LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr18 February masa. 1-4
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
  • Tumitu
  • FEBRUARY 5-11
  • FEBRUARY 19-25
  • FEBRUARY 26–MARCH 4
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
mwbr18 February masa. 1-4

Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

FEBRUARY 5-11

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 12-13

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 12:20

Nyale Yofuka: Kale, nyale imene anthu ambili anali kuseŵenzetsa inali nsupa, imene anali kuthilamo mafuta a maolivi. Inali kuyaka cifukwa mafuta anali kukwela ku thambo yake. Mu Cigiriki, mau akuti “nyale yofuka” angatanthauze nthambo ya nyale yofuka utsi cifukwa cakuti moto ukaliko koma lawi lake likuzima kapena lazimilatu. Ulosi wa pa Yesaya 42:3 unakambilatu za cifundo ca Yesu kuti, sadzazimitsa ciyembekezo ca anthu odzicepetsa ndi opondelezedwa.

FEBRUARY 12-18

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 14-15

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 14:21

osaŵelengela akazi ndi ana aang’ono: Ni Mateyu cabe amene anachula za akazi ndi ana pokamba za cozizwitsa cimeneci. N’kutheka kuti ciŵelengelo ca anthu amene anadyetsedwa mozizwitsa cinaposa pa 15,000.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 15:7

onyenga: Liu la Cigiriki lakuti hy·po·kri·tesʹ poyamba linali kukamba za Agiriki (ndipo kenako za Aroma) ocita maseŵelo, amene anali kuvala vophimba nkhope vikulu-vikulu kuti vizikuza mau. Anali kuseŵenzetsa liuli mophiphilitsa pofuna kukamba za munthu wobisa zolinga zake kapena umunthu wake. Apa Yesu anachula atsogoleli a Ciyuda kuti “onyenga.”—Mat. 6:5, 16.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 15:26

ana . . . tiagalu: Popeza kuti agalu anali odetsedwa malinga na Cilamulo ca Mose, nthawi zambili Malemba amaseŵenzetsa liu lakuti agalu m’lingalilo lonyoza. (Lev. 11:27; Mat. 7:6; Afil. 3:2; Chiv. 22:15) Komabe, m’mabuku onse aŵili, Maliko (7:27) na Mateyu, Yesu pokamba, anaseŵenzetsa liu locepetsa lotanthauza “tiagalu” kapena “galu wa m’nyumba,” pofuna kuti mauwo asamveke onyoza. Cioneka kuti mwina Yesu anali kukamba mau oonetsa cikondi pa ziŵeto za m’nyumba zimene anthu osakhala Ayuda anali kusunga. Conco, Yesu poyelekezela Aisiraeli ndi “ana,” ndiponso anthu osakhala Ayuda ndi “tiagalu,” mwacionekele anali kufuna kuonetsa cimene cinali cofunika kwambili. Ngati panyumba panali ana ndi tiagalu, ana ndiwo anali oyambilila kupatsiwa cakudya.

FEBRUARY 19-25

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 16-17

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 16:18

Iwe ndiwe Petulo, ndipo pathanthwe ili: Liu la Cigiriki lakuti peʹtros, litanthauza “cidutswa ca thanthwe; mwala.” Pano liuli laseŵenzetsedwa monga dzina leni-leni (Petulo), dzina la Cigiriki limene Yesu anapatsa Simoni. (Yoh. 1:42) Liu lina lofanana nalo ni peʹtra, kutanthauza “thanthwe.” Liu limeneli lingatanthauzenso thanthwe lapansi, kapena cimwala cacikulu. Liu la Cigiriki limeneli lipezekanso pa Mat. 7:24, 25; 27:60; Luka 6:48; 8:6; Aroma 9:33; 1 Akor. 10:4; 1 Pet. 2:8. N’zoonekelatu kuti Petulo sanadzione kuti ndiye mwala umene Yesu anali kudzamangapo mpingo wake, cifukwa pa 1 Petulo 2:4-8, iye analemba kuti Yesu ndiye anali mwala wokambidwilatu “wapakona pa maziko,” wosankhiwa na Mulungu. Mofananamo, nayenso mtumwi Paulo anakamba kuti Yesu ndiye anali “maziko” komanso ‘thanthwe lauzimu.’ (1 Akor. 3:11; 10:4) Conco, Yesu mwacionekele anaseŵenzetsa mau okuluŵika pofuna kukamba kuti: ‘Iwe amene ndikucha Petulo, Cidutswa ca Thanthwe, wazindikila Khristu weni-weni, amene ndi “thanthwe ili,” amenenso adzakhala maziko a mpingo wacikhristu.’

mpingo: Apa m’pamene liu la Cigiriki lakuti ek·kle·siʹa liyambila kuonekela. Linacokela ku mau aŵili a Cigiriki, ek, kutanthauza “ku,” ka·leʹo kutanthauza “itana.” Liu limeneli lakuti ek·kle·siʹa, limatanthauza gulu la anthu oitanidwa kapena osonkhanitsidwa pamodzi pa colinga cinacake kapena pa cocitika cinacake. (Onani Glossary.) Mu vesi iyi, Yesu anakambilatu za kukhazikitsidwa kwa mpingo wacikhristu, wopangidwa na Akhristu odzozedwa, amene monga “miyala yamoyo,” akumangidwa “n’kukhala nyumba yauzimu.” (1 Pet. 2:4, 5) Liu la Cigiriki limeneli linaseŵenzetsewa kwambili mu Baibo ya Septuagint, ndipo liuli likamasulidwa ndendende mu Ciheberi limatanthauza “mpingo.” Nthawi zambili, limatanthauza mtundu wonse wa anthu a Mulungu. (Deut. 23:3; 31:30) Pa Mac. 7:38, Aisiraeli amene anaitaniwa kucoka ku Iguputo, anachulidwa kuti ni “mpingo.” Mofananamo, Akhristu amene ‘akuitanidwa kucoka mu mdima’ na ‘kusankhidwa kucokela m’dziko,’ amapanga “mpingo wa Mulungu.”—1 Pet. 2:9; Yoh. 15:19; 1 Akor. 1:2.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 16:19

makiyi a Ufumu wakumwamba: M’Baibo anthu amene anali kupatsiwa makiyi, kaya akhale makiyi eni-eni kapena ophiphilitsa, anali kupatsiwa ulamulilo winawake. (1 Mbiri 9:26, 27; Yes. 22:20-22) Conco, mau akuti “kiyi” anayamba kuimila ulamulilo na udindo. Petulo anaseŵenzetsa “makiyi” amene anapatsiwa kutsegulila Ayuda (Mac. 2:22-41), Asamariya (Mac. 8:14-17), ndi anthu amitundu ina mwayi wolandila mzimu wa Mulungu kuti akaloŵe mu Ufumu wa kumwamba.

FEBRUARY 26–MARCH 4

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 18-19

“Muzisamala Kuti Musadzipunthwitse Kapena Kupunthwitsa Ena”

nwtsty mfundo zounikila pa Mat. 18:6, 7

cimwala ca mphelo . . . cimene bulu amayendetsa: Kapena kuti “cimwala cacikulu ca mphelo.” Mau ake eni-eni ni “cimwala ca mphelo ca bulu.” Zioneka kuti cimwala caconco, cinali mamita 1.2 mpaka 1.5 m’cimimba mwake. Cinali colema ngako cakuti cinali kufunika kuyendetsedwa na bulu.

zopunthwitsa: Tanthauzo leni-leni la liu la Cigiriki lakuti skanʹda·lon, lomasulidwa kuti “zopunthwitsa,” liganizilidwa kuti litanthauza msampha. Ena amakamba kuti kanali kamtengo kamene anali kuikako cakudya pofuna kukola cinacake. Koma m’kupita kwa nthawi, linayamba kutanthauza cinthu cimene cingapangitse wina kupunthwa kapena kugwa. M’mau ophiphilitsa, liuli limatanthauza zocita kapena mikhalidwe imene ingacititse munthu kutsatila njila yolakwika, kupunthwa kapena kugwa m’makhalidwe, kapena kugwela m’chimo. Pa Mat. 18:8, 9, liu lofananako lakuti skan·da·liʹzo, limene linamasulidwa kuti “kupunthwitsa,” lingatanthauzenso “kukhala msampha kapena kucititsa kucimwa.”

nwtsty zithunzi

Cimwala ca mphelo

Miyala ya mphelo anali kuiseŵenzetsa popela mbewu na posikinya mafuta a maolivi. Miyala ina inali ing’ono-ing’ono cakuti anali kuiyendetsa na manja. Koma ina inali ikulu-ikulu cakuti anali kufunika kuiyendetsa na nyama. Miyala yaconco iyenela kuti inali kulingana na cimwala cimene Afilisiti anauza Samisoni kuti aziciyendetsa. (Ower. 16:21) Mphelo zoyendetsedwa na nyama zinali zofala ku Isiraeli na m’madela ambili mu Ufumu wa Roma.

Mwala wa Mphelo wa Pamwamba na wa Pansi

Mwala waukulu wa mphelo monga umene waonetsedwa pano, unali kuyendetsedwa na nyama zoŵeta monga bulu, ndipo anali kuuseŵenzetsa popela mbewu kapena kusikinya maolivi. Mwala wa mphelo wapamwamba ungakhale waukulu mamita 1.5 m’cimimba mwake, ndipo ungayendetsedwe pa cimwala capansi cokulilapo.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 18:9

Gehena: Liu limeneli linacokela ku liu la Ciheberi lakuti geh hin·nomʹ, kutanthauza “cigwa ca Hinomu,” cimene cinali kumadzulo na kum’mwela kwa Yerusalemu wakale. (Onani (sgd) Gawo 16, mapu “Yerusalemu ndi Malo Oyandikila.”) Pofika m’nthawi ya Yesu, cigwaco cinakhala dzala lotenthelako zinyalala. Conco, liu lakuti “Gehena” linali lophiphilitsa kutanthauza ciwonongeko cothelatu.

nwtstg

Gehena

Ni dzina la Cigiriki la Cigwa ca Hinomu, cimene cinali kum’mwela cakumadzulo kwa Yerusalemu wakale. (Yer. 7:31) Ulosi unakambilatu kuti cigwaci cidzakhala malo otailako mitembo ya anthu. (Yer. 7:32; 19:6) Palibe umboni woonetsa kuti nyama kapena anthu anali kuponyedwa ku Gehena kuti atenthedwe amoyo kapena kuti azunzidwe. Conco, malo amenewa saimila malo osaoneka kumene mizimu ya anthu imazunzidwilako kosatha m’moto weni-weni. M’malomwake, Yesu na ophunzila ake anaseŵenzetsa liu lakuti Gehena, pofuna kutanthauza cilango cosatha ca “imfa yaciŵili,” cimene ni kuwonongedwa kwamuyaya, kapena kuti kufafanizidwa kothelatu.—Chiv. 20:14; Mat. 5:22; 10:28.

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 18:10

amaona nkhope ya Atate wanga: Kapena kuti “kuonekela kwa atate wanga.” Popeza kuti angelo ali na mwayi woonekela kwa Mulungu, ndiwo okha amene angathe kuona nkhope ya Mulungu.—Eks. 33:20.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 18:22

nthawi 77: Mau ake eni-eni ni 70 kuwilikiza ka 7. Mau a Cigiriki amenewa angatanthauze “70 + 7” ( nthawi 77) kapena “70 × 7” (nthawi 490). Mau amodzi-modzi opezeka mu Baibo ya Septuagint pa Gen. 4:24, mu Ciheberi ni “nthawi 77,” imene ikugwilizana ndi “nthawi 77,” zochulidwa mu Baibulo la Dziko Latsopano. Mosasamala kanthu za mmene munthu angamvetsetsele, namba ya 7 ikabwelezedwa, imatanthauza “mpaka kalekale” kapena kuti “palibe malile.” Yesu anasintha nthawi 7 zimene Petulo anakamba, n’kukhala nthawi 77. Iye anacita izi pofuna kuuza otsatila ake kuti sayenela kuika malile pa nkhani yokhululukila munthu. Mosiyana na izi, Talmud ya Ababulo (Yoma 86b) imati: “Ngati munthu wacita colakwa, nthaŵi yoyamba, yaciŵili ndiponso nthaŵi yacitatu iye akhululukidwa, nthaŵi yacinayi sakhululukidwa.”

nwtsty mfundo younikila pa Mat. 19:7

kalata yothetsa ukwati: Kapena kuti “kalata ya cisudzulo.” Cilamulo cinali kufuna kuti mwamuna amene anali kuganizila zosudzula mkazi wake, azilemba kalata yovomelezeka mwalamulo na kufunsila kwa akulu. Izi zinali kumupatsa mpata woganizilapo mozama pa cosankha cacikulu cimeneco. Colinga ca Cilamulo cinali kuteteza anthu kuti asamasudzulane mwacisawawa ndi kuti akazi azikhala otetezeka. (Deut. 24:1) Koma atsogoleli acipembedzo a m’nthawi ya Yesu, anali kupangitsa kuti kusudzulana kuzikhala kosavuta. Josephus, Mfarisi wolemba mbili wakale, amenenso cikwati cake cinatha, anakamba kuti kuthetsa cikwati kunali kololeka “pa cifukwa ciliconse (ndipo amuna ambili amakamba kuti ali na zifukwa zambili zothetsela vikwati vawo).”

nwtsty zithunzi

Kalata ya Cisudzulo

Kalata iyi ya cisudzulo inalembewa ca m’ma 71 kapena 72 C.E., ndipo inalembewa m’Cialamu. Inapezeka kumpoto kwa mtsinje wouma wa Wadi Murabbaat, m’Cipululu ca Yudeya. Kalatayi ikamba kuti m’caka ca 6, pamene Ayuda anali kuukila boma, Joseph mwana wa Naqsan, anasudzula Miriam, mwana wa Jonathan amene anali kukhala mu mzinda wa Masada.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani