NYIMBO 78
Phunzitsani Mau a Mulungu
Yopulinta
1. Timakonda kuphunzitsa
Anthu za Yehova.
Madalitso timapeza
Ni osaneneka.
Tiphunzitse mwa cikondi
Monga Yesu Khristu
Kuti anthu onse
Ayandikile kwa Yehova.
2. Tiziyesetsa mwakhama
Kucita zabwino,
Kuti onse otiona
Amvele uthenga.
Zimene taphunzitsidwa
Tiphunzitse ena.
Tidzakhala acimwemwe
Tikaphunzitsa ena.
3. M’lungu adzatithandiza
Pophunzitsa anthu.
Tikapemphela kwa iye,
Adzatithandiza.
Tikonde onse amene
Tiphunzila nawo.
Posacedwa nawonso
Adzapita patsogolo.
(Onaninso Sal. 119:97; 2 Tim. 4:2; Tito 2:7; 1 Yoh. 5:14.)