Khalani Maso! Satana Akufuna Kukumezani
“Khalani maso. Mdani wanu Mdyelekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.”—1 PET. 5:8.
1. Fotokozani zimene zinacitika kuti mngelo wina akhale Satana.
POYAMBA Satana anali mngelo wabwino wa Yehova. Koma patapita nthawi anayamba kulakalaka kuti anthu azimulambila. M’malo mothetsa cilakolako coipaco, iye anacilekelela mpaka cinakula ndi kubala chimo. (Yak. 1:14, 15) Satana “sanakhazikike m’coonadi,” koma anapandukila Yehova ndi kukhala “tate wake wa bodza.”—Yoh. 8:44.
2, 3. Kodi maina akuti “Satana,” “Mdyelekezi,” “njoka” ndi “cinjoka” amatiuzanji za mdani wamkulu wa Yehova?
2 Kuyambila pamene anapanduka, Satana wakhala mdani wamkulu wa Yehova ndi anthu. Maina amene Satana anapatsidwa amaonetsa kuti iye ndi woipa kwambili. Dzina lakuti Satana limatanthauza “Wotsutsa,” kuonetsa kuti mngelo woipayu sacilikiza ulamulilo wa Mulungu koma amadana nawo ndi kulimbana nawo mwamphamvu. Ndipo Satana amafunitsitsa kuti ulamulilo wa Yehova uthe.
3 Pa Chivumbulutso 12:9, Satana amachedwa Mdyelekezi, kutanthauza “Woneneza.” Dzinali limatikumbutsa kuti Satana anaipitsa dzina la Yehova mwa kunena kuti iye ndi wabodza. Dzina lakuti “njoka yakale ija” limatikumbutsa zimene zinacitika mu Edeni pamene Satana ananyenga Hava mwa kugwilitsila nchito njoka. Dzina lakuti “cinjoka” limatipangitsa kuganiza za cilombo coopsa, ndipo ndi loyenelela Satana cifukwa amafunitsitsa kulepheletsa colinga ca Yehova ndi kuononga anthu Ake.
4. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?
4 N’zoonekelatu kuti Satana amafunitsitsa kutilepheletsa kukhala okhulupilika kwa Mulungu. Ndiye cifukwa cake Baibulo limatilangiza kuti: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyelekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Pet. 5:8) Motelo, m’nkhani ino tikambilana makhalidwe atatu a Satana amene akuonetsa kuti tifunika kusamala ndi mdani woopsa ameneyu wa Yehova ndi anthu Ake.
SATANA NDI WAMPHAMVU
5, 6. (a) Pelekani zitsanzo zoonetsa kuti angelo ndi “amphamvu.” (b) N’cifukwa ciani tinganene kuti Satana ali ndi “njila yobweletsela imfa”?
5 Angelo ndi zolengedwa zauzimu ‘zamphamvu.’ (Sal. 103:20) Angelo ndi apamwamba kwambili kuposa anthu ndipo ali ndi nzelu ndi mphamvu zoculuka. Ngakhale ndi conco, angelo okhulupilika amagwilitsila nchito mphamvu zao pocita zinthu zabwino. Mwacitsanzo, nthawi ina mngelo wa Yehova anapha asilikali 185,000 a Asuri. Munthu mmodzi sangakwanitse kucita zotelo, ndipo si copepuka kuti gulu la asilikali licite zimenezi. (2 Maf. 19:35) Nthawi inanso, mngelo anagwilitsila nchito mphamvu ndi nzelu zake kutulutsa atumwi a Yesu m’ndende. Mngeloyo anadutsa pa malo acitetezo, anatsegula zitseko, kenako anatulutsa atumwiwo ndi kutsekanso zitsekozo. Iye anacita zimenezi ngakhale kuti alonda anali pomwepo.—Mac. 5:18-23.
6 Monga taonela, angelo abwino amagwilitsila nchito moyenela mphamvu zao. Koma Satana amagwilitsila nchito mphamvu zake molakwika. Ndipo iye ali ndi mphamvu zambili. Malemba amamucha “wolamulila wa dzikoli” ndi “mulungu wa nthawi ino.” (Yoh. 12:31; 2 Akor. 4:4) Satana Mdyelekezi alinso ndi “njila yobweletsela imfa.” (Aheb. 2:14) Sikuti iye amapha anthu mwacindunji. Komabe, amacititsa anthu ambili m’dzikoli kukhala ndi mtima woipa ngati wake. Komanso cifukwa cakuti Hava anamvela bodza la Satana, ndipo Adamu sanamvele Mulungu, ucimo ndi imfa zinafalikila kwa anthu onse. (Aroma 5:12) Mwa njila imeneyi, Mdyelekezi anakhala ndi “njila yobweletsela imfa.” Satana ndi “wopha anthu,” monga mmene Yesu anakambila. (Yoh. 8:44) Satana ndi mdani wathu wamphamvu kwambili.
7. Kodi ziwanda zaonetsa bwanji kuti ndi zamphamvu?
7 Tikamatsutsa Satana timakhala adani ake, ndiponso adani a onse amene ali kumbali yake pa nkhani ya ulamulilo wa cilengedwe conse. Adani athu akuphatikizapo angelo oipa kapena kuti ziwanda. (Chiv. 12:3, 4) Nthawi ndi nthawi, ziwanda zaonetsa kuti ndi zamphamvu mwa kuvutitsa kwambili anthu amene zawagwila. (Mat. 8:28-32; Maliko 5:1-5) Sitiyenela kudelela mphamvu za ziwanda kapena za “wolamulila ziwanda.” (Mat. 9:34) Popanda thandizo la Yehova, sitingapambane pa nkhondo yathu yolimbana ndi Satana.
SATANA NDI WANKHANZA
8. (a) Kodi colinga ca Satana n’ciani? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Malinga ndi mmene inuyo mwaonela, n’ciani cionetsa kuti anthu ali ndi mtima wankhanza ngati Satana?
8 Mtumwi Petulo anayelekezela Satana ndi “mkango wobangula.” Malinga ndi buku lina, liu la Cigiriki lomasulilidwa kuti ‘kubangula’ limanena za “kulila kwa cilombo ca njala kwambili.” Mau amenewa amafotokoza bwino mtima woipa umene Satana ali nao. Ngakhale kuti dziko lonse lili kale m’manja mwake, Satana akufunabe kugwila anthu ena. (1 Yoh. 5:19) Kwa iye, anthu a m’dzikoli ali ngati “kadyonkho” cabe. Koma amafunitsitsa kugwila otsalila odzozedwa ndi anzao a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16; Chiv. 12:17) Colinga cake ndi kumeza anthu a Yehova. Kuyambila m’nthawi ya atumwi, Satana wakhala akusonkhezela anthu kuzunza kwambili otsatila a Yesu, ndipo zimenezi ndi umboni wakuti iye ndi wankhanza.
9, 10. (a) Kodi Satana anayesa bwanji kulepheletsa colinga ca Mulungu cokhudza mtundu wa Aisiraeli? (Pelekani zitsanzo.) (b) N’cifukwa ciani Satana anali kuukila Aisiraeli kaŵilikaŵili? (c) Kodi muganiza kuti Mdyelekezi amamva bwanji mtumiki wa Yehova akacita chimo lalikulu?
9 Pamene Satana akuyesa kulepheletsa colinga ca Mulungu, amacitanso zinthu zina zoonetsa kuti ndi wankhanza. Mkango wanjala sucita cifundo ukafuna kugwila nyama, kapena pambuyo pogwila nyamayo. Nayenso Satana sacita cifundo ndi anthu amene amafuna kuwagwila. Mwacitsanzo, nthawi zambili Satana Mdyelekezi anali kusonkhezela Aisiraeli kucita macimo monga dyela ndiponso ciwelewele. Tikamaŵelenga Baibulo timamva za mavuto amene Zimiri anakumana nao cifukwa ca ciwelewele, ndiponso amene Gehazi anakumana nao cifukwa ca dyela. Mwacionekele, pamene zimenezi zinali kucitika, Satana anali kusangalala kwambili.—Num. 25:6-8, 14, 15; 2 Maf. 5:20-27.
Satana amasangalala mtumiki wa Yehova akacita chimo (Onani ndime 10)
10 Satana anali kuukila mtundu wa Aisiraeli pa cifukwa cina capadela. Mtunduwo unali kudzatulutsa Mesiya, amene adzaphwanya Satana ndi kutsimikizila kuti Yehova ndiye woyenela kulamulila. (Gen. 3:15) Satana sanafune kuti Aisiraeli azilambila Mulungu, ndipo kaŵilikaŵili anali kuwasonkhezela kucita macimo. N’zoonekelatu kuti Satana sanamve cisoni pamene Davide anacita cigololo kapena pamene mneneli Mose analephela kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Iye amasangalala mtumiki wa Mulungu akacita chimo lalikulu. Ndiponso zinthu zikatelo, Mdyelekezi amayamba kutonza Yehova.—Miy. 27:11.
11. Kodi Satana ayenela kuti anali ndi colinga cotani pamene anali kuyesa Sara?
11 Satana anali kudana kwambili ndi anthu a mu mzele wobadwila wa Mesiya. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika Abulahamu atangouzidwa kuti adzakhala “mtundu waukulu.” (Gen. 12:1-3) Pamene Abulahamu ndi Sara anali ku Iguputo, Farao anatenga Sara ndi kupita naye kunyumba kwake kuti akhale mkazi wake. Koma Yehova anacitapo kanthu mwa kuteteza Sara kuti asaipitsidwe. (Ŵelengani Genesis 12:14-20.) Isaki atatsala pang’ono kubadwa, zofanana ndi zimenezi zinacitikanso ku Gerari. (Gen. 20:1-7) Kodi Satana ndiye anacititsa zimenezo? Kodi iye anaganiza kuti Sara, amene anacoka mumzinda wolemela wa Uri ndi kukakhala m’mahema, angakopeke ndi nyumba zokongola za Farao ndi Abimeleki? Kodi Satana anaganiza kuti Sara angacitile cinyengo mwamuna wake ndi Yehova ndi kulowa m’cikwati cacigololo? Baibulo silikamba, koma tidziŵa kuti Mdyelekezi anali kufuna kuipitsa Sara kuti akhale wosayenelela kubeleka mwana amene Yehova analonjeza. Satana sakanamva cisoni ngati Sara akanaononga banja lake, mbili yake, ndiponso ubwenzi wake ndi Yehova. Satana alibedi cifundo ngakhale pang’ono.
12, 13. (a) Kodi Satana anaonetsa bwanji kuti ndi wankhanza Yesu atabadwa? (b) Kodi muganiza kuti Satana amamva bwanji akaona acicepele amene amakonda Yehova ndi kum’tumikila?
12 Yesu anabadwa patapita zaka zambili kucokela pamene Abulahamu anafa. Satana sanaganize kuti khandalo linali lokongola, losangalatsa ndiponso lamtengo wapatali. Iye anadziŵa kuti khandalo likadzakula lidzakhala Mesiya wolonjezedwa. Inde, Yesu ndi mbali yoyamba ya mbeu ya Abulahamu, amene ‘adzaononga nchito za Mdyelekezi.’ (1 Yoh. 3:8) Kodi Satana anaganizilapo zoti kupha khanda ndi kucita zinthu mopitilila malile? Iyai. Iye alibe makhalidwe abwino. Ndipo sanacedwe kukonzela ciwembu Yesu pamene anali mwana. Kodi anakonza ciwembu cotani?
13 Mfumu Herode inakwiya kwambili pamene openda nyenyezi anaifunsa za ‘mfumu ya Ayuda imene inabadwa,’ ndipo inakonza zakuti iphe khandalo. (Mat. 2:1-3, 13) Pofuna kuonetsetsa kuti khandalo laphedwa ndithu, iye analamula anthu kukapha ana onse aamuna m’Betelehemu ndi m’zigawo zake, kuyambila azaka ziŵili kutsika m’munsi. (Ŵelengani Mateyu 2:13-18.) Yesu anapulumuka pa cocitika coopsaco. Koma kodi izi zikusonyeza ciani ponena za mdani wathu Satana? Zikusonyeza kuti Mdyelekezi salemekeza moyo wa munthu. Ndipo alibenso cifundo ndi ana. Ndithudi, Satana ndi “mkango wobangula.” Iye ndi wankhanza kwambili.
SATANA NDI WACINYENGO
14, 15. Kodi Satana wacititsa bwanji “khungu maganizo a anthu osakhulupilila”?
14 Popeza kuti Satana ndi wacinyengo, iye amanyengelela anthu kuti apandukile Yehova, Mulungu wacikondi. (1 Yoh. 4:8) Mwa kugwilitsila nchito cinyengo, Satana amalepheletsa anthu ‘kuzindikila zosowa zao zauzimu.’ (Mat. 5:3) Motelo, iye “wacititsa khungu maganizo a anthu osakhulupilila, kuti asaone kuwala kwa uthenga wabwino waulemelelo wonena za Kristu, yemwe ali cifanizilo ca Mulungu.”—2 Akor. 4:4.
15 Njila imodzi yaikulu imene Satana amanyengela anthu ndi kupitila m’cipembedzo conama. Iye ayenela kuti amakondwela kwambili akaona anthu akulambila makolo ao, cilengedwe, nyama kapena zinthu zina osati Yehova, amene ‘amafuna kuti anthu azidzipeleka kwa iye yekha.’ (Eks. 20:5) Ngakhale anthu amene amaganiza kuti amalambila Mulungu m’njila yoyenela ndi akapolo a zikhulupililo zonama ndi miyambo yacabecabe. Iwo amamvetsa cisoni kwambili ngati anthu amene Yehova anawauza kuti: “N’cifukwa ciani anthu inu mukuwononga ndalama polipilila zinthu zimene si cakudya, ndipo n’cifukwa ciyani mukuvutika kugwilila nchito zinthu zimene sizikhutitsa? Tchelani khutu kwa ine kuti mudye zabwino, ndiponso kuti moyo wanu usangalale kwambili ndi zakudya zamafuta.”—Yes. 55:2.
16, 17. (a) N’cifukwa ciani Yesu anauza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana”? (b) Kodi Satana angatinyenge bwanji kuti tigone mwa kuuzimu?
16 Satana anganyenge ngakhale atumiki okhulupilika a Yehova. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika pamene Yesu anauza atumwi ake kuti anali pafupi kuphedwa. Mtumwi Petulo anatengela Yesu pambali ndi kumuuza kuti: “Dzikomeleni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikucitikileni ngakhale pang’ono.” Petulo ayenela kuti anali ndi maganizo abwino ndithu ponena zimenezi. Koma Yesu anamuyankha mwamphamvu kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana!” (Mat. 16:22, 23) N’cifukwa ciani Yesu anachula Petulo kuti “Satana”? Cifukwa cakuti Yesu anadziŵa zimene zinali pafupi kucitika. Iye anali atatsala pang’ono kufa monga nsembe ndi kusonyeza kuti Mdyelekezi ndi wabodza. Panthawi yovutayi, Yesu sanafunike ‘kudzikomela mtima.’ Koma Satana anali kufuna kuti iye acite zimenezo.
17 Pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, ifenso tikukhala m’nthawi yovuta. Satana amafuna kuti ‘tidzikomele mtima’ mwa kudzifunila umoyo wa wofuwofu m’dzikoli n’colinga cakuti tigone mwa kuuzimu. Koma musalole kuti Satana akunyengeleleni mwa njila imeneyi. M’malomwake, “khalanibe maso.” (Mat. 24:42) Musakhulupilile bodza la Satana lakuti mapeto ali kutali kapena kuti sadzabwela.
18, 19. (a) Kodi Satana amafuna kuti tizidziona bwanji? (b) Kodi Yehova amatithandiza bwanji kukhalabe maso ndi oganiza bwino?
18 Satana amayesanso kutinyenga mwa njila ina. Iye amafuna kuti tizikhulupilila kuti Mulungu satikonda ndi kuti sangatikhululukile macimo athu. Onsewa ndi mabodza a Satana. Kunena zoona, ndani makamaka amene sakondedwa ndi Yehova? Ndi Satana. Nanga ndani makamaka amene sangakhululukidwe ndi Mulungu? Inde, ndi Satana yemweyo. Komabe, Baibulo limatitsimikizila kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikila oyela ndipo mukupitiliza kuwatumikila.” (Aheb. 6:10) Yehova amayamikila zimene timacita kuti timukondweletse, ndipo utumiki wathu sudzapita pacabe. (Ŵelengani 1 Akorinto 15:58.) Conco, tisanyengedwe ndi mabodza a Satana.
19 Monga taonela, Satana ndi wamphamvu, wankhanza, ndi wacinyengo. Nanga tingacite ciani kuti tipambane polimbana ndi mdani wathu woopsa ameneyu? Yehova amatiteteza. Mau ake amatiuza za macenjela a Satana, ndipo “tikudziŵa bwino ziwembu zake.” (2 Akor. 2:11) Tikadziŵa bwino njila zacinyengo za Satana, sicikhala covuta kukhalabe maso ndi oganiza bwino. Koma kudziŵa cabe ziwembu za Satana si kokwanila. Baibulo limati: “Tsutsani Mdyelekezi ndipo adzakuthawani.” (Yak. 4:7) M’nkhani yotsatila tidzakambilana makhalidwe atatu amene tifunika kupewa kuti tipambane polimbana ndi Satana.