LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 January tsa. 2
  • Mwai Womanga ndi Wokonza Malo Athu Olambilila

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mwai Womanga ndi Wokonza Malo Athu Olambilila
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • TINGATHANDIZE PA NCHITOYI MWA . . .
  • Awa Ndi Malo Athu Olambilila
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Malo Olambilila
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Nchito Yomanga Imene Imalemekeza Yehova
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Tingacite Ciani Kuti Tisamalile Nyumba Yathu ya Ufumu?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 January tsa. 2

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Mwai Womanga ndi Wokonza Malo Athu Olambilila

Kuti kacisi wa Yehova amangidwe, panafunikila nchito yaikulu komanso ndalama zambili. Komabe, Aisiraeli anacilikiza nchitoyo mwacangu. (1 Mbiri 29:2-9; 2 Mbiri 6:7, 8) Mmene Aisiraeli anali kusamalila kacisiyo pambuyo pakuti amaliza kumanga, zinali kuonetsa kuti anali kukonda Mulungu kapena ai. (2 Maf. 22:3-6; 2 Mbiri 28:24; 29:3) Masiku ano, Akristu amagwilitsila nchito nthawi yao ndi mphamvu zao pomanga, kuyeletsa, ndi kukonza Nyumba za Ufumu ndiponso Mabwalo a Msonkhano. Kunena zoona, kugwila nchito ndi Yehova mwa njila imeneyi ndi mwai wapadela kwambili, ndipo ndi mbali ya utumiki wathu wopatulika.—Sal. 127:1; Chiv. 7:15.

TINGATHANDIZE PA NCHITOYI MWA . . .

  • Kukonza malo okhala m’Nyumba ya Ufumu

    Kuyeletsa pambuyo pa misonkhano. Ngati simungathe kutelo, mungatole zinyalala zimene zili pafupi ndi pamene mwakhala.

  • Kuyeletsa Nyumba ya Ufumu

    Kugwila nao nchito yoyeletsa ndi kukonza Nyumba ya Ufumu. Pakaculuka ogwila nchito, nchitoyo imasangalatsa ndiponso imapepuka.—lv tsa. 92-93 ndime 18.

  • Kupanga copeleka m’bokosi la zopeleka

    Kupanga zopeleka za ndalama. Ngakhale titapeleka “timakobidi tiŵili tating’ono,” Yehova amayamikila.—Maliko 12:41-44.

  • Kukonza malo olambililamo

    Kudzipeleka pa nchito yomanga ndi kukonza nyumba zolambililamo ngati mungathe kutelo. Simufunikila luso lapadela kuti mugwile nao nchito imeneyi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani