NYIMBO 4
‘Yehova ni M’busa Wanga’
Yopulinta
(Salimo 23)
1. Yehova ni M’busa wanga,
Ine nidzam’tsatila.
Amadziŵa zonse nifuna;
Amanisamalila.
Nikakhala na mavuto
Iye anithandiza.
Poyenda amanitsogolela,
Kumalo a mtendele.
Iye amanitsogolela
Kumalo a mtendele.
2. Njila zanu M’busa wanga
Zimanitsitsimula.
Conde ine nitetezeni
Kuti nisasocele.
Poyenda m’zigwa za mdima,
Sinidzayopa kanthu.
Yehova ndinudi Bwenzi langa,
Ine sinidzayopa.
Bwenzi langa ndinu Yehova,
Ine sinidzayopa.
3. M’lungu ndinu M’busa wanga,
Nidzakulondolani.
Inu mumanipatsa mphamvu;
Mumanilimbikitsa.
Zonse ndinu munipatsa
Cifukwa munikonda.
Sungani moyo wanga Yehova,
Nimakudalilani.
Ine nimakudalilani,
Sungani moyo wanga.
(Onaninso Sal. 28:9; 80:1.)