NYIMBO 86
Tifunika Kuphunzitsidwa
Yopulinta
(Yesaya 50:4; 54:13)
1. Mosangalala bwelani mulandile,
Malangizo a Yehova M’lungu.
Onse anjala ya coonadi,
Mulungu wathu adzaŵadyetsa.
2. Tipitilize kusonkhana pamodzi,
Kuti ’se tidziŵe zolungama.
Mwa ‘bale athu, mzimu wa M’lungu
Umatiyendetsa m’coonadi.
3. Mau otamanda Atate Yehova
Ni abwino, ni otsitsimula.
Tizipezeka ku misonkhano
Ndipo Yehova ‘dzatidalitsa.
(Onaninso Aheb. 10:24, 25; Chiv. 22:17.)