “sanalole kusiya cikhulupililo cawo kuti amasulidwe. Iwo anacita zimenezi kuti adzauke kwa akufa, komwe ndi kuuka kwabwino kwambili.” (Aheb. 11:35) Ngakhale kuti sindife otsimikiza za anthu amene Paulo anali kukamba, ena monga Naboti na Zekariya, anaphedwa mwa kuponyedwa miyala cifukwa comvela Mulungu ndi kucita cifunilo cake. (1 Maf. 21:3, 15; 2 Mbiri 24:20, 21) Danieli na anzake anali na ufulu wosankha kusiya cikhulupililo cawo kuti amasulidwe. Koma cikhulupililo cawo mu mphamvu za Mulungu, cinawacititsa ‘kutseka mikango pakamwa’ ndi ‘kugonjetsa mphamvu ya moto, titelo kukamba kwake.’—Aheb. 11:33, 34; Dan. 3:16-18, 20, 28; 6:13, 16, 21-23.
-
-
Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Zimene MuyembekezelaNsanja ya Mlonda (Yophunzila)—2016 | October
-
-
12. N’ndani anapeleka citsanzo copambana pa kupilila mayeselo? Ndipo n’ciani cinam’thandiza?
12 Pambuyo pochula amuna ndi akazi osiyana-siyana okhulupilika, Paulo anaunika citsanzo copambana onse—Ambuye wathu Yesu Khiristu. Pa Aheberi 12:2 pamati: “Cifukwa ca cimwemwe cimene anamuikila patsogolo pake, anapilila mtengo wozunzikilapo. Iye sanasamale kuti zocititsa manyazi zimucitikila, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu.” Zoona, tifunika ‘kuganizila mozama’ citsanzo ca kukhulupilika kwa Yesu pokumana na mayeselo osiyana-siyana. (Ŵelengani Aheberi 12:3.) Mofanana ndi Yesu, Akhiristu oyambilila amene anafela cikhulupililo, monga wophunzila Antipa, sanagonje pa cikhulupililo cawo. (Chiv. 2:13) Iwo anali kuyembekezela mphoto yaciukililo ca moyo wakumwamba. Mphoto imeneyo inali yoposa “kuuka kwabwino kwambili,” kumene amuna akale okhulupilika anali kuyembekezela. (Aheb. 11:35) Pambuyo pa kukhadzikitsidwa kwa Ufumu mu 1914, odzozedwa okhulupilika onse amene anali m’manda anaukitsidwa ku moyo wauzimu kumwamba kuti akathandizane na Yesu kulamulila anthu padziko.—Chiv. 20:4.
-