LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • km 7/13 masa. 5-6
  • Mvetselani ndi Kuphunzila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mvetselani ndi Kuphunzila
  • Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Nkhani Zofanana
  • ‘Sonkhanitsani Anthu’
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2014
Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
km 7/13 masa. 5-6

Mvetselani ndi Kuphunzila

1. N’cifukwa ciani tifunika kucita khama kwambili kuti timvetsele ndi kuphunzila pa msonkhano wa cigawo?

1 Posacedwapa misonkhano ya Cigawo ya 2013 idzayamba. Nchito yaikulu yacitika yokonza pulogalamu imene idzathandiza pa zosoŵa za padziko lonse. Kodi mwakonzekela pasadakhale kuti mukapezekepo masiku onse atatu? Misonkhano ikulu-ikulu ingakhale ndi zoceukitsa zambili, conco tiyenela kucita khama kuti tikhale chelu kwambili kumvetsela mapulogalamu. Popeza zigawo za pamsonkhano zimatenga nthawi yaitali kuposa misonkhano ya mpingo, tiyenela kukhala chelu kwa nthawi yaitali. Kuonjezela apo, kuyenda kuti tifike ku malo a msonkhano komanso zinthu zina zingacititse kuti titope. Kodi n’ciani cidzatithandiza kuti tikhalebe chelu n’colinga cakuti timvetsele ndi kuphunzila?—Deut. 31:12.

2. Kodi tingakonzekeletse bwanji mtima wathu kaamba ka pulogalamu ya msonkhano?

2 Msonkhano Usanayambe: Webu saiti yathu ya www.pr2711.com, imaonetsa pulogalamu ya msonkhano, imeneyi imaphatikizapo mitu ya nkhani zonse komanso lemba limodzi kapena aŵili amene amakhala ndi mfundo yaikulu m’nkhani iliyonse. Ngati tili ndi Intaneti, kuonelatu nkhani zimenezi, kudzatithandiza kuti tikonzekeletse mitima yathu kaamba ka zimene zidzakambidwe. (Ezara 7:10) Pa Kulambila kwanu kwa Pabanja, kodi mungakambitsilane ndi banja lanu pulogalamu ya msonkhano n’colinga cokonzekeletse mitima yao kaamba ka msonkhano?

3. N’ciani cidzatithandiza kuti tizimvetsela mwachelu?

3 Pa Msonkhano: Ngati n’kotheka, mungapitiletu ku cimbudzi pulogalamu isanayambe. Muyenela kuzima foni yanu kuti isakusokonezeni pamene anthu ena akutumilani kapena kukulembelani mameseji kapenanso kuti inuyo musatumile ena mameseji mkati mwa pulogalamu. Ngati simufuna kuzima foni yanu, muyenela kuichela m’njila yakuti isasokoneze ena munthu wina akakutumilani foni. Ngati mugwilitsila nchito kompyuta (tabuleti) mkati mwa pulogalamu, muyenela kuiseŵenzetsa m’njila yakuti isasokoneze ena. Simuyenela kudya mkati mwa mapulogalamu. (Mlal. 3:1) Muziyang’ana wokamba nkhani. Lemba likamaŵelengedwa, inunso muyenela kutsatila m’Baibo yanu. Muyenelanso kulemba manotsi.

4. Kodi makolo angathandize bwanji ana ao kumvetsela ndi kuphunzila?

4 Timafunanso kuti ana athu azimvetsela ndi kuphunzila. Miyambo 29:15 imati: “Mwana womulekelela adzacititsa manyazi mai ake.” Ndiye cifukwa cake, mabanja ayenela kukhala pamodzi kuti makolo aziona ngati ana ao akupanga congo, kulemba mameseji, kapena kuyenda-yenda m’malo momvetsela ku pulogalamu. Ngakhale kuti ndi aang’ono kwambili cakuti sangamvetse zonse zimene zidzakambidwa, ana angaphunzitsidwe kuti azikhala maso komanso asazipanga congo.

5. N’cifukwa ciani kubweleza mfundo za pa msonkhano n’kofunika? Ndipo tingacite bwanji zimenezi?

5 Msonkhano Ukatha Tsiku Lililonse: Muzigona mwamsanga n’colinga cakuti mupume mokwanila. Kubweleza zimene mwamvetsela pa msonkhano kudzakuthandizani kuti muzizikumbukila kwa nthawi yaitali. Conco, ndi bwino banja lonse kukambitsilana zimene mwamvetsela pa msonkhano kwa mphindi zocepa madzulo aliwonse. Komanso mukapita kumalo odyela ndi anzanu, zingakhale bwino ngati mungatenge manotsi anu ndi kukambitsilana nao mfundo imodzi kapena ziŵili zimene zakusangalatsani kwambili. Msonkhano ukatha mukabwelela kunyumba, mungazikambitsilana pa Kulambila kwa Pabanja mmene mungagwilitsile nchito mfundo zimene munaphunzila monga banja. Mungakonzenso zakuti mlungu uliwonse muzibweleza cofalitsa ciliconse catsopano cimene cinatulutsidwa.

6. Kodi kungopezekapo pa msonkhano n’kokwanila? Fotokozani.

6 Phwando lalilkulu la cakudya limakhala laphindu ngati tadya cakudya ndipo cayamba kugwila nchito m’thupi lathu. N’cimodzi-modzi ndi phwando la kuuzimu limene tidzakhala nalo pa msonkhano wa cigawo. Tidzapindula kwambili ngati tapezekapo pa cigawo ciliconse, kumvetsela mwachelu, ndi kugwilitsila nchito zimene tiphunzila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani