Kodi Zimene Zimacitika Padziko N’cifunilo ca Mulungu?
Tikaŵelenga nyuzipepala iliyonse, kapena kuonelela TV, ngakhale kumvetsela wailesi, timamvela nkhani zambili za upandu, nkhondo, ndi zaucigaŵenga. Ganizilani za mavuto a paumoyo wanu. Mwina ndinu wovutika maganizo cifukwa ca wokondedwa wanu amene adwala kapena amene anamwalila. Mwina inunso mukumva mmene munthu wabwino Yobu anamvelela, amene anakamba kuti “ndadzazidwa ndi mavuto.”—Yobu 10:15.
Dzifunseni mafunso awa:
Kodi mavuto amene ine ndi anthu onse timakumana nao n’cifunilo ca Mulungu?
Kodi ndingapeze kuti thandizo pa mavuto anga?
Kodi pali ciyembekezo cakuti tidzakhala ndi mtendele weni-weni padziko lapansi?
Baibo ili ndi mayankho omveka pa mafunso amenewa.
BAIBO IMAPHUNZITSA KUTI MULUNGU ADZACITA IZI PADZIKO LAPANSI.
“Adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4
‘Munthu wolemala adzakwela phili ngati mmene imacitila mbawala yamphongo.’—Yesaya 35:6
“Maso a anthu akhungu adzatsegulidwa.”—Yesaya 35:5
“Onse ali m’manda acikumbutso . . . adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29
“Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24
“Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili.”—Salimo 72:16
ZIMENE BAIBO IMAPHUNZITSA ZINGAKUPINDULITSENI
Musafulumile kuganiza kuti zimene zili pa peji 4 ndi 5 ndi maganizo cabe. Mulungu ndiye analonjeza kuti adzacita zimenezi, ndipo Baibo imatiuza mmene adzazicitila.
Koma Baibo siitiuza zimenezo cabe. Imatiuzanso cisinsi ca mmene tingakhalile ndi umoyo wacimwemwe ndi wokhutilitsa ngakhale panthawi ino. Ganizilani mwakanthawi za nkhawa ndi mavuto anu. Mwina angakhale a zandalama, mavuto a m’banja, kudwala kwa wokondedwa wanu kapena imfa. Baibo ingakuthandizeni pa mavuto anu, ndipo ingakukhazikeni mtima pansi mwa kuyankha mafunso monga awa:
N’cifukwa ciani timavutika?
Kodi tingalimbane bwanji ndi nkhawa za paumoyo?
Kodi tingacite ciani kuti banja lathu likhale lacimwemwe?
N’ciani cimacitika tikafa?
Kodi okondedwa athu amene anafa tidzawaonanso?
Kodi tingatsimikize bwanji kuti Mulungu adzakwanilitsa zimene analonjeza kucita mtsogolo?
Kuŵelenga kwanu buku lino kukuonetsa kuti mufuna kudziŵa zambili zimene Baibo imaphunzitsa. Ndipo buku ili lidzakuthandizani kwambili. Mudzaona kuti mapalagalafu ali ndi mafunso ake pansi pa pejiyo. Pamene a Mboni za Yehova amaphunzila Baibo ndi anthu, amagwilitsila nchito njila ya mafunso ndi mayankho. Anthu ambili aona kuti njila imeneyi ndi yothandiza. Tikhulupilila kuti ngakhale inu mudzaikonda. Tsopano tikufunilani dalitso la Mulungu pamene musangalala kuphunzila zimene Baibo imaphunzitsa m’ceni-ceni.